Sondo, October 5
Kapolo wa Ambuye sayenela kukangana ndi anthu. Koma ayenela kukhala wodekha kwa onse.—2 Tim. 2:24.
Munthu akakhala wofatsa sindiye kuti ni wofooka. Zimafuna mphamvu kuti munthu akhalebe wodekha akaputidwa. Kufatsa ni ‘khalidwe limene munthu amakhala nalo mothandizidwa na mzimu woyela.’ (Agal. 5:22, 23) Liwu la Cigiriki lomasulidwa kuti “kufatsa” nthawi zina anali kuliseŵenzetsa pofotokoza za hachi yakuchile imene yayamba kuwetedwa. Hachiyo imakhala yodekha koma imakhalabe yamphamvu. Nanga ife tingakulitse bwanji khalidwe la kufatsa, koma pa nthawi imodzimodzi n’kukhalanso olimba? Izi sizingatheke mwa mphamvu zathu zokha. Koma zingatheke mwa kupempha mzimu wa Mulungu kuti utithandize kukulitsa khalidwe limeneli. Pali umboni woonetsa kuti zimenezi n’zotheka. Mboni zambili zimayankha mofatsa anthu akaziputa. Kutelo kwathandiza anthu kukhala na kaonedwe kabwino ka gulu lathu.—2 Tim 2:24, 25. w23.09 15 ¶3
Mande, October 6
Ndinkapempha . . . ndipo Yehova wandipatsa zimene ndinapempha.—1 Sam. 1:27.
M’masomphenya ocititsa cidwi, mtumwi Yohane anaona akulu 24 akulambila Yehova kumwamba. Iwo anatamanda Mulungu poona kuti ni woyenela kulandila “ulemelelo, ulemu ndi mphamvu.” (Chiv. 4:10, 11) Angelo okhulupilika nawonso ali na zifukwa zambili zotamandila Yehova na kum’lemekeza. Iwo amakhala naye kumwamba, ndipo anafika pom’dziŵa bwino kwambili. Amaona makhalidwe ake mwa zocita zake. Conco, amasonkhezeledwa kum’tamanda. (Yobu 38:4-7) Nafenso tizitamanda Yehova m’mapemphelo athu, mwa kuchula zimene timakonda komanso zimene timayamikila zokhudza iye. Pamene muŵelenga na kuphunzila Baibo, muziyesa kupeza makhalidwe a Yehova amene amakukhudzani mtima. (Yobu 37:23; Aroma 11:33) Kenako, muuzeni Yehova mmene mumamvela za makhalidwe akewo. Tingam’tamandenso cifukwa amatithandiza, komanso amathandiza abale na alongo athu.—1 Sam. 2:1, 2. w23.05 3-4 ¶6-7
Ciŵili, October 7
Mukhale ndi khalidwe logwilizana ndi zimene Yehova amafuna.—Akol. 1:10.
Mu 1919, anthu a Mulungu anamasuka ku Babulo Wamkulu. M’caka cimeneco, “kapolo wokhulupilika komanso wanzelu” anaikidwa kuti athandize anthu oona mtima kuyenda pa “Msewu wa Ciyelo” wamakono. (Mat. 24:45-47; Yes. 35:8) Nchito yokonza msewu umenewo imene amuna okhulupilika anagwila kalelo, ikuthandiza anthu oyenda pa msewu waukuluwo kuti adziŵe zambili zokhudza colinga ca Yehova. (Miy. 4:18) Iwo amathanso kusintha umoyo wawo kuti ugwilizane na miyeso ya Yehova. Yehova sayembekezela anthu ake kupanga masinthidwe onse panthawi imodzi. M’malo mwake, iye wakhala akuyenga anthu ake pang’ono-pang’ono. Tonsefe tidzakhala okondwa panthawi imene zocita zathu zonse zizikondweletsa Mulungu wathu! Kucokela mu 1919, nchito yokonza “Msewu wa Ciyelo” yakhala ikucitika, kuti anthu ambili acoke m’Babulo Wamkulu. w23.05 17 ¶15; 19 ¶16