Kodi Nthawi Zonse Mumayang’anapo pa Boodi ya Zilengezo?
Akulu, atumiki othandiza, ndi ena amene ali ndi maudindo mumpingo kaŵili-kaŵili amayang’ana pa boodi ya zilengezo, kuti aone pamene adzakhala ndi mbali. Komabe, onse mumpingo adzapezapo mfundo zothandiza. Kodi mudziŵa tsiku limene mudzayeletsa Nyumba ya Ufumu? Kodi woyang’anila dela kapena ofesi ya nthambi atumizilako mpingo wanu makalata ofunika? Kodi muudziŵa mutu wa nkhani ya anthu onse ya mlungu uno, n’colinga cakuti mukaitane phunzilo lanu la Baibo? Kodi pali masinthidwe ena okhudza ndandanda ya misonkhano kapena yokhudza kagulu kanu ka ulaliki? Zambili za izi tinaleka kulengeza mkati mwa misonkhano, ndipo n’zosatheka kuti akulu azidziŵitsa ofalitsa aliyense zimenezi. Ndiye cifukwa cake, nthawi zonse tiyenela kuyang’ana boodi ya zilengezo. Ngati ticita zimenezi nthawi zonse, ndiye kuti zinthu zonse zidzacitika “moyenela ndi mwadongosolo.”—1 Akor. 14:40.