LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
Tulukani
Loŵani
LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Takulandilani
Ici ni cida cofufuzila m'mabuku olembewa na Mboni za Yehova mu vitundu volekana-lekana.
Ngati mufuna kucita daunilodi, yendani pa jw.org.
  • Lelo

Sondo, August 10

Mnzako weniweni amakusonyeza cikondi nthawi zonse, ndipo ndi mʼbale amene anabadwa kuti akuthandize pakagwa mavuto.​—Miy. 17:17.

Pamene Akhristu ku Yudeya anali pa njala yadzaoneni. Abale mu mpingo wa ku Antiokeya “anatsimikiza mtima kutumiza thandizo kwa abale a ku Yudeya, aliyense mogwilizana ndi zimene akanakwanitsa.” (Mac. 11:27-30) Ngakhale kuti okhudzidwa na njala anali kukhala kutali kwambili na ku Antiyokeya, Akhristu a ku Antiyokeya anapelekabe thandizo kwa abale awo. (1 Yoh. 3:17, 18) Nafenso tingawacitile cifundo alambili anzathu tikamva kuti tsoka lawagwela. Timacitapo kanthu mwamsanga, mwina mwa kufunsa akulu ngati tingadzipeleke kukathandizila. Cina, timapanga zopeleka pa nchito ya padziko lonse, kapena timapemphelela omwe akumana na tsokalo. Abale na alongo athu angadzafunikile thandizo kuti apeze zofunikila pa umoyo. Mfumu yathu Khristu Yesu akadzabwela kudzaweluza anthu, tikufuna adzatipeze tikuonetsa cifundo, na kutiuza kuti “lowani mu Ufumu.”​—Mat. 25:34-40. w23.07 4 ¶9-10; 6 ¶12

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025

Mande, August 11

Anthu onse adziŵe kuti ndinu ololela.​—Afil. 4:5.

Yesu anatengela citsanzo ca Yehova ca kulolela. Iye anatumidwa padziko lapansi kudzalalikila “kwa nkhosa zotayika za nyumba ya Isiraeli.” Koma anaonetsa kulolela pocita utumiki wakewo. Panthawi ina, mayi wina amene sanali Mwisiraeli anam’condelela kuti acilitse mwana wake wamkazi, amene anali ‘atagwidwa ndi ciwanda mocititsa mantha.’ Mwacifundo, Yesu anacita zimene mayiyo anam’pempha ndipo anam’cilitsa mwanayo. (Mat. 15:21-28) Naci citsanzo cina. Ca kumayambililo kwa utumiki wake, Yesu ananena kuti: “Aliyense amene adzandikane . . . , inenso ndidzamukana.” (Mat. 10:33) Iye anakanidwa katatu na Petulo. Koma kodi Yesu anam’kana Petulo? Ayi. Yesu anaona kulapa na cikhulupililo ca Petulo. Pambuyo poukitsidwa, Yesu anaonekela kwa Petulo. Ndipo mwacionekele, anam’tsimikizila kuti anam’khululukila komanso kuti anali kum’kondabe. (Luka 24:33, 34) Yehova Mulungu na Yesu Khristu ni ololela. Nanga bwanji ife? Yehova amafuna kuti nafenso tikhale ololela. w23.07 21 ¶6-7

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025

Ciŵili, August 12

Imfa sidzakhalaponso.​—Chiv. 21:4.

Kodi ni zitsimikizo ziti zimene tingauzeko aja amene amakaikila zakuti lonjezo la Mulungu la Paradaiso lidzakwanilitsidwa? Coyamba, Yehova iye mwini ndiye anapeleka lonjezolo. Buku la Chivumbulutso limati: “Wokhala pampando wacifumu anati: ‘Taonani! Ndikupanga zinthu zonse kukhala zatsopano.’” Iye ali na nzelu, mphamvu, komanso cifuno cokwanilitsa lonjezo lake limeneli. Caciŵili, kukwanilitsidwa kwa lonjezo limeneli ni kodalilika, moti malinga na kaonedwe ka Yehova, kwa iye zili ngati zakwanilitsika kale. Ndiye cifukwa cake anati: “Mawu awa ndi odalilika ndi oona. . . . Zakwanilitsidwa!” Cacitatu, Yehova akayamba kucita cina cake, amacicitabe mpaka atacikwanilitsa, ndiye cifukwa cake anati: “Ine ndine Alefa ndi Omega.” (Chiv. 21:6) Yehova adzaonetsa poyela kuti Satana ni wabodza komanso wolephela. Conco, wina akadzanena kuti, “N’zosatheka kucitika,” mukaŵelenge na kumufotokozela Chivumbulutso 21:5, 6. Muonetseni mmene Yehova watsimikizila lonjezo lake limeneli mwa kulisainila iye mwini, titelo kunena kwake.​—Yes. 65:16. w23.11 7 ¶18-19

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025
Takulandilani
Ici ni cida cofufuzila m'mabuku olembewa na Mboni za Yehova mu vitundu volekana-lekana.
Ngati mufuna kucita daunilodi, yendani pa jw.org.
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani