Cisanu, September 19
[Pitilizani] kukondana.—1 Yoh. 4:7.
Tonse timafuna kuti “tipitilize kukondana.” Komabe, m’pofunika kwambili kukumbukila cenjezo la Yesu lakuti “cikondi ca anthu ambili cidzazilala.” (Mat. 24:12) Yesu sanatanthauze kuti izi zidzacitika pa mlingo waukulu pakati pa ophunzila ake. Ngakhale n’telo, tiyenela kukhala osamala kuti tisasoceletsedwe na kupanda cikondi kwa m’dzikoli. Tili na mfundo imeneyi m’maganizo, tiyeni tione funso lofunika kwambili ili: Kodi pali njila imene tingadziŵile ngati cikondi cathu pa abale cikali colimba? Njila imodzi imene tingadziŵile ngati cikondi cathu cikali colimba, ni kuona mmene timasamalila zocitika zina mu umoyo wathu. (2 Akor. 8:8) Cocitika cimodzi cinachulidwa na mtumwi Petulo. Iye anati: “Koposa zonse, khalani okondana kwambili, pakuti cikondi cimakwilila macimo oculuka.” (1 Pet. 4:8) Conco, zifooko komanso kupanda ungwilo kwa ena zingatithandize kudziŵa ngati cikondi cathu pa iwo cikali colimba. w23.11 10-11 ¶12-13
Ciŵelu, September 20
Muzikondana.—Yoh. 13:34.
Sitingamvele lamulo la Yesu lakuti tizikondana ngati timakonda ena mu mpingo na kupewa kukonda ena. Monga mmene zinalili kwa Yesu, nafenso sitingakhale omasuka kwa onse. (Yoh. 13:23; 20:2) Koma mtumwi Petulo akutikumbutsa kuti tiyenela kuyesetsa ‘kukonda gulu lonse la abale,’ cifukwa ni mbali ya banja lathu. (1 Pet. 2:17) Petulo anatilimbikitsa kuti tiyenela ‘kukondana kwambili kucokela mu mtima.’ (1 Pet. 1:22) Palembali, mawu akuti kukonda “kwambili” aphatikizapo kuonetsa cikondi kwa munthu wina ngakhale kuti zingakhale zovuta kucita zimenezo. Mwacitsanzo, ngati m’bale watikhumudwitsa m’njila ina yake, mwacibadwa tingafune kubwezela m’malo moonetsa cikondi. Komabe, Petulo anaphunzila kuti kubwezela sikukondweletsa Mulungu. (Yoh. 18:10, 11) Petulo analemba kuti: “Osabwezela coipa pa coipa kapena cipongwe pa cipongwe, koma m’malomwake muzidalitsa.” (1 Pet. 3:9) Lolani cikondi kukusonkhezelani kukhala okoma mtima komanso oganizila ena. w23.09 28-29 ¶9-11
Sondo, September 21
Nawonso akazi akhale . . . ocita zinthu mosapitilila malile, okhulupilika m’zinthu zonse.—1 Tim. 3:11.
Timacita cidwi kuona mmene mwana amakulila mwamsanga kukhala wamkulu. Kukula kumeneku kumacitika pakokha. Komabe, kukhala Mkhristu wokhwima sikucitika pakokha. (1 Akor. 13:11; Aheb. 6:1) Kuti tikwanilitse colinga cimeneci, tiyenela kukhala paubwenzi wa thithithi na Yehova. Tifunikilanso mzimu wake woyela pokulitsa makhalidwe aumulungu, kukulitsa maluso othandiza komanso kukonzekela maudindo a m’tsogolo. (Miy. 1:5) Yehova ndiye analenga amuna na akazi. (Gen. 1:27) N’zoonekelatu kuti amuna na akazi amasiyana m’maonekedwe. Ndipo amasiyananso m’njila zina. Mwacitsanzo, Yehova analenga amuna na akazi kuti azigwila nchito zosiyana. Conco, onse ayenela kukhala na makhalidwe komanso maluso amene angawathandize kukwanilitsa maudindo awo.—Gen. 2:18. w23.12 18 ¶1-2