Citatu, August 13
Ndidzakupangitsa kuti ukhale mtundu waukulu.—Gen. 12:2.
Yehova ananena lonjezo limeneli kwa Abulahamu amene anali na zaka 75 ndipo analibe mwana. Kodi Abulahamu anaona kukwanilitsidwa kwa lonjezo limeneli? Osati kwathunthu. Atawoloka Mtsinje wa Firate, anayembekezela zaka 25 kuti mozizwitsa akhale na mwana Isaki. Ndipo anayembekezelanso zaka zina 60 kuti adzukulu ake Esau na Yakobo abadwe. (Aheb. 6:15) Koma Abulahamu sanaone mbadwa zake zikukhala mtundu waukulu na kulandila Dziko Lolonjezedwa. Ngakhale n’telo, munthu wokhulupilika ameneyu anali pa ubwenzi wolimba na Mlengi wake. (Yak. 2:23) Abulahamu akadzaukitsidwa, adzakondwela kwambili kudziŵa kuti cikhulupililo na kuleza mtima kwake zinabweletsa madalitso ku mtundu wonse wa anthu. (Gen. 22:18) Kodi tiphunzilapo ciyani? Si malonjezo onse a Yehova amene adzakwanilitsidwa ife tili moyo. Komabe, tikaleza mtima monga Abulahamu, tidzakhala otsimikiza kuti Yehova adzatifupa pali pano, komanso m’dziko latsopano tidzalandila madalitso oculuka.—Maliko 10:29, 30. w23.08 24 ¶14
Cinayi, August 14
Pa nthawi imene iye ankafunafuna Yehova, Mulungu woonayo anacititsa kuti zinthu zizimuyendela bwino.—2 Mbiri 26:5.
Ali wacicepele, Mfumu Uziya anali wodzicepetsa. Iye anaphunzila ‘kuopa Mulungu woona.’ Uziya anakhala na moyo kwa zaka 68, ndipo kwa zaka zambili pa umoyo wake Yehova anamudalitsa. (2 Mbiri 26:1-4) Uziya anagonjetsa adani ambili a Yuda, ndipo anakhwimitsa citetezo ca Yerusalemu. (2 Mbiri 26:6-15) Mosakaika, Uziya anakondwela ngako cifukwa ca zimene Mulungu anam’thandiza kucita. (Mlal. 3:12, 13) Mfumu Uziya anali atazoloŵela kuuza ena zoyenela kucita. N’kutheka kuti izi zinam’pangitsa kuona kuti angacite ciliconse cimene afuna. Tsiku lina, Uziya analoŵa m’kacisi wa Yehova, ndipo modzikuza anayamba kufukiza nsembe, cinthu cimene mafumu sanali kuloledwa kucita. (2 Mbiri 26:16-18) Mkulu wa Ansembe Azariya anayesa kumuwongolela, koma Uziya anakwiya zedi. N’zacisoni kuti Uziya anawononga mbili yake yokhulupilika, ndipo anakanthidwa na khate. (2 Mbiri 26:19-21) Akanakhalabe wodzicepetsa, moyo wake ukanakhala wabwino ngako! w23.09 10 ¶9-10
Cisanu, August 15
Iye . . . anadzipatula, cifukwa ankaopa anthu odulidwawo.—Agal. 2:12.
Ngakhale pambuyo pokhala Mkhristu wodzozedwa, mtumwi Petulo anali kulimbanabe na zifooko zake. Mu 36 C.E, Petulo anaona kamaso pamene Koneliyo, munthu wosadulidwa, anadzozedwa na mzimu woyela. Uwu unali umboni woonekelatu wakuti “Mulungu alibe tsankho,” komanso kuti anthu amitundu ina angakhale mu mpingo wacikhristu. (Mac. 10:34, 44, 45) Pambuyo pa izi, Petulo anali womasuka kudyela pamodzi na anthu a mitundu ina, zimene kumbuyoku sakanacita. Komabe, Akhristu ena aciyuda anali kuona kuti Ayuda na anthu amitundu ina sayenela kudyela pamodzi. Ayuda ena atafika ku Antiokeya, Petulo analeka kudya na Akhristu a mitundu ina, mwina poopa kukhumudwitsa Akhristu aciyuda. Mtumwi Paulo anaona kuti cimeneco n’cinyengo. Conco, anam’dzudzula pamaso pa anthu. (Agal. 2:13, 14) Ngakhale kuti Petulo anaphonyetsanso, sanabwelele m’mbuyo. w23.09 22 ¶8