Mande, October 6
Ndinkapempha . . . ndipo Yehova wandipatsa zimene ndinapempha.—1 Sam. 1:27.
M’masomphenya ocititsa cidwi, mtumwi Yohane anaona akulu 24 akulambila Yehova kumwamba. Iwo anatamanda Mulungu poona kuti ni woyenela kulandila “ulemelelo, ulemu ndi mphamvu.” (Chiv. 4:10, 11) Angelo okhulupilika nawonso ali na zifukwa zambili zotamandila Yehova na kum’lemekeza. Iwo amakhala naye kumwamba, ndipo anafika pom’dziŵa bwino kwambili. Amaona makhalidwe ake mwa zocita zake. Conco, amasonkhezeledwa kum’tamanda. (Yobu 38:4-7) Nafenso tizitamanda Yehova m’mapemphelo athu, mwa kuchula zimene timakonda komanso zimene timayamikila zokhudza iye. Pamene muŵelenga na kuphunzila Baibo, muziyesa kupeza makhalidwe a Yehova amene amakukhudzani mtima. (Yobu 37:23; Aroma 11:33) Kenako, muuzeni Yehova mmene mumamvela za makhalidwe akewo. Tingam’tamandenso cifukwa amatithandiza, komanso amathandiza abale na alongo athu.—1 Sam. 2:1, 2. w23.05 3-4 ¶6-7
Ciŵili, October 7
Mukhale ndi khalidwe logwilizana ndi zimene Yehova amafuna.—Akol. 1:10.
Mu 1919, anthu a Mulungu anamasuka ku Babulo Wamkulu. M’caka cimeneco, “kapolo wokhulupilika komanso wanzelu” anaikidwa kuti athandize anthu oona mtima kuyenda pa “Msewu wa Ciyelo” wamakono. (Mat. 24:45-47; Yes. 35:8) Nchito yokonza msewu umenewo imene amuna okhulupilika anagwila kalelo, ikuthandiza anthu oyenda pa msewu waukuluwo kuti adziŵe zambili zokhudza colinga ca Yehova. (Miy. 4:18) Iwo amathanso kusintha umoyo wawo kuti ugwilizane na miyeso ya Yehova. Yehova sayembekezela anthu ake kupanga masinthidwe onse panthawi imodzi. M’malo mwake, iye wakhala akuyenga anthu ake pang’ono-pang’ono. Tonsefe tidzakhala okondwa panthawi imene zocita zathu zonse zizikondweletsa Mulungu wathu! Kucokela mu 1919, nchito yokonza “Msewu wa Ciyelo” yakhala ikucitika, kuti anthu ambili acoke m’Babulo Wamkulu. w23.05 17 ¶15; 19 ¶16
Citatu, October 8
Sindidzakusiyani.—Aheb. 13:5.
Bungwe Lolamulila lakhala likuphunzitsa mwacindunji owathandiza m’makomiti awo osiyana-siyana. Abale othandiza amenewa akusenza maudindo akulu-akulu mokhulupilika. Iwo aphunzitsidwa bwino kuti apitilize kugwila nchito yosamalila nkhosa za Khristu. Odzozedwa akadzatha onse kutengedwa kupita kumwamba, cakumapeto kwa cisautso cacikulu, kulambila koyela kudzapitilizabe pano padziko lapansi. Ndife oyamikila kuti utsogoleli wa Khristu udzathandiza kuti olambila Mulungu adzapitilize kumulambila mokhulupilika. N’zoona kuti panthawiyo Gogi wa Magogi adzatiukila, amene ni mgwilizano wankhanza wa mitundu. (Ezek. 38:18-20) Koma kutiukila kwa kanthawi kumeneku sikudzapambana; sikudzalepeletsa anthu a Mulungu kulambila Yehova. Iye adzawapulumutsa ndithu! M’masomphenya, mtumwi Yohane anaona “khamu lalikulu” lomwe ni gulu la nkhosa zina za Khristu. Yohane anauzidwa kuti “khamu lalikulu” limeneli ‘latuluka m’cisautso cacikulu.’ (Chiv. 7:9, 14) Inde, iwo adzatetezedwa! w24.02 5-6 ¶13-14