Ciŵelu, October 4
Ndimacita zinthu zonse cifukwa ca uthenga wabwino, kuti ndilalikile uthengawu kwa anthu ena.—1 Akor. 9:23.
Zinthu zikasintha pa umoyo wathu, kuthandizabe ena n’kofunika kwambili, maka-maka mwa kulalikila. Tizikhala ololela pa utumiki wathu. Timakumana na anthu a zikhulupililo na maganizo osiyana-siyana, komanso ocokela kosiyana-siyana. Mtumwi Paulo anali wololela, ndipo tingatengeleko citsanzo cake. Yesu anaika Paulo kukhala ‘mtumwi wotumidwa kwa mitundu ina.’ (Aroma 11:13) Pa utumiki wake umenewo, Paulo analalikila kwa Ayuda, Agiriki, anthu ophunzila, alimi osauka, anyanchito a boma, komanso mafumu. Kuti awafike pa mtima anthu onsewo, Paulo ‘anakhala zinthu zonse kwa anthu osiyanasiyana.’ (1 Akor. 9:19-22) Poganizila cikhalidwe na zikhulupililo za anthu amene anali kuwalalikila, mtumwi Paulo anasintha njila yolalikila. Nafenso tingakhale alaliki ogwila mtima tikamakhala okonzeka kusintha ulaliki wathu kuti ugwilizane na munthu amene tapeza. w23.07 23 ¶11-12
Sondo, October 5
Kapolo wa Ambuye sayenela kukangana ndi anthu. Koma ayenela kukhala wodekha kwa onse.—2 Tim. 2:24.
Munthu akakhala wofatsa sindiye kuti ni wofooka. Zimafuna mphamvu kuti munthu akhalebe wodekha akaputidwa. Kufatsa ni ‘khalidwe limene munthu amakhala nalo mothandizidwa na mzimu woyela.’ (Agal. 5:22, 23) Liwu la Cigiriki lomasulidwa kuti “kufatsa” nthawi zina anali kuliseŵenzetsa pofotokoza za hachi yakuchile imene yayamba kuwetedwa. Hachiyo imakhala yodekha koma imakhalabe yamphamvu. Nanga ife tingakulitse bwanji khalidwe la kufatsa, koma pa nthawi imodzimodzi n’kukhalanso olimba? Izi sizingatheke mwa mphamvu zathu zokha. Koma zingatheke mwa kupempha mzimu wa Mulungu kuti utithandize kukulitsa khalidwe limeneli. Pali umboni woonetsa kuti zimenezi n’zotheka. Mboni zambili zimayankha mofatsa anthu akaziputa. Kutelo kwathandiza anthu kukhala na kaonedwe kabwino ka gulu lathu.—2 Tim 2:24, 25. w23.09 15 ¶3
Mande, October 6
Ndinkapempha . . . ndipo Yehova wandipatsa zimene ndinapempha.—1 Sam. 1:27.
M’masomphenya ocititsa cidwi, mtumwi Yohane anaona akulu 24 akulambila Yehova kumwamba. Iwo anatamanda Mulungu poona kuti ni woyenela kulandila “ulemelelo, ulemu ndi mphamvu.” (Chiv. 4:10, 11) Angelo okhulupilika nawonso ali na zifukwa zambili zotamandila Yehova na kum’lemekeza. Iwo amakhala naye kumwamba, ndipo anafika pom’dziŵa bwino kwambili. Amaona makhalidwe ake mwa zocita zake. Conco, amasonkhezeledwa kum’tamanda. (Yobu 38:4-7) Nafenso tizitamanda Yehova m’mapemphelo athu, mwa kuchula zimene timakonda komanso zimene timayamikila zokhudza iye. Pamene muŵelenga na kuphunzila Baibo, muziyesa kupeza makhalidwe a Yehova amene amakukhudzani mtima. (Yobu 37:23; Aroma 11:33) Kenako, muuzeni Yehova mmene mumamvela za makhalidwe akewo. Tingam’tamandenso cifukwa amatithandiza, komanso amathandiza abale na alongo athu.—1 Sam. 2:1, 2. w23.05 3-4 ¶6-7