Citatu, September 10
Ngakhale nditacita mokakamizika, ndinebe woyangʼanila mogwilizana ndi udindo umene ndinapatsidwa.—1 Akor. 9:17.
Nanga bwanji ngati mwaona kuti mapemphelo anu komanso utumiki wanu zikungocitika mwa mwambo cabe? Ngati zaconco zakucitikilani pambuyo pa ubatizo, musaganize kuti basi mzimu wa Yehova wakucokelani. Ndinu wopanda ungwilo, ndipo nthawi zina mungamamve conco. Ngati cangu canu cayamba kucepa, muzisinkhasinkha citsanzo ca mtumwi Paulo. Ngakhale kuti anali kuyesetsa kutengela citsanzo ca Yesu, iye anadziŵa kuti nthawi zina sangakhale na cikhumbo cofuna kucita zimenezo. Paulo anali wotsimikiza mtima kukwanilitsa utumiki wake mosasamala kanthu za mmene anali kumvela pa nthawiyo. Mofananamo, musadalile maganizo anu opanda ungwilo popanga zisankho. Khalani otsimikiza kucita zoyenela mosasamala kanthu za mmene mukumvela.—1 Akor. 9:16. w24.03 11-12 ¶12-13
Cinayi, September 11
Asonyezeni kuti mumawakonda.—2 Akor. 8:24.
Tingawaonetse cikondi abale na alongo athu pokhala nawo pa ubwenzi. (2 Akor. 6:11-13) Ambili tili m’mipingo muli abale na alongo a zikhalidwe zosiyana-siyana, komanso zibadwa zosiyana-siyana. Tingakulitse cikondi cathu kwa onsewo mwa kuyang’ana kwambili pa makhalidwe awo abwino. Tikamaona ena mmene Yehova amawaonela, timaonetsa kuti timawakonda. Pa cisautso cacikulu, cikondi cidzakhala cofunika kwambili. Kodi n’kuti kumene tidzapeza citetezo cisautsoco cikadzayamba? Onani malangizo amene Yehova anauza atumiki ake Babulo wakale ataukilidwa. Iye anawauza kuti: “Inu anthu anga, pitani mukaloŵe m’zipinda zanu zamkati ndipo mukatseke zitseko. Mukabisale kwa kanthawi mpaka mkwiyo utadutsa.” (Yes. 26:20) Zioneka kuti malangizo amenewa adzagwilanso nchito kwa ife pa cisautso cacikulu. w23.07 6-7 ¶14-16
Cisanu, September 12
Zocitika zapadzikoli zikusintha.—1 Akor. 7:31.
Dzifunseni kuti: ‘Kodi anthu amanidziŵa kuti ndine munthu wololela? Kapena amanidziŵa kuti ndine woumitsa zinthu, wokhwimitsa zinthu, kapena wa zimene ndanena-ndanena? Kodi nimamvako za ena na kulolela kuti zinthu zicitike mmene iwo afunila ngati n’kotheka?’ Tikamaonetsa kwambili kulolela, timaonetsanso kuti tikutengela kwambili Yehova na Yesu. Munthu wololela amakhala wokonzeka kusintha pamene mikhalidwe yasintha. Zinthu zikasintha, tingakumane na mavuto amene sitinawayembekezele. Mwacitsanzo, tingadwale mwadzidzidzi. Mwina kusintha mosayembekezela kwa zacuma kapena zandale, kungapangitse umoyo wathu kukhala wovuta kwadzaoneni. (Mlal. 9:11) Ngakhale kusinthidwa pa udindo, utumiki, kapena malo otumikilako kungatiike pa mayeso. Tikhoza kusintha mogwilizana na mikhalidwe yathu yatsopano ngati tatsatila masitepe anayi otsatilawa: (1) civomelezeni kuti zinthu zasintha, (2) yang’anani kutsogolo, (3) muziika maganizo anu pa zinthu zolimbikitsa, komanso (4) muzithandiza ena. w23.07 21-22 ¶7-8