July
Ciŵili, July 1
Anayenda mʼdziko lonse nʼkumacita zabwino ndiponso kucilitsa.—Mac. 10:38.
Zonse zimene Yesu anakamba na kucita, kuphatikizapo zozizwitsa, zinaonetsa bwino maganizo a Atate wake na mmene iwo amamvela. (Yoh. 14:9) Kodi zozizwitsa za Yesu zimatiphunzitsa ciyani? Yesu na Atate wake amatikonda kwambili. Ali pa dziko lapansi, Yesu anaonetsa kuzama kwa cikondi cake pa anthu. Anatelo mwa kugwilitsa nchito mphamvu zake zocita zozizwitsa pothandiza nazo anthu ovutika. Panthawi ina, amuna aŵili akhungu anam’condolela kuti awathandize. (Mat. 20:30-34) Onani kuti Yesu “atagwidwa ndi cifundo,” anawacilitsa. Palembali, mawu Acigiriki amene anamasulidwa kuti ‘kugwidwa ndi cifundo’ amatanthauza kukhudzika mtima kwambili. Cifundo cacikuluci, cimenenso ni njila ina yoonetsela cikondi, cinapangitsa Yesu kudyetsa anjala komanso kucilitsa munthu wakhate. (Mat. 15:32; Maliko 1:41) Tingakhale na cidalilo kuti Yehova, Mulungu “wacifundo cacikulu,” na Mwana wake amatikonda ngako, ndipo zimawapweteka mtima akamationa tikuvutika. (Luka 1:78; 1 Pet. 5:7) Iwo ayenela kuti ni ofunitsitsa kwambili kucotsa mavuto onse amene amavutitsa mtundu wa anthu! w23.04 3 ¶4-5
Citatu, July 2
Inu amene mumakonda Yehova, muzidana ndi zoipa. Iye amateteza moyo wa anthu ake okhulupilika. Amaŵapulumutsa mʼmanja mwa oipa.—Sal. 97:10.
Tingayesetse kupewa maganizo oipa ofala m’dziko la Satanali. Tiyenela kudzaza maganizo athu na zinthu zabwino mwa kuŵelenga Baibo na kuiphunzila. Cina cimene cingateteze maganizo athu, ni kupezeka ku misonkhano komanso kulalikila. Ndipo Yehova analonjeza kuti sadzalola kuti tiyesedwe kufika pamene sitingapilile. (1 Akor. 10:12, 13) Kuti tikhalebe okhulupilika kwa Yehova m’masiku ano ovuta, aliyense wa ife ayenela kupemphela kwambili kuposa kale lonse. Yehova amafuna kuti tikamapemphela, ‘tizim’khuthulila zamumtima mwathu.’ (Sal. 62:8) Mtamandeni Yehova na kumuyamikila pa zonse zimene amaticitila. Cina, m’pempheni kuti akulimbitseni mtima mu ulaliki. Cinanso, m’condeleleni kuti akuthandizeni kupilila vuto lililonse komanso kukaniza mayeselo. Conde, musalole ciliconse kapena aliyense kukuletsani kupemphela kwa Yehova nthawi zonse. w23.05 7 ¶17-18
Cinayi, July 3
Tiyeni tiganizilane kuti tilimbikitsane.—Aheb. 10:24, 25.
N’cifukwa ciyani timapezeka kumisonkhano ya mpingo? Cifukwa cacikulu ni kutamanda Yehova. (Sal. 26:12; 111:1) Timapezekanso kumisonkhano kuti tilimbikitsane m’nthawi zino zovuta. (1 Ates. 5:11) Tikakweza dzanja na kupelekapo ndemanga, timakwanilitsa zolinga ziŵili zimenezi. Koma pali zinthu zimene zingatimange pofuna kupeleka ndemanga. Tingamadodome, kapena tingamafunitsitse kuyankhapo kangapo, koma sitikupatsidwa mwayi mmene tikufunila. N’ciyani cingatithandize pambali zimenezi? Mtumwi Paulo anati tikasonkhana pamodzi, colinga cathu cizikhala ‘kulimbikitsana.’ Tikadziŵa kuti ndemanga yathu idzalimbitsa cikhulupililo ca ena, sitidzadodoma kukweza dzanja kuti tiyankhepo, ngakhale itakhala yaifupi. Ndipo ngati sitinapatsidwe mwayi woyankhapo kangapo, tizikhalabe okondwela kuti ena akhala na mpata wopelekapo ndemanga zawo.—1 Pet. 3:8. w23.04 20 ¶1-3
Cisanu, July 4
[Pitani] ku Yerusalemu, . . . nʼkukamanganso nyumba ya Yehova.—Ezara 1:3.
Mfumu inalengeza kuti Ayuda amene anali akapolo ku Babulo kwa zaka 70, ni omasuka kubwelela kawo ku Isiraeli. (Ezara 1:2-4) Ni Yehova yekha akanatheketsa zimenezi. Cifukwa Ababulo sanali kumasula akapolo awo. (Yes. 14:4, 17) Koma Babulo anali atagonjetsedwa, ndipo wolamulila watsopano anauza Ayuda kuti angabwelele kwawo. Conco Myuda aliyense, maka-maka mitu ya mabanja, inayenela kusankha kaya kukhalabe ku Babulo kapena kucoka. Kupanga cisankho cimeneci sikunali kopepuka. Kwa okalamba, zinali zovuta kupanga ulendo umenewo. Cina, Ayuda ambili anabadwila ku Babulo, ndipo ndilo dziko lokhalo limene anali kudziŵa. Kwa iwo, Isiraeli inali dziko la makolo awo. Ndipo zioneka kuti Ayuda ena anali kukhala umoyo wa wofu-wofu ku Babulo. Conco, cinali covuta kusiya nyumba zawo zabwino na malonda awo, kuti akakhale m’dziko lacilendo limenelo. w23.05 14 ¶1-2
Ciŵelu, July 5
Khalani okonzeka.—Mat. 24:44.
Mawu a Mulungu amatilimbikitsa kusaleka kukulitsa makhalidwe a kupilila, cifundo, na cikondi. Luka 21:19 imati: “Ngati inu mudzapilile, mudzapeza moyo.” Akolose 3:12 nayonso imati: “Valani . . . cifundo cacikulu.” Ndipo 1 Atesalonika 4:9, 10 imati: “Mulungu amakuphunzitsani kukondana. . . . Koma tikukudandaulilani abale kuti mupitilize kutelo mowonjezeleka.” Malembawa analembela ophunzila omwe anali kuonetsa kale kupilila, cifundo, na cikondi. Komabe, anayenela kupitiliza kukulitsa makhalidwe amenewa. Nafenso tiyenela kucita cimodzimodzi. Onani mmene Akhristu oyambilila anaonetsela makhalidwewa. Kenaka, onani mmene mungatengele citsanzo cawo, kuti muonetse kuti mukucikonzekela cisautso cacikulu. Ndiyeno cisautso cacikulu cikadzayamba, mudzakhala mutaphunzila kupilila, ndipo mudzakhala wofunitsitsa kupililabe. w23.07 3 ¶4, 8
Sondo, July 6
Kumeneko kudzakhala msewu waukulu . . . Msewu Wopatulika.—Yes 35:8.
Kaya ndife odzozedwa kapena a “nkhosa zina,” tiyenela kuyendabe pa “Msewu wa Ciyelo,” umene ukutitsogolela ku paradaiso wauzimu, komanso ku madalitso a Ufumu a m’tsogolo. (Yoh. 10:16) Kuyambila 1919, amuna, akazi, komanso ana akhala akucoka mu Babulo Wamkulu, ufumu wa dziko lonse wa cipembedzo conyenga, ndipo ayamba kuyenda pa msewu wophiphilitsa umenewo. Yehova anaonetsetsa kuti wacotsa zopinga zonse zimene Ayuda akanakumana nazo pa ulendo wawo wocoka ku Babulo. (Yes. 57:14) Nanga bwanji za “Msewu wa Ciyelo” wamakono? Kwa zaka mahandiledi ambili cisanafike caka ca 1919, Yehova anaseŵenzetsa amuna omuopa kukonza msewu wothandiza anthu kutuluka m’Babulo Wamkulu. (Yelekezelani na Yesaya 40:3.) Iwo anayamba kukonza msewu wauzimu, kuti athandize anthu a maganizo abwino kucoka mu Babulo Wamkulu, na kuloŵa m’paradaiso wauzimu. w23.05 15-16 ¶8-9
Mande, July 7
Tumikilani Yehova mokondwela. Bwelani kwa iye mukufuula mosangalala.—Sal. 100:2.
Yehova amafuna kuti tizim’tumikila mokondwela komanso mofunitsitsa. (2 Akor. 9:7) Koma kodi tiyenela kuyesetsa kukwanilitsa colinga cathu ngakhale pamene tilibe cikhumbo? Ganizilani citsanzo ca mtumwi Paulo. Iye anati: “Ndikulanga thupi langa nʼkulicititsa kukhala ngati kapolo,.” (1 Akor. 9:25-27, mawu a m’munsi) Paulo anadzikakamiza kucita zoyenela ngakhale pamene analibe cikhumbo cocita zimenezo. Kodi Yehova anakondwela nawo utumiki wa Paulo? Inde! Ndipo Yehova anam’dalitsa kaamba ka kuyesetsa kwake.(2 Tim. 4:7, 8) Mofananamo, Yehova amakondwela akationa tikuyesetsa kukwanilitsa zolinga zathu ngakhale pamene tilibe cikhumbo cocita zimenezo. Amakondwela cifukwa amadziŵa kuti timacita zimenezo cifukwa com’konda, ngakhale pamene tilibe cikhumbo cocita utumikiwo. Monga Paulo, nafenso Yehova adzatidalitsa pa kuyesetsa kwathu. (Sal. 126:5) Ndipo tikadziŵa kuti Yehova akutidalitsa, cikhumbo cathu cimakula. w23.05 29 ¶9-10
Ciŵili, July 8
Tsiku la Yehova lidzabwela.—1 Ates. 5:2.
Mtumwi Paulo anayelekezela anthu amene sadzapulumuka tsiku la Yehova na anthu amene ali mtulo. Iwo sadziŵa zimene zikucitika kapena mmene nthawi ikupitila. Conco, saona zocitika zikulu-zikulu zimene zikucitika ndipo sacitapo kanthu. Anthu ambili masiku ano ali m’tulo twauzimu. (Aroma 11:8) Iwo sakhulupilila maumboni oonetsa kuti tikukhala “m’masiku otsiliza,” komanso kuti cisautso cacikulu cifika posacedwa. (2 Pet. 3:3, 4) Komabe, tsiku lililonse likamadutsa, m’pofunika kwambili kutsatila uphungu wouzilidwa wakuti tikhalebe maso. (1 Ates. 5:6) N’cifukwa ciyani tiyenela kukhala odekha komanso osasunthika? Kuti tisatengeke na zandale kapena zocitika zina za m’dzikoli. Pamene tsiku la Yehova likuyandikila, tingakakamizike kwambili kutengako mbali m’zinthu zimenezi. Koma sitiyenela kuda nkhawa na mmene tikacitile. Pa nthawiyo, mzimu wa Mulungu udzatithandiza kukhala odekha komanso osasunthika, kuti tipange zisankho zabwino.—Luka 12:11, 12. w23.06 10 ¶6-7
Citatu, July 9
Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, conde, ndikumbukileni ndi kundipatsa mphamvu.—Ower. 16:28.
N’ciyani cimabwela m’maganizo mwanu mukamva dzina lakuti Samisoni? Ngati mumaganizila za mwamuna wamphamvu zodabwitsa, simunaphonye. Koma Samisoni anapanga cisankho coipa cimene pambuyo pake cinam’bweletsela mavuto aakulu kwambili. Ngakhale n’conco, Yehova anayang’ana pa kukhulupilika kumene Samisoni anaonetsa pom’tumikila. Anaonetsetsanso kuti nkhani yake yalembedwa m’Baibo kuti itipindulile. Yehova anaseŵenzetsa Samisoni kucita zinthu zodabwitsa kuti athandize anthu ake osankhidwa, Aisiraeli. Patapita zaka mahandiledi Samisoni atamwalila, Yehova anauzila mtumwi Paulo kuti aphatikize dzina la Samisoni pa mndandanda wa maina a anthu a cikhulupililo colimba. (Aheb. 11:32-34) Citsanzo ca Samisoni cingatilimbikitse. Iye anadalila Yehova ngakhale panthawi zovuta. Citsanzo ca Samisoni cingatilimbikitse kwambili, ndipo tingaphunzile zambili kwa iye. w23.09 2 ¶1-2
Cinayi, July 10
Zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.—Afil. 4:6.
Cimene tingacite kuti tikhale opilila, ni kupemphela kwa Yehova mocokela pansi pa mtima nthawi zonse, na kumuuza nkhawa zathu. (1 Ates. 5:17) N’kutheka kuti pali pano simukukumana na mayeso aakulu. Ngakhale n’telo, muyenela kupemphabe citsogozo kwa Yehova mukakhumudwa kapena kuthedwa nzelu. Ngati pali pano mumatembenukila kwa Mulungu kuti akuthandizeni pa zovuta za tsiku na tsiku, simudzazengeleza kukacita zimenezo mukadzakumana na mavuto aakulu m’tsogolomu. Ndipo mudzakhala wotsimikiza kuti iye amadziŵa nthawi yabwino yokuthandizani, komanso mmene angacitile zimenezo. (Sal. 27:1, 3) Tikamapilila mavuto pali pano, tingadzapililenso cisautso cacikulu m’tsogolomu. (Aroma 5:3) N’cifukwa ciyani tikutelo? Abale na alongo athu ambili aona kuti akapilila mayeso oyesa cikhulupililo cawo, amatha kupililanso ena. Kupilila kumawayenga na kulimbitsa cidalilo cawo cakuti Yehova ni wokonzeka komanso wofunitsitsa kuwathandiza. Ndipo cidaliloco cimawathandiza kupilila mayeso alionse.—Yak 1:2-4. w23.07 3 ¶7-8
Cisanu, July 11
Ndavomela zimene wapempha.—Gen. 19:21.
Kudzicepetsa kwa Yehova na cifundo cake, zimamulimbikitsa kukhala wololela. Mwacitsanzo, kudzicepetsa kwa Yehova kuonaonekela bwino atatsala pang’ono kuwononga anthu oipa a mu Sodomu. Kupitila mwa angelo ake, Yehova anauza munthu wolungama Loti kuti athaŵile kumapili. Koma Loti anaopa kupita kumeneko. Conco, anacondelela Mulungu kuti amulole pamodzi na banja lake kuti athaŵile mu mzinda waung’ono wa Zowari, umene unayenelanso kuwonongedwa. Yehova akanafuna akanaumilila ndithu kuti Loti angotsatila malangizowo ndendende. Koma m’malo mwake, iye anamva pempho la Loti, ngakhale kuti izi zinatanthauza kusawononga mzinda wa Zowari. (Gen. 19:18-22) Patapita zaka mahandiledi, Yehova anaonetsa cifundo kwa anthu a ku Nineve. Anatuma mneneli Yona kukalengeza kuti mzindawo pamodzi na anthu oipa okhala mmenemo adzawonongedwa. Koma anthu a ku Nineve atalapa, Yehova anawamvela cisoni, ndipo sanauwononge mzindawo.—Yona 3:1, 10; 4:10, 11. w23.07 21 ¶5
Ciŵelu, July 12
Iwo [Anamupha Yehoasi] . . . , koma sanamuike mʼmanda a mafumu.—2 Mbiri 24:25.
Kodi tiphunzila ciyani kwa Yehoasi? Iye anali ngati mtengo umene mizu yake sinazikike pansi kwambili, ndipo unali kudalila mzati kuti usagwe. Koma pamene mzatiwo—Yehoyada—unacoka ndiponso cimphepo campatuko cinawomba, iye anagwa. Nkhaniyi itiphunzitsa kuti kuopa kwathu Mulungu, sikuyenela kudalila kwambili Akhristu anzathu, ngakhalenso a m’banja mwathu. Kuti tikhalebe olimba mwauzimu, tiyenela kukulitsa cikondi komanso mantha athu pa iye, mwa kuphunzila Baibo nthawi zonse, kusinkhasinkha, na kupemphela. (Yer. 17:7, 8; Akol. 2:6, 7) Yehova sayembekezela zambili kwa ife. Zimene amafuna kwa ife zinafotokozedwa pa Mlaliki 12:13, imene imati: “Opa Mulungu woona ndi kusunga malamulo ake cifukwa zimenezi ndiye zimene munthu ayenela kucita.” Tikamaopa Mulungu, tidzatha kuima nji poyang’anizana na mayeso alionse m’tsogolomu. Palibe cimene cidzatha kuwononga ubale wathu na Yehova. w23.06 19 ¶17-19
Sondo, July 13
Taonani! Zinthu zonse zimene ndikupanga ndi zatsopano.—Chiv. 21:5.
Mulungu potitsimikizila anayamba na mawu akuti: “Ndipo wokhala pampando wacifumu anati.” (Chiv. 21:5a) Aka kanali koyamba pa maulendo atatu pamene Yehova iye mwini analankhula m’masomphenya m’buku la Chivumbulutso. Citsimikizo cimeneci cinapelekedwa na Yehova mwini wakeyo, osati na mngelo wamphamvu winawake, kapena Yesu woukitsidwayo ayi! Zimenezi zionetsa kudalilika kwa mawu otsatilapo. N’cifukwa ciyani? Cifukwa Yehova “sanganame.” (Tito 1:2) Mawu amenewo atitsimikizila kuti zimene timaŵelenga pa Chivumbulutso 21:5, 6 n’zodalilikadi. Ganizilani liwu lakuti “Taonani!” Liwu la Cigiriki limene anamasulila kuti “taonani!” analiseŵenzetsa mobweleza-bweleza m’buku la Chivumbulutso. Kodi Mulungu ananena ciyani pambuyo pa mfuulilo umenewu? Iye anati: “Zinthu zonse zimene ndikupanga n’zatsopano.” N’zoona kuti Yehova anali kunena za masinthidwe a m’tsogolo, koma iye anali wotsimikiza kuti zidzacitikadi, moti ananena ngati zikucitika.—Yes. 46:10. w23.11 3-4 ¶7-8
Mande, July 14
Anatuluka panja nʼkuyamba kulila mopwetekedwa mtima kwambili.—Mat. 26:75.
Mtumwi Petulo anali kulimbana na zifooko zake. Onankoni zitsanzo izi. Yesu atafotokoza mmene adzavutikile komanso kuphedwa kwake pokwanilitsa ulosi wa m’Baibo, Petulo anam’dzudzula. (Maliko 8:31-33) Mobweleza-bweleza, Petulo na atumwi anzake anali kukangana za amene anali wamkulu pakati pawo. (Maliko 9:33, 34) Pa usiku wakuti maŵa lake Yesu aphedwa, mopupuluma Petulo anadula khutu la munthu wina. (Yoh. 18:10) Ndipo usiku womwewo, cifukwa coopa anthu, Petulo anakana bwenzi lake Yesu katatu konse kuti sam’dziŵa. (Maliko 14:66-72) Izi zinapangitsa Petulo kulila mopwetekedwa mtima ngako. Yesu sanamusiye mtumwi wake wolefulidwayo. Yesu ataukitsidwa, anapeleka mwayi kwa Petulo wakuti aonetse ngati akali kum’konda. Yesu anaika Petulo kukhala m’busa wodzicepetsa wa nkhosa zake. (Yoh. 21:15-17) Iye anauvomela udindo umenewo. Pa tsiku la Pentekosite, Petulo anali ku Yerusalemu, ndipo anali pagulu la Akhristu oyamba kudzozedwa na mzimu woyela. w23.09 22 ¶6-7
Ciŵili, July 15
Weta ana a nkhosa anga.—Yoh. 21:16.
Mtumwi Petulo analimbikitsa akulu anzake kuti “Wetani gulu la nkhosa za Mulungu.” (1 Pet. 5:1-4) Ngati ndinu mkulu, tidziŵa kuti mumawakonda abale na alongo ndipo mufuna kuwasamalila. Komabe, nthawi zina mungamadzimve kuti simungakwanitse kusamalila udindo umenewu cifukwa cokhala wotopa kapena wotangwanika kwambili. Ngati zakhala conco, khutulilani Yehova nkhawa zanuzo. Petulo analemba kuti: “Ngati wina akutumikila, atumikile modalila mphamvu imene Mulungu amapeleka.” (1 Pet. 4:11) Abale komanso alongo anu angakumane na mavuto amene sangathetsedwe m’dongosolo lino la zinthu. Koma muzikumbukila kuti Yesu ‘mbusa wamkulu,’ angathe kuwathandiza kuposa wina aliyense. Angakwanitse kucita zimenezi palipano ndiponso m’dziko latsopano. Mulungu amafuna kuti akulu azionetsa cikondi kwa abale awo, kuwaweta komanso kuti akhale “zitsanzo kwa gulu la nkhosa.” w23.09 29-30 ¶13-14
Citatu, July 16
Yehova amadziŵa kuti maganizo a anthu anzelu ndi opanda pake.—1 Akor. 3:20.
Tizipewa kudalila nzelu za anthu. Tikamaona zinthu potengela maganizo a anthu, tinganyanyale Yehova na miyeso yake. (1 Akor 3:19) “Nzelu za m’dzikoli” nthawi zambili zimapangitsa anthu kusamvela Mulungu. Akhristu angapo a mu mzinda wa Pegamo komanso Tiyatira, anatengela kapenyedwe ka anthu owazungulila pa nkhani ya kulambila mafano, ndiponso zaciwelewele. Yesu anapeleka uphungu wamphamvu kwa Akhristu a m’mizindayi cifukwa colekelela zaciwelewele. (Chiv. 2:14, 20) Masiku anonso, timayesedwa kuti titengele maganizo oipa a dzikoli. Acibale athu na anansi athu, angamatinyengelele kuti tiphwanye malamulo a Yehova. Mwacitsanzo, angamatiuze kuti kutsatila zilakolako za thupi si nkhani yaikulu, komanso kuti malamulo a m’Baibo ni acikalekale. Nthawi zina, tingaganize kuti malangizo amene Yehova amatipatsa si okwanila. Tingafike pofuna ‘kupitilila zinthu zolembedwa.’—1 Akor. 4:6. w23.07 16 ¶10-11
Cinayi, July 17
Mnzako weniweni amakusonyeza cikondi nthawi zonse, ndipo ndi mʼbale amene anabadwa kuti akuthandize pakagwa mavuto.—Miy. 17:17.
Mariya mayi wa Yesu anali kufunikila mphamvu. Iye anali wosakwatiwa, koma anali kudzakhala na mimba. Cina, anali asanalelepo mwana, koma anali kudzalela mwana amene anali kudzakhala Mesiya. Ndipo popeza anali namwali, kodi akanafotokoza bwanji nkhaniyi kwa Yosefe amene anali kufuna kum’kwatila? (Luka 1:26-33) Kodi Mariya anapeza bwanji mphamvu? Anapempha thandizo kwa ena. Mwacitsanzo, iye anapempha mngelo Gabirieli kuti amuuze zowonjezeleka zokudza utumiki umenewo. (Luka 1:34) Posakhalitsa, Mariya anayenda ulendo wautali n’kupita “kudela lamapili” kudziko la Yuda kuti akaone wacibale wake Elizabeti. Elizabeti anayamikila Mariya, ndipo mouzilidwa na Yehova anakamba ulosi wolimbikitsa ponena za mwana amene anali kudzabadwayo. (Luka 1:39-45) Mariya anakamba kuti Yehova “wacita zamphamvu ndi dzanja lake.” (Luka 1:46-51) Yehova analimbikitsa Mariya kupitila mwa mngelo Gabirieli, komanso Elizabeti. w23.10 14-15 ¶10-12
Cisanu, July 18
Nʼkutipanga kukhala mafumu ndi ansembe kuti titumikile Mulungu wake ndi Atate wake.—Chiv. 1:6.
Ophunzila a Khristu oŵelengeka anadzozedwa na mzimu woyela, ndipo amasangalala kukhala paubale wapadela na Yehova. A 144,000 amenewa azikatumikila pamodzi na Yesu kumwamba monga ansembe. (Chiv. 14:1) Malo Oyela m’cihema amaimila kudzozedwa kwawo monga ana a Mulungu pa dziko lapansi. (Aroma 8:15-17) Malo Oyela Koposa amaimila kumwamba kumene Yehova amakhala. “Nsalu yochinga” imene inalekanitsa Malo Oyela na Malo Oyela Koposa inali kuimila thupi la Yesu laumunthu limene linali kumulepheletsa kuloŵa kumwamba monga Mkulu Wansembe woposa onse wakacisi wauzimu. Pomwe Yesu anapeleka nsembe thupi lake laumunthu, anatsegulila Akhristu odzozedwa njila yopita kumwamba. Iwo ayenela kusiya matupi awo aumunthu kuti akalandile mphoto yawo kumwamba.—Aheb. 10:19, 20; 1 Akor. 15:50. w23.10 28 ¶13
Ciŵelu, July 19
Nthawi indicepela kuti ndipitilize kufotokoza za Gidiyoni.—Aheb. 11:32.
Gidiyoni anayankha mofatsa pamene a Efuraimu anamuimba mlandu. (Ower. 8:1-3) Iye sanayankhe mwaukali. Anaonetsa kudzicepetsa mwa kumvetsela zokamba zawo, ndipo mwaluso anabweza mkwiyo wawo. Akulu anzelu amatengela citsanzo ca Gidiyoni mwa kumvetsela mwachelu, komanso kuyankha mofatsa ena akamawaimba mlandu. (Yak. 3:13) Mwakutelo, iwo amalimbikitsa mtendele mu mpingo. Gidiyoni atatamandidwa cifukwa cogonjetsa Amidiyani, anapeleka citamandoco kwa Yehova. (Ower. 8:22, 23) Kodi amuna apaudindo angatengele motani citsanzo ca Gidiyoni? Iwo ayenela kupeleka citamando kwa Yehova pa zimene iwowo akwanitsa kucita. (1 Akor. 4:6, 7) Mwacitsanzo, mkulu akayamikilidwa cifukwa ca luso lake la kuphunzitsa, anganene kuti malangizowo acokela m’Mawu a Mulungu, komanso kuti gulu la Yehova n’limene limatiphunzitsa tonsefe. Akulu ayenela kudziunika kuti aone ngati amaphunzitsa m’njila imene imalemekeza Yehova, kapena ngati akudzifunila ulemelelo. w23.06 4 ¶7-8
Sondo, July 20
Maganizo anga ndi osiyana ndi maganizo anu.—Yes. 55:8.
Ngati sitinalandile cinthu cimene takhala tikupemphelela, tingafunike kudzifunsa kuti, ‘Kodi nikupemphelela cinthu coyenela?’ Nthawi zambili timaona kuti tidziŵa zoyenela kwa ife. Koma nthawi zina zimene timapemphela sizingatiphindulile kwenikweni. Tikamapemphelela za vuto linalake, pangakhale njila ina yabwino yothetsela vutolo kuposa imene tikupempha. Ndipo nthawi zina zimene timapemphelela sizingakhale zogwilizana na cifunilo ca Yehova. (1 Yoh. 5:14) Mwacitsanzo, ganizilani za makolo amene anapempha Yehova kuti athandize mwana wawo kukhalabe m’coonadi. Pempho limenelo lingakhale lomveka. Koma Yehova sakakamiza aliyense kumutumikila. Iye amafuna kuti tonsefe, kuphatikizapo ana athu, tidzisankhile tokha kum’tumikila. (Deut. 10:12, 13; 30:19, 20) Conco m’malomwake, makolo angapemphe kuti Yehova awathandize kum’fika pamtima mwana wawo pom’phunzitsa kuti adzisankhile yekha kukonda Yehova na kukhala bwenzi lake.—Miy. 22:6; Aef. 6:4. w23.11 21 ¶5; 23 ¶12
Mande, July 21
Pitilizani kutonthozana.—1 Ates. 4:18.
N’cifukwa ciyani kutonthoza ena ili njila yabwino yowaonetsela cikondi? Buku lina lofotokoza Baibo linakamba kuti mawu amene mtumwi Paulo anaseŵenzetsa akuti “kutonthoza” amatanthauza “kukhala pafupi na munthu kuti timutonthoze pamene akumana na zovuta zazikulu.” Motelo, tikatonthoza wolambila mnzathu, timam’thandiza kuti apeze mphamvu, ndiponso kuti apitilizebe kuyenda pa njila ya ku moyo. Conco, nthawi iliyonse tikatonthoza abale na alongo athu, timaonetsa kuti timawakonda. (2 Akor. 7:6, 7, 13) Pali kugwilizana pakati pa kumvela ena cifundo komanso kuwatonthoza. Motani? Munthu amene wagwidwa cifundo, amayesetsa kutonthoza ena komanso kuwathandiza pa mavuto awo. Coyamba, timagwidwa na cisoni, kenako timapeleka thandizo. Onani mmene mtumwi Paulo akugwilizanitsila cifundo ca Yehova na citonthozo cimene amapeleka. Paulo akufotokoza kuti Yehova ni “Atate wacifundo cacikulu ndi Mulungu amene amatitonthoza m’njila iliyonse.”—2 Akor. 1:3. w23.11 9-10 ¶8-10
Ciŵili, July 22
[Sangalalani mukakumana] ndi mavuto.—Aroma 5:3.
Otsatila onse a Khristu amadziŵa kuti angazunzidwe. Ganizilani citsanzo ca mtumwi Paulo. Iye analembela Atesalonika kuti: “Pamene tinali nanu limodzi, tinali kukuuzilanitu kuti tiyenela kudzakumana ndi masautso, ndipo mmene zacitikilamu ndi mmenenso inu mukudziŵila.” (1 Ates. 3:4) Analembelanso Akorinto kuti: “Abale, sitikufuna kuti mukhale osadziŵa za masautso amene tinakumana nawo . . . Tinalibenso ciyembekezo coti tikhala ndi moyo.” (2 Akor. 1:8; 11:23-27) Ngakhale masiku ano, Akhristu angayembekezele kuzunzidwa m’njila inayake. (2 Tim. 3:12) Cifukwa cokhulupilila Yesu na kuyamba kum’tsatila, mabwenzi komanso acibale anu angakucitileni nkhanza. Kodi munakumanapo na mavuto ku nchito cifukwa cocita zinthu moona mtima? (Aheb. 13:18) Kodi munazunzidwapo na boma cifukwa couzako ena ciyembekezo canu? Paulo anati tizisangalala mosasamala kanthu za mtundu wa masautso amene takumana nawo. w23.12 10-11 ¶9-10
Citatu, July 23
Mwandiputila mavuto aakulu.—Gen. 34:30.
Yakobo anapilila mavuto ambili. Ana ake aŵili Simiyoni na Levi, ananyazitsa banja lawo, komanso anatonzetsa dzina la Mulungu. Kuwonjezela apo, Rakele mkazi wake wokondeka, anamwalila pobeleka mwana wawo waciŵili. Ndipo cifukwa ca njala yaikulu, Yakobo anakakamizika kusamukila kudziko la Iguputo muukalamba wake. (Gen. 35:16-19; 37:28; 45:9-11, 28) Mosasamala kanthu za mavuto onsewa, Yakobo sanataye cikhulupililo cake mwa Yehova na malonjezo Ake. Ndipo nayenso Yehova anaonetsa kuti anali kumuyanja Yakobo. Mwa citsanzo, Yehova anam’dalitsa Yakobo kuthupi. Ndipo tangoganizilani cimwemwe na ciyamikilo cimene Yakobo anali naco kwa Yehova, ataonananso na mwana wake Yosefe, amene anali kuganiza kuti anafa kale-kale! Ubwenzi wolimba na Yehova ni umene unam’thandiza Yakobo kupilila mavuto onsewo. (Gen. 30:43; 32:9, 10; 46:28-30) Nafenso tikakhala pa ubwenzi wathithithi na Yehova, tidzakwanitsa kupilila mavuto adzidzidzi. w23.04 15 ¶6-7
Cinayi, July 24
Yehova ndi Mʼbusa wanga. Sindidzasoŵa kanthu.—Sal. 23:1.
Salimo 23 ni nyimbo imene imafotokoza cidalilo cimene tili naco pa cikondi ca Yehova komanso mmene amatisamalila. Davide, amene analemba salimoli, anafotokoza ubwenzi wolimba umene unalipo pakati pa iye na M’busa wake, Yehova. Davide anadzimva kukhala wotetezeka polola Yehova kuti am’tsogolele, ndipo anali kumudalila na mtima wonse. Davide anali kudziŵa kuti Yehova adzamuonetsa cikondi masiku onse a moyo wake. N’cifukwa ciyani anali na cidalilo cacikulu conci? Davide anadzimva kuti ni wosamalidwa bwino cifukwa nthawi zonse Yehova anali kumupatsa zofunikila. Davide anasangalalanso na ubwenzi komanso ciyanjo ca Yehova. Ndiye cifukwa cake anali wotsimikiza kuti mulimonse mmene zinthu zidzakhalile m’tsogolo, Yehova adzapitilizabe kumusamalila pa zosoŵa zake. Cifukwa cakuti Davide anali kudziŵa kuti Yehova amamukonda komanso kuti adzamusamalila, zinamuthandiza kuti asakhale na nkhawa iliyonse pa mavuto ake. M’malo mwake anali wokhutila komanso wosangalala.—Sal. 16:11. w24.01 29 ¶12-13
Cisanu, July 25
Ine ndili limodzi ndi inu masiku onse mpaka mʼnyengo ya mapeto a nthawi ino.—Mat. 28:20.
Kucokela pa nkhondo yaciŵili ya padziko lonse, anthu a Yehova m’maiko ambili anapezako mtendele komanso ufulu pogwila nchito yolalikila. Ndipo nchitoyi yapita patsogolo kwambili. Masiku anonso, a m’Bungwe Lolamulila akupitiliza kuyang’ana kwa Khristu kaamba ka citsogozo. Amafuna kuti malangizo amene amapeleka kwa abale na alongo azikhala ogwilizana na cifunilo ca Mulungu. Ndipo amaseŵenzetsa oyang’anila madela, komanso akulu popeleka malangizo amenewa ku mipingo. Akulu odzodzedwa ali “m’dzanja . . . lamanja” la Khristu. (Chiv. 2:1) Akulu amenewa ni opanda ungwilo ndipo nthawi zina amalakwitsa. Mose, Yoswa, komanso atumwi anali kulakwitsa zinthu nthawi zina. (Num. 20:12; Yos. 9:14, 15; Aroma 3:23) Ngakhale n’telo, Khristu akutsogolela kapolo wokhulupilika, komanso akulu osankhidwa, ndipo adzapitiliza kukhala nawo. Cotelo, tili na zifukwa zomveka zokhalila na cidalilo m’citsogozo cimene Yesu akupeleka kupitila mwa awo amene anasankhidwa kuti azititsogolela. w24.02 23-24 ¶13-14
Ciŵelu, July 26
Muzitsanzila Mulungu, monga ana ake okondedwa.—Aef. 5:1.
Masiku ano, tingamukondweletse Yehova pokamba za iye mwaubwenzi, moyamikila, komanso mwacikondi. Tikakhala mu utumiki timakumbukila kuti colinga cathu cacikulu ni kukokela anthu kwa Yehova, na kuwathandiza kumuona monga Tate wacikondi mmene ifeyo timamuonela. (Yak. 4:8) Timakondwela kusonyeza anthu mmene Baibo imamufotokozela Yehova, mmene imaonetsela cikondi cake, cilungamo cake, nzelu zake, mphamvu zake, komanso makhalidwe ena abwino. Timatamandanso Yehova na kumukondweletsa pamene tiyesetsa kutengela citsanzo cake. Tikatelo, timakhala osiyana nawo anthu oipa a m’dzikoli. Anthu angaone kuti ndife osiyana nawo, ndipo angafune kudziŵa cifukwa cake. (Mat. 5:14-16) Pocita nawo zinthu za tsiku na tsiku, tingawafotokozele cifukwa cake timacita zinthu zina mosiyana. Zotsatila zake n’zakuti, timakokela anthu a mitima yabwino kwa Mulungu wathu. Tikamatamanda Yehova m’njila zimenezi, timakondweletsa mtima wake.—1 Tim. 2:3, 4. w24.02 10 ¶7
Sondo, July 27
[Muzitha] kulimbikitsa . . . ndiponso kudzudzula.—Tito 1:9.
Kuti mukhale Mkhristu wokhwima, muyenela kukulitsa maluso othandiza. Izi zidzakuthandizani kusenza maudindo mu mpingo, kupeza nchito yokuthandizani inuyo na banja lanu, komanso kukhala paubwenzi wabwino na anthu ena. Mwacitsanzo, phunzilani kuŵelenga na kulemba bwino. Baibo imati mwamuna wacimwemwe komanso wopambana amaseŵenzetsa nthawi yake kuŵelenga Mawu a Mulungu na kuwasinkhasinkha. (Sal. 1:1-3) Kuŵelenga Baibo tsiku lililonse kumam’thandiza kudziŵa bwino kaganizidwe ka Yehova, zimene zimamuthandiza kukhala woganiza bwino. (Miy. 1:3, 4) Abale na alongo athu amayang’ana kwa amuna oyenelela akafuna malangizo. Ngati mumatha kuŵelenga na kulemba, mudzakwanitsa kukonzekela nkhani na ndemanga zogwila mtima komanso zolimbikitsa cikhulupililo. Mudzakwanitsanso kulemba manotsi atanthauzo amenewa adzakuthandizani kulimbitsa cikhulupililo canu komanso kulimbikitsa ena. w23.12 26-27 ¶9-11
Mande, July 28
Amene ali wogwilizana ndi inu ndi wamkulu kuposa amene ali wogwilizana ndi dziko.—1 Yoh. 4:4.
Mukakhala na mantha, muzisinkhasinkha zimene Yehova adzacita m’tsogolo Satana akadzacotsedwapo. Msonkhano wa cigawo wa mu 2014 unali na citsanzo coonetsa tate akukambilana na banja lake mmene lemba la 2 Timoteyo 3:1-5 likanalembedwela cikanakhala kuti linali kulosela mmene Paradaiso adzakhalile. Analiŵelenga motele: “Masiku a m’dziko latsopano adzakhala nthawi yapadela komanso yosangalatsa. Pakuti anthu adzakhala okonda anzawo, okonda kulambila Mulungu, odzicepetsa, ofatsa, otamanda Mulungu, omvela makolo, oyamika, okhulupilika, okonda acibale awo, ofuna kugwilizana ndi anzawo, onena zabwino za anzawo, odziletsa, odekha, okonda zabwino, odalilika, oganizila ena, osadzitukumula, ndiponso osanyada, okonda Mulungu m’malo mokonda zosangalatsa, ndiponso odzipelekadi kwa Mulungu, anthu amenewa usasiyane nawo.” Kodi mumakambilana nawo a m’banja lanu kapena alambili anzanu za mmene umoyo udzakhalile m’dziko latsopano? w24.01 6 ¶13-14
Ciŵili, July 29
Umandisangalatsa kwambili.—Luka 3:22.
N’zolimbikitsa zedi kudziŵa kuti Yehova amakonda gulu lonse la anthu ake! Baibo imati: “Yehova amasangalala ndi anthu ake.” (Sal. 149:4) Komabe, nthawi zina ena amalefuka moti amafika podzifunsa kuti, ‘Kodi Yehova amakondwela nane?’ Ena mwa alambili okhulupilika a Yehova ochulidwa m’Baibo anavutikapo na maganizo otelo. (1 Sam. 1:6-10; Yobu 29:2, 4; Sal. 51:11) Baibo imakamba momveka bwino kuti anthu opanda ungwilo angapeze ciyanjo ca Yehova. Motani? Mwa kukhulupilila Yesu Khristu na kubatizika. (Yoh. 3:16) Mwa kutelo, timaonetsa poyela kuti tinalapa macimo athu, komanso kuti tinapanga lonjezo kwa Mulungu lakuti tidzacita cifunilo cake. (Mac. 2:38; 3:19) Yehova amakondwela ngati tapanga masitepe amenewa kuti tikhale naye pa ubale. Kuwonjezela apo, amakondwela nafe ngati tipitiliza kucita zonse zimene tingathe posunga lumbilo lathu la kudzipatulila. Ndipo amationa kukhala mabwenzi ake a pamtima.—Sal. 25:14. w24.03 26 ¶1-2
Citatu, July 30
Sitingasiye kulankhula za zinthu zimene tinaziona ndi kuzimva.—Mac. 4:20.
Tingatengele citsanzo ca ophunzila mwa kupitiliza kulalikila ngakhale pamene maboma atilamula kuti tileke kulalikila. Tili na cidalilo kuti Yehova adzatithandiza kukwanilitsa utumiki wathu. Conco mupemphani kuti akuthandizeni kukhala wolimba mtima, akupatseni nzelu komanso kuti akuthandizeni kuthana na mavuto. Ambili a ife tikulimbana na mavuto monga matenda, kupsinjika maganizo, kutaikilidwa wokondedwa wathu mu imfa, mavuto a m’banja, mazunzo, kapena vuto lina. Ndipo zinthu monga milili na nkhondo, zapangitsa kuti cikhale covuta kwambili kuthana na mavuto ngati amenewa. Conco, m’khuthulileni za kumtima kwanu Yehova. Muuzeni za vuto lanu mmene mungauzile bwenzi lanu lapamtima. Khalani wotsimikiza kuti Yehova “adzakuthandizani.” (Sal. 37:3, 5) Kulimbikila kupemphela kudzatithandiza ‘kupilila mavuto.’ (Aroma 12:12) Yehova amadziŵa mavuto amene atumiki ake amakumana nawo, “amamva kufuula kwawo kopempha thandizo.”—Sal. 145:18, 19. w23.05 5-6 ¶12-15
Cinayi, July 31
Nthawi zonse muzitsimikizila kuti covomelezeka kwa Ambuye nʼciti.—Aef. 5:10.
Tikafunika kupanga cisankho cofunika kwambili, tiyenela “kuzindikila cifunilo ca Yehova,” na kucita zinthu mogwilizana na cifuniloco. (Aef. 5:17) Tikamafufuza na kupeza mfundo za m’Baibo zothandiza pa cisankho cimene tifuna kupanga, kwenikweni timakhala tikufunafuna maganizo a Mulungu pa nkhaniyo. Ndipo tikagwilitsa nchito mfundo zake, timapanga zisankho zabwino. Mdani wathu Satana, “Woipayo,” amafuna kuticenjeneka na kufuna-funa zinthu za m’dzikoli n’colinga cakuti tizisoŵelatu nthawi yotumikila Mulungu. (1 Yoh. 5:19) Cingakhale capafupi kwa Mkhristu kutsogoza zakuthupi, maphunzilo, kapena nchito m’malo moseŵenzetsa mipata imene ilipo yotumikila Yehova. Zotelezi zikacitika, zingaonetse kuti munthu wayamba kuyendela maganizo a m’dzikoli. N’zoona kuti zinthu zimenezi si zoipa kwenikweni. Koma si ndiye zomwe tiyenela kutsogoza pa umoyo wathu. w24.03 24 ¶16-17