LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
Tulukani
Loŵani
LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Takulandilani
Ici ni cida cofufuzila m'mabuku olembewa na Mboni za Yehova mu vitundu volekana-lekana.
Ngati mufuna kucita daunilodi, yendani pa jw.org.
  • Lelo

Cinayi, August 14

Pa nthawi imene iye ankafunafuna Yehova, Mulungu woonayo anacititsa kuti zinthu zizimuyendela bwino.​—2 Mbiri 26:5.

Ali wacicepele, Mfumu Uziya anali wodzicepetsa. Iye anaphunzila ‘kuopa Mulungu woona.’ Uziya anakhala na moyo kwa zaka 68, ndipo kwa zaka zambili pa umoyo wake Yehova anamudalitsa. (2 Mbiri 26:1-4) Uziya anagonjetsa adani ambili a Yuda, ndipo anakhwimitsa citetezo ca Yerusalemu. (2 Mbiri 26:6-15) Mosakaika, Uziya anakondwela ngako cifukwa ca zimene Mulungu anam’thandiza kucita. (Mlal. 3:12, 13) Mfumu Uziya anali atazoloŵela kuuza ena zoyenela kucita. N’kutheka kuti izi zinam’pangitsa kuona kuti angacite ciliconse cimene afuna. Tsiku lina, Uziya analoŵa m’kacisi wa Yehova, ndipo modzikuza anayamba kufukiza nsembe, cinthu cimene mafumu sanali kuloledwa kucita. (2 Mbiri 26:16-18) Mkulu wa Ansembe Azariya anayesa kumuwongolela, koma Uziya anakwiya zedi. N’zacisoni kuti Uziya anawononga mbili yake yokhulupilika, ndipo anakanthidwa na khate. (2 Mbiri 26:19-21) Akanakhalabe wodzicepetsa, moyo wake ukanakhala wabwino ngako! w23.09 10 ¶9-10

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025

Cisanu, August 15

Iye . . . anadzipatula, cifukwa ankaopa anthu odulidwawo.​—Agal. 2:12.

Ngakhale pambuyo pokhala Mkhristu wodzozedwa, mtumwi Petulo anali kulimbanabe na zifooko zake. Mu 36 C.E, Petulo anaona kamaso pamene Koneliyo, munthu wosadulidwa, anadzozedwa na mzimu woyela. Uwu unali umboni woonekelatu wakuti “Mulungu alibe tsankho,” komanso kuti anthu amitundu ina angakhale mu mpingo wacikhristu. (Mac. 10:34, 44, 45) Pambuyo pa izi, Petulo anali womasuka kudyela pamodzi na anthu a mitundu ina, zimene kumbuyoku sakanacita. Komabe, Akhristu ena aciyuda anali kuona kuti Ayuda na anthu amitundu ina sayenela kudyela pamodzi. Ayuda ena atafika ku Antiokeya, Petulo analeka kudya na Akhristu a mitundu ina, mwina poopa kukhumudwitsa Akhristu aciyuda. Mtumwi Paulo anaona kuti cimeneco n’cinyengo. Conco, anam’dzudzula pamaso pa anthu. (Agal. 2:13, 14) Ngakhale kuti Petulo anaphonyetsanso, sanabwelele m’mbuyo. w23.09 22 ¶8

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025

Ciŵelu, August 16

Adzakulimbitsani.​—1 Pet. 5:10.

Kudziunika moona mtima kungakuthandizeni kuti muone pamene muyenela kuongolela, koma musalefuke. “Ambuye ndi wokoma mtima,” ndipo adzakuthandizani kuti muongolele. (1 Pet. 2:3) Mtumwi Petulo anatitsimikizila kuti “Mulungu . . . adzamalizitsa kukuphunzitsani. Adzakulimbitsani.” Panthawi ina, Petulo anaziona wosayenela kukhala pamodzi na Mwana wa Mulungu. (Luka 5:8) Koma cifukwa ca thandizo la Yehova komanso la Yesu, anakwanitsa kutsatila Khristu mokhulupilika. Zotsatila zake zinali zakuti Yehova ‘anam’tsegulila khomo kuti aloŵe mwaulemelelo mu ufumu wosatha wa Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu.’ (2 Pet. 1:11) Mphoto yosangalatsa zedi! Ngati mwaikilapo mtima mmene Petulo anacitila komanso kulola Yehova kuti akuphunzitseni, inunso mudzalandila mphoto ya moyo wosatha. Ndipo “cikhulupililo canu cidzacititsa kuti miyoyo yanu ipulumuke.”​—1 Pet. 1:9. w23.09 31 ¶16-17

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025
Takulandilani
Ici ni cida cofufuzila m'mabuku olembewa na Mboni za Yehova mu vitundu volekana-lekana.
Ngati mufuna kucita daunilodi, yendani pa jw.org.
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani