Ciŵili, August 12
Imfa sidzakhalaponso.—Chiv. 21:4.
Kodi ni zitsimikizo ziti zimene tingauzeko aja amene amakaikila zakuti lonjezo la Mulungu la Paradaiso lidzakwanilitsidwa? Coyamba, Yehova iye mwini ndiye anapeleka lonjezolo. Buku la Chivumbulutso limati: “Wokhala pampando wacifumu anati: ‘Taonani! Ndikupanga zinthu zonse kukhala zatsopano.’” Iye ali na nzelu, mphamvu, komanso cifuno cokwanilitsa lonjezo lake limeneli. Caciŵili, kukwanilitsidwa kwa lonjezo limeneli ni kodalilika, moti malinga na kaonedwe ka Yehova, kwa iye zili ngati zakwanilitsika kale. Ndiye cifukwa cake anati: “Mawu awa ndi odalilika ndi oona. . . . Zakwanilitsidwa!” Cacitatu, Yehova akayamba kucita cina cake, amacicitabe mpaka atacikwanilitsa, ndiye cifukwa cake anati: “Ine ndine Alefa ndi Omega.” (Chiv. 21:6) Yehova adzaonetsa poyela kuti Satana ni wabodza komanso wolephela. Conco, wina akadzanena kuti, “N’zosatheka kucitika,” mukaŵelenge na kumufotokozela Chivumbulutso 21:5, 6. Muonetseni mmene Yehova watsimikizila lonjezo lake limeneli mwa kulisainila iye mwini, titelo kunena kwake.—Yes. 65:16. w23.11 7 ¶18-19
Citatu, August 13
Ndidzakupangitsa kuti ukhale mtundu waukulu.—Gen. 12:2.
Yehova ananena lonjezo limeneli kwa Abulahamu amene anali na zaka 75 ndipo analibe mwana. Kodi Abulahamu anaona kukwanilitsidwa kwa lonjezo limeneli? Osati kwathunthu. Atawoloka Mtsinje wa Firate, anayembekezela zaka 25 kuti mozizwitsa akhale na mwana Isaki. Ndipo anayembekezelanso zaka zina 60 kuti adzukulu ake Esau na Yakobo abadwe. (Aheb. 6:15) Koma Abulahamu sanaone mbadwa zake zikukhala mtundu waukulu na kulandila Dziko Lolonjezedwa. Ngakhale n’telo, munthu wokhulupilika ameneyu anali pa ubwenzi wolimba na Mlengi wake. (Yak. 2:23) Abulahamu akadzaukitsidwa, adzakondwela kwambili kudziŵa kuti cikhulupililo na kuleza mtima kwake zinabweletsa madalitso ku mtundu wonse wa anthu. (Gen. 22:18) Kodi tiphunzilapo ciyani? Si malonjezo onse a Yehova amene adzakwanilitsidwa ife tili moyo. Komabe, tikaleza mtima monga Abulahamu, tidzakhala otsimikiza kuti Yehova adzatifupa pali pano, komanso m’dziko latsopano tidzalandila madalitso oculuka.—Maliko 10:29, 30. w23.08 24 ¶14
Cinayi, August 14
Pa nthawi imene iye ankafunafuna Yehova, Mulungu woonayo anacititsa kuti zinthu zizimuyendela bwino.—2 Mbiri 26:5.
Ali wacicepele, Mfumu Uziya anali wodzicepetsa. Iye anaphunzila ‘kuopa Mulungu woona.’ Uziya anakhala na moyo kwa zaka 68, ndipo kwa zaka zambili pa umoyo wake Yehova anamudalitsa. (2 Mbiri 26:1-4) Uziya anagonjetsa adani ambili a Yuda, ndipo anakhwimitsa citetezo ca Yerusalemu. (2 Mbiri 26:6-15) Mosakaika, Uziya anakondwela ngako cifukwa ca zimene Mulungu anam’thandiza kucita. (Mlal. 3:12, 13) Mfumu Uziya anali atazoloŵela kuuza ena zoyenela kucita. N’kutheka kuti izi zinam’pangitsa kuona kuti angacite ciliconse cimene afuna. Tsiku lina, Uziya analoŵa m’kacisi wa Yehova, ndipo modzikuza anayamba kufukiza nsembe, cinthu cimene mafumu sanali kuloledwa kucita. (2 Mbiri 26:16-18) Mkulu wa Ansembe Azariya anayesa kumuwongolela, koma Uziya anakwiya zedi. N’zacisoni kuti Uziya anawononga mbili yake yokhulupilika, ndipo anakanthidwa na khate. (2 Mbiri 26:19-21) Akanakhalabe wodzicepetsa, moyo wake ukanakhala wabwino ngako! w23.09 10 ¶9-10