Ciŵelu, July 26
Muzitsanzila Mulungu, monga ana ake okondedwa.—Aef. 5:1.
Masiku ano, tingamukondweletse Yehova pokamba za iye mwaubwenzi, moyamikila, komanso mwacikondi. Tikakhala mu utumiki timakumbukila kuti colinga cathu cacikulu ni kukokela anthu kwa Yehova, na kuwathandiza kumuona monga Tate wacikondi mmene ifeyo timamuonela. (Yak. 4:8) Timakondwela kusonyeza anthu mmene Baibo imamufotokozela Yehova, mmene imaonetsela cikondi cake, cilungamo cake, nzelu zake, mphamvu zake, komanso makhalidwe ena abwino. Timatamandanso Yehova na kumukondweletsa pamene tiyesetsa kutengela citsanzo cake. Tikatelo, timakhala osiyana nawo anthu oipa a m’dzikoli. Anthu angaone kuti ndife osiyana nawo, ndipo angafune kudziŵa cifukwa cake. (Mat. 5:14-16) Pocita nawo zinthu za tsiku na tsiku, tingawafotokozele cifukwa cake timacita zinthu zina mosiyana. Zotsatila zake n’zakuti, timakokela anthu a mitima yabwino kwa Mulungu wathu. Tikamatamanda Yehova m’njila zimenezi, timakondweletsa mtima wake.—1 Tim. 2:3, 4. w24.02 10 ¶7
Sondo, July 27
[Muzitha] kulimbikitsa . . . ndiponso kudzudzula.—Tito 1:9.
Kuti mukhale Mkhristu wokhwima, muyenela kukulitsa maluso othandiza. Izi zidzakuthandizani kusenza maudindo mu mpingo, kupeza nchito yokuthandizani inuyo na banja lanu, komanso kukhala paubwenzi wabwino na anthu ena. Mwacitsanzo, phunzilani kuŵelenga na kulemba bwino. Baibo imati mwamuna wacimwemwe komanso wopambana amaseŵenzetsa nthawi yake kuŵelenga Mawu a Mulungu na kuwasinkhasinkha. (Sal. 1:1-3) Kuŵelenga Baibo tsiku lililonse kumam’thandiza kudziŵa bwino kaganizidwe ka Yehova, zimene zimamuthandiza kukhala woganiza bwino. (Miy. 1:3, 4) Abale na alongo athu amayang’ana kwa amuna oyenelela akafuna malangizo. Ngati mumatha kuŵelenga na kulemba, mudzakwanitsa kukonzekela nkhani na ndemanga zogwila mtima komanso zolimbikitsa cikhulupililo. Mudzakwanitsanso kulemba manotsi atanthauzo amenewa adzakuthandizani kulimbitsa cikhulupililo canu komanso kulimbikitsa ena. w23.12 26-27 ¶9-11
Mande, July 28
Amene ali wogwilizana ndi inu ndi wamkulu kuposa amene ali wogwilizana ndi dziko.—1 Yoh. 4:4.
Mukakhala na mantha, muzisinkhasinkha zimene Yehova adzacita m’tsogolo Satana akadzacotsedwapo. Msonkhano wa cigawo wa mu 2014 unali na citsanzo coonetsa tate akukambilana na banja lake mmene lemba la 2 Timoteyo 3:1-5 likanalembedwela cikanakhala kuti linali kulosela mmene Paradaiso adzakhalile. Analiŵelenga motele: “Masiku a m’dziko latsopano adzakhala nthawi yapadela komanso yosangalatsa. Pakuti anthu adzakhala okonda anzawo, okonda kulambila Mulungu, odzicepetsa, ofatsa, otamanda Mulungu, omvela makolo, oyamika, okhulupilika, okonda acibale awo, ofuna kugwilizana ndi anzawo, onena zabwino za anzawo, odziletsa, odekha, okonda zabwino, odalilika, oganizila ena, osadzitukumula, ndiponso osanyada, okonda Mulungu m’malo mokonda zosangalatsa, ndiponso odzipelekadi kwa Mulungu, anthu amenewa usasiyane nawo.” Kodi mumakambilana nawo a m’banja lanu kapena alambili anzanu za mmene umoyo udzakhalile m’dziko latsopano? w24.01 6 ¶13-14