Cisanu, July 25
Ine ndili limodzi ndi inu masiku onse mpaka mʼnyengo ya mapeto a nthawi ino.—Mat. 28:20.
Kucokela pa nkhondo yaciŵili ya padziko lonse, anthu a Yehova m’maiko ambili anapezako mtendele komanso ufulu pogwila nchito yolalikila. Ndipo nchitoyi yapita patsogolo kwambili. Masiku anonso, a m’Bungwe Lolamulila akupitiliza kuyang’ana kwa Khristu kaamba ka citsogozo. Amafuna kuti malangizo amene amapeleka kwa abale na alongo azikhala ogwilizana na cifunilo ca Mulungu. Ndipo amaseŵenzetsa oyang’anila madela, komanso akulu popeleka malangizo amenewa ku mipingo. Akulu odzodzedwa ali “m’dzanja . . . lamanja” la Khristu. (Chiv. 2:1) Akulu amenewa ni opanda ungwilo ndipo nthawi zina amalakwitsa. Mose, Yoswa, komanso atumwi anali kulakwitsa zinthu nthawi zina. (Num. 20:12; Yos. 9:14, 15; Aroma 3:23) Ngakhale n’telo, Khristu akutsogolela kapolo wokhulupilika, komanso akulu osankhidwa, ndipo adzapitiliza kukhala nawo. Cotelo, tili na zifukwa zomveka zokhalila na cidalilo m’citsogozo cimene Yesu akupeleka kupitila mwa awo amene anasankhidwa kuti azititsogolela. w24.02 23-24 ¶13-14
Ciŵelu, July 26
Muzitsanzila Mulungu, monga ana ake okondedwa.—Aef. 5:1.
Masiku ano, tingamukondweletse Yehova pokamba za iye mwaubwenzi, moyamikila, komanso mwacikondi. Tikakhala mu utumiki timakumbukila kuti colinga cathu cacikulu ni kukokela anthu kwa Yehova, na kuwathandiza kumuona monga Tate wacikondi mmene ifeyo timamuonela. (Yak. 4:8) Timakondwela kusonyeza anthu mmene Baibo imamufotokozela Yehova, mmene imaonetsela cikondi cake, cilungamo cake, nzelu zake, mphamvu zake, komanso makhalidwe ena abwino. Timatamandanso Yehova na kumukondweletsa pamene tiyesetsa kutengela citsanzo cake. Tikatelo, timakhala osiyana nawo anthu oipa a m’dzikoli. Anthu angaone kuti ndife osiyana nawo, ndipo angafune kudziŵa cifukwa cake. (Mat. 5:14-16) Pocita nawo zinthu za tsiku na tsiku, tingawafotokozele cifukwa cake timacita zinthu zina mosiyana. Zotsatila zake n’zakuti, timakokela anthu a mitima yabwino kwa Mulungu wathu. Tikamatamanda Yehova m’njila zimenezi, timakondweletsa mtima wake.—1 Tim. 2:3, 4. w24.02 10 ¶7
Sondo, July 27
[Muzitha] kulimbikitsa . . . ndiponso kudzudzula.—Tito 1:9.
Kuti mukhale Mkhristu wokhwima, muyenela kukulitsa maluso othandiza. Izi zidzakuthandizani kusenza maudindo mu mpingo, kupeza nchito yokuthandizani inuyo na banja lanu, komanso kukhala paubwenzi wabwino na anthu ena. Mwacitsanzo, phunzilani kuŵelenga na kulemba bwino. Baibo imati mwamuna wacimwemwe komanso wopambana amaseŵenzetsa nthawi yake kuŵelenga Mawu a Mulungu na kuwasinkhasinkha. (Sal. 1:1-3) Kuŵelenga Baibo tsiku lililonse kumam’thandiza kudziŵa bwino kaganizidwe ka Yehova, zimene zimamuthandiza kukhala woganiza bwino. (Miy. 1:3, 4) Abale na alongo athu amayang’ana kwa amuna oyenelela akafuna malangizo. Ngati mumatha kuŵelenga na kulemba, mudzakwanitsa kukonzekela nkhani na ndemanga zogwila mtima komanso zolimbikitsa cikhulupililo. Mudzakwanitsanso kulemba manotsi atanthauzo amenewa adzakuthandizani kulimbitsa cikhulupililo canu komanso kulimbikitsa ena. w23.12 26-27 ¶9-11