LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
Tulukani
Loŵani
LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Takulandilani
Ici ni cida cofufuzila m'mabuku olembewa na Mboni za Yehova mu vitundu volekana-lekana.
Ngati mufuna kucita daunilodi, yendani pa jw.org.
  • Lelo

Cisanu, October 3

Musamaganizile zofuna zanu zokha, koma muziganizilanso zofuna za ena.​—Afil. 2:4.

Mouzilidwa na mzimu woyela, mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu kuti aziganizila zofuna za ena. Kodi tingatsatile motani uphungu umenewu pa misonkhano? Mwa kukumbukila kuti nawonso abale na alongo athu amafuna kupelekapo ndemanga. Ganizilani izi. Mukamaceza na mabwenzi anu, kodi mungamalankhule kwambili moti anzanuwo n’kusoŵa mpata wakuti alankhulepo? Ayi simungatelo. Mumafuna kuti nawonso azilankhulapo. Mofananamo, pamisonkhano tiyenela kusiyilako ena mpata wopelekapo ndemanga. Ndipo njila yabwino koposa yolimbikitsila abale na alongo athu, ni kuwapatsa mpata woonetsa cikhulupililo cawo. (1 Akor. 10:24) Ndemanga zathu zizikhala zazifupi, kuti ena azikhalanso na mpata wopelekapo ndemanga. Ngakhale popeleka ndemanga yaifupi, pewani kukamba mfundo zambili. Musacite kukombelatu mfundo zonse m’ndime, moti ena n’kusoŵa ndemanga yopelekapo. w23.04 22-23 ¶11-13

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025

Ciŵelu, October 4

Ndimacita zinthu zonse cifukwa ca uthenga wabwino, kuti ndilalikile uthengawu kwa anthu ena.​—1 Akor. 9:23.

Zinthu zikasintha pa umoyo wathu, kuthandizabe ena n’kofunika kwambili, maka-maka mwa kulalikila. Tizikhala ololela pa utumiki wathu. Timakumana na anthu a zikhulupililo na maganizo osiyana-siyana, komanso ocokela kosiyana-siyana. Mtumwi Paulo anali wololela, ndipo tingatengeleko citsanzo cake. Yesu anaika Paulo kukhala ‘mtumwi wotumidwa kwa mitundu ina.’ (Aroma 11:13) Pa utumiki wake umenewo, Paulo analalikila kwa Ayuda, Agiriki, anthu ophunzila, alimi osauka, anyanchito a boma, komanso mafumu. Kuti awafike pa mtima anthu onsewo, Paulo ‘anakhala zinthu zonse kwa anthu osiyanasiyana.’ (1 Akor. 9:19-22) Poganizila cikhalidwe na zikhulupililo za anthu amene anali kuwalalikila, mtumwi Paulo anasintha njila yolalikila. Nafenso tingakhale alaliki ogwila mtima tikamakhala okonzeka kusintha ulaliki wathu kuti ugwilizane na munthu amene tapeza. w23.07 23 ¶11-12

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025

Sondo, October 5

Kapolo wa Ambuye sayenela kukangana ndi anthu. Koma ayenela kukhala wodekha kwa onse.​—2 Tim. 2:24.

Munthu akakhala wofatsa sindiye kuti ni wofooka. Zimafuna mphamvu kuti munthu akhalebe wodekha akaputidwa. Kufatsa ni ‘khalidwe limene munthu amakhala nalo mothandizidwa na mzimu woyela.’ (Agal. 5:22, 23) Liwu la Cigiriki lomasulidwa kuti “kufatsa” nthawi zina anali kuliseŵenzetsa pofotokoza za hachi yakuchile imene yayamba kuwetedwa. Hachiyo imakhala yodekha koma imakhalabe yamphamvu. Nanga ife tingakulitse bwanji khalidwe la kufatsa, koma pa nthawi imodzimodzi n’kukhalanso olimba? Izi sizingatheke mwa mphamvu zathu zokha. Koma zingatheke mwa kupempha mzimu wa Mulungu kuti utithandize kukulitsa khalidwe limeneli. Pali umboni woonetsa kuti zimenezi n’zotheka. Mboni zambili zimayankha mofatsa anthu akaziputa. Kutelo kwathandiza anthu kukhala na kaonedwe kabwino ka gulu lathu.​—2 Tim 2:24, 25. w23.09 15 ¶3

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025
Takulandilani
Ici ni cida cofufuzila m'mabuku olembewa na Mboni za Yehova mu vitundu volekana-lekana.
Ngati mufuna kucita daunilodi, yendani pa jw.org.
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani