Ciŵelu, September 13
Ndiwe munthu wokondedwa kwambili.—Dan. 9:23.
Mneneli Danieli anali wacinyamata pamene Ababulo anam’tengela kutali na kwawo monga mkaidi. Koma Ababulowo anacita naye cidwi Danieli. Iwo anaona kuti iye ‘analibe cilema ciliconse, anali wooneka bwino,’ komanso kuti anacokela m’banja lolemekezeka. (1 Sam. 16:7) Pa zifukwa zimenezi, Ababulowo anam’phunzitsa kuti akatumikile m’nyumba yacifumu. (Dan. 1:3, 4, 6) Yehova anali kum’konda Danieli, cifukwa ca khalidwe lake labwino. Ndipo Danieli ayenela kuti anali na zaka za m’ma 20 pamene Yehova anam’chula kuti wolungama pamodzi na Nowa komanso Yobu—amuna amene anapanga mbili yabwino na Mulungu kwa zaka zambili. (Gen. 5:32; 6:9, 10; Yobu 42:16, 17; Ezek. 14:14) Yehova sanaleke kum’konda Danieli pa umoyo wake wonse.—Dan. 10:11, 19. w23.08 2 ¶1-2
Sondo, September 14
Muthe kumvetsa bwino m’lifupi ndi m’litali, kukwela ndi kuzama kwa coonadi.—Aef. 3:18.
Mukafuna kugula nyumba mungafune kudzionela nokha nyumbayo, kuizungulila na kuona milingo yake yonse. Tiyenela kucita cimodzi-modzi poŵelenga na kuphunzila Baibo. Mukamaŵelenga mothamanga, mungadziŵe mfundo zocepa cabe—“mfundo zoyambilila za m’mawu opatulika a Mulungu.” (Aheb. 5:12) M’malo mwake, monga mmene mungacitile na nyumba, “fufuzani” kuti mumvetse mfundo zamtengo wapatali. Njila yabwino koposa yoŵelengela mawu a Mulungu ni kuyesa kuona mmene mfundo zosiyana-siyana zikugwilizanila. Muziyesetsa kumvetsa zimene mumakhulupilila komanso cifukwa cake mumazikhulupilila. Kuti timvetse Mawu a Mulungu, tiyenela kuŵelenga mfundo zozama za coonadi. Mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu anzake kuti ayenela kuŵelenga Mawu a Mulungu mwakhama ‘kuti athe kudziŵa bwino m’lifupi ndi m’litali ndi kukwela ndi kuzama’ kwa coonadi. Kucita zimenezi kunawathandiza ‘kuti azike mizu mokhazikika’ pa cikhulupililo. (Aef. 3:14-19) Ifenso tiyenela kucita cimodzi-modzi. w23.10 18 ¶1-3
Mande, September 15
Abale, pa nkhani ya kumva zowawa ndi kuleza mtima, tengelani citsanzo ca aneneli amene analankhula mʼdzina la Yehova.—Yak. 5:10.
M’Baibo, muli zitsanzo zambili za anthu amene anali oleza mtima. Conco, mungadziikile colinga coŵelenga zitsanzo zimenezo pa phunzilo la inu mwini. Mwacitsanzo, ngakhale kuti Davide anadzozedwa akali wacicepele kukhala mfumu yam’tsogolo ya Isiraeli, anayembekezela kwa zaka zambili kuti ayambe kulamulila. Nayenso Simiyoni komanso Anna anatumikila Yehova mokhulupilika poyembekezela Mesiya wolonjezedwayo. (Luka 2:25, 36-38) Mukamaŵelenga nkhani ngati zimenezi, muziyesa kupeza mayankho pa mafunso awa: N’ciyani cinathandiza munthu ameneyu kukhala woleza mtima? Kodi kuleza mtima kunam’pindulila motani? Nanga ningatengele bwanji citsanzo cake? Tingatengenso cenjezo pa zitsanzo za anthu amene sanali oleza mtima. (1 Sam. 13:8-14) Mungadzifunse kuti: ‘N’ciyani cinapangitsa kuti asakhale oleza mtima? Nanga anakumana na mavuto otani?’ w23.08 25 ¶15