LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
Tulukani
Loŵani
LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Takulandilani
Ici ni cida cofufuzila m'mabuku olembewa na Mboni za Yehova mu vitundu volekana-lekana.
Ngati mufuna kucita daunilodi, yendani pa jw.org.
  • Lelo

Mande, August 11

Anthu onse adziŵe kuti ndinu ololela.​—Afil. 4:5.

Yesu anatengela citsanzo ca Yehova ca kulolela. Iye anatumidwa padziko lapansi kudzalalikila “kwa nkhosa zotayika za nyumba ya Isiraeli.” Koma anaonetsa kulolela pocita utumiki wakewo. Panthawi ina, mayi wina amene sanali Mwisiraeli anam’condelela kuti acilitse mwana wake wamkazi, amene anali ‘atagwidwa ndi ciwanda mocititsa mantha.’ Mwacifundo, Yesu anacita zimene mayiyo anam’pempha ndipo anam’cilitsa mwanayo. (Mat. 15:21-28) Naci citsanzo cina. Ca kumayambililo kwa utumiki wake, Yesu ananena kuti: “Aliyense amene adzandikane . . . , inenso ndidzamukana.” (Mat. 10:33) Iye anakanidwa katatu na Petulo. Koma kodi Yesu anam’kana Petulo? Ayi. Yesu anaona kulapa na cikhulupililo ca Petulo. Pambuyo poukitsidwa, Yesu anaonekela kwa Petulo. Ndipo mwacionekele, anam’tsimikizila kuti anam’khululukila komanso kuti anali kum’kondabe. (Luka 24:33, 34) Yehova Mulungu na Yesu Khristu ni ololela. Nanga bwanji ife? Yehova amafuna kuti nafenso tikhale ololela. w23.07 21 ¶6-7

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025

Ciŵili, August 12

Imfa sidzakhalaponso.​—Chiv. 21:4.

Kodi ni zitsimikizo ziti zimene tingauzeko aja amene amakaikila zakuti lonjezo la Mulungu la Paradaiso lidzakwanilitsidwa? Coyamba, Yehova iye mwini ndiye anapeleka lonjezolo. Buku la Chivumbulutso limati: “Wokhala pampando wacifumu anati: ‘Taonani! Ndikupanga zinthu zonse kukhala zatsopano.’” Iye ali na nzelu, mphamvu, komanso cifuno cokwanilitsa lonjezo lake limeneli. Caciŵili, kukwanilitsidwa kwa lonjezo limeneli ni kodalilika, moti malinga na kaonedwe ka Yehova, kwa iye zili ngati zakwanilitsika kale. Ndiye cifukwa cake anati: “Mawu awa ndi odalilika ndi oona. . . . Zakwanilitsidwa!” Cacitatu, Yehova akayamba kucita cina cake, amacicitabe mpaka atacikwanilitsa, ndiye cifukwa cake anati: “Ine ndine Alefa ndi Omega.” (Chiv. 21:6) Yehova adzaonetsa poyela kuti Satana ni wabodza komanso wolephela. Conco, wina akadzanena kuti, “N’zosatheka kucitika,” mukaŵelenge na kumufotokozela Chivumbulutso 21:5, 6. Muonetseni mmene Yehova watsimikizila lonjezo lake limeneli mwa kulisainila iye mwini, titelo kunena kwake.​—Yes. 65:16. w23.11 7 ¶18-19

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025

Citatu, August 13

Ndidzakupangitsa kuti ukhale mtundu waukulu.​—Gen. 12:2.

Yehova ananena lonjezo limeneli kwa Abulahamu amene anali na zaka 75 ndipo analibe mwana. Kodi Abulahamu anaona kukwanilitsidwa kwa lonjezo limeneli? Osati kwathunthu. Atawoloka Mtsinje wa Firate, anayembekezela zaka 25 kuti mozizwitsa akhale na mwana Isaki. Ndipo anayembekezelanso zaka zina 60 kuti adzukulu ake Esau na Yakobo abadwe. (Aheb. 6:15) Koma Abulahamu sanaone mbadwa zake zikukhala mtundu waukulu na kulandila Dziko Lolonjezedwa. Ngakhale n’telo, munthu wokhulupilika ameneyu anali pa ubwenzi wolimba na Mlengi wake. (Yak. 2:23) Abulahamu akadzaukitsidwa, adzakondwela kwambili kudziŵa kuti cikhulupililo na kuleza mtima kwake zinabweletsa madalitso ku mtundu wonse wa anthu. (Gen. 22:18) Kodi tiphunzilapo ciyani? Si malonjezo onse a Yehova amene adzakwanilitsidwa ife tili moyo. Komabe, tikaleza mtima monga Abulahamu, tidzakhala otsimikiza kuti Yehova adzatifupa pali pano, komanso m’dziko latsopano tidzalandila madalitso oculuka.​—Maliko 10:29, 30. w23.08 24 ¶14

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025
Takulandilani
Ici ni cida cofufuzila m'mabuku olembewa na Mboni za Yehova mu vitundu volekana-lekana.
Ngati mufuna kucita daunilodi, yendani pa jw.org.
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani