LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
Tulukani
Loŵani
LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Takulandilani
Ici ni cida cofufuzila m'mabuku olembewa na Mboni za Yehova mu vitundu volekana-lekana.
Ngati mufuna kucita daunilodi, yendani pa jw.org.
Cilengezo
Taikaponso citundu cina: Shan
  • Lelo

Ciŵili, August 26

Onse amene amacita zinthu mopupuluma amasauka.​—Miy. 21:5.

Kuleza mtima kumatithandiza pocita zinthu na anthu ena. Kumatithandiza kumvetsela modekha ena akamalankhula. (Yak. 1:19) Kuleza mtima kumalimbikitsanso mtendele. Kumatiteteza kuti tisacite zinthu mopupuluma, na kukamba zinthu zosayenela tikapanikizika maganizo. Ndipo tikakhala oleza mtima, sitidzakwiya msanga wina akatikhumudwitsa. M’malo mobwezela, ‘tidzapitiliza kulolelana na kukhululukilana ndi mtima wonse.’ (Akol. 3:12, 13) Kuleza mtima kungatithandizenso kupanga zisankho zabwino. M’malo modya mfulumila, tidzapatula nthawi yofufuza na kusanthula zisankhozo kuti tione zimene zili zabwino koposa. Mwacitsanzo, tikamafuna-funa nchito, tingafulumile kuvomela nchito iliyonse imene yapezeka. Komabe, tikakhala oleza mtima, tidzakhala pansi na kuganizila mmene idzakhudzila banja lathu na umoyo wathu wauzimu. Tikakhala oleza mtima, tidzapewa kupanga zisankho zoipa. w23.08 22 ¶8-9

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025

Citatu, August 27

Ndimaona lamulo lina mʼthupi langa likumenyana ndi malamulo amʼmaganizo mwanga nʼkundicititsa kukhala kapolo wa lamulo la ucimo limene lili mʼthupi langa.​—Aroma 7:23.

Ngati mungalefuke poona kuti mumakhala na zilakolako zoipa, kuganizila lonjezo limene munapeleka kwa Yehova podzipatulila kudzakuthandizani kutsimikiza mtima kugonjetsa mayeselo. Ndipo zoona zake n’zakuti lumbilo lanu la kudzipatulila lidzakuthandizani kugonjetsa mayeselo. Motani? Mukadzipatulila kwa Yehova mumadzikana nokha. Izi zikutanthauza kunena kuti toto ku zikhumbo zanu, na zolinga zanu zimene sizingakondweletse Yehova. (Mat. 16:24) Conco, mukakumana na mayeso simudzacedwa na kuganizilapo zimene muyenela kucita. Mudzakhala mutadziwilatu zocita, zomwe ni kukhalabe wokhulupilika kwa Yehova. Mudzakhalabe wosasunthika pa kukondweletsa Yehova. Mudzakhala ngati Yobu amene ngakhale pambuyo pokumana na mavuto aakulu ananena motsimikiza kuti: “Sindidzasiya kukhala wokhulupilika.”​—Yobu 27:5. w24.03 9 ¶6-7

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025

Cinayi, August 28

Yehova ali pafupi ndi onse amene amamuitana, onse amene amamuitana mʼcoonadi.​—Sal. 145:18.

Yehova, “Mulungu amene ndi wacikondi,” ali nafe! (2 Akor. 13:11) Iye amationetsa cidwi aliyense payekha-payekha. Ndife otsimikiza kuti ndife ‘otetezeka ndi cikondi Cake cokhulupilika.’ (Sal. 32:10) Tikapitiliza kusinkhasinkha za mmene iye waonetsela cikondi cake pa ife, m’pamene iyenso amakhala weniweni kwa ife. Ndipo timamva kuti tikuyandikana naye. Tingamufikile momasuka na kumuuza kufunika kwa cikondi cake kwa ife. Tingamufotokozele nkhawa zathu zonse tili na cidalilo kuti amatimvetsa, komanso kuti ni wofunitsitsa kutithandiza. (Sal. 145:19) Monga mmene timafunila moto kukazizila, tifunikilanso cikondi ca Yehova. Ngakhale kuti cikondi ca Yehova n’camphamvu, cimapelekedwa mokoma mtima. Conco muzikhala wosangalala podziŵa kuti Yehova amakukondani kwambili. Ndipo tonsefe tiyeni tinene mofuula za cikondi cake kuti: “Ndimakonda Yehova”!​—Sal. 116:1. w24.01 31 ¶19-20

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025
Takulandilani
Ici ni cida cofufuzila m'mabuku olembewa na Mboni za Yehova mu vitundu volekana-lekana.
Ngati mufuna kucita daunilodi, yendani pa jw.org.
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani