Kubweleza za m’Sukulu ya Ulaliki
Tidzakambilana mafunso otsatilawa pa Sukulu ya Ulaliki kuyambila mlungu wa August 31, 2015.
Kodi mfundo coonadi zokhudza Yehova Mulungu zopezeka m’pemphelo la Solomo zimalimbitsa bwanji cikhulupililo cathu? Nanga kuganizila mozama mfundo zimenezi n’kopindulitsa bwanji? (1 Maf. 8:22-24, 28) [July 6, w05 7/1 tsa. 30 ndime 3]
Kodi tingaphunzile ciani pa citsanzo ca Davide ca kukhala “ndi mtima wosagaŵanika”? (1 Maf. 9:4) [July 13, w12 11/15 tsa. 7 ndime 18-19]
Kodi zimene Mulungu anacita potumiza Eliya kwa mkazi wamasiye wa ku Zarefati zikutiphunzitsa mfundo yofunika iti? (1 Maf. 17: 8-14) [July 27, w14 2/15 tsa. 14]
Kodi kuganizila mozama nkhani ya pa 1 Mafumu 17:10-16 kungalimbitse bwanji cikhulupililo cathu mwa Yehova? [July , 27 w14 2/15 mas. 13-15]
Tingaphunzile ciani pa zimene Eliya anacita atapanikizika maganizo? (1 Maf. 19:4) [Aug. 3, ia mas. 102-103 ndime 10-12; w14 3/15 tsa. 15 ndime 15-16]
Kodi Yehova anacita ciani pamene mneneli wake wokhulupilika Eliya anapanikizika ndi mavuto? Nanga tingatsatile bwanji citsanzo ca Mulungu wathu wacikondi? (1 Maf. 19:7, 8) [Aug. 3, w14 6/1 tsa. 21 ndime 15-16]
Ndi maganizo olakwika ati amene Mfumu Ahabu anali nao? Nanga Akristu angapewe bwanji maganizo otelo? [Aug. 10, lv mas. 164-165, bokosi; w14 2/1 tsa. 30 ndime 3-4]
Tikuphunzilapo ciani pa zimene Elisa anapempha kwa Eliya, makamaka ngati tapatsidwa utumiki watsopano? (2 Maf. 2:9, 10) [Aug. 17, w03 11/1 tsa. 31 ndime 5-6]
Kodi acicepele angatengele bwanji cikhulupililo ndi kulimba mtima kwa kamtsikana kaciisiraeli kochulidwa pa 2 Mafumu 5:1-3? [Aug. 24, w12 2/15 mas. 12-13 ndime 11]
M’masiku otsiliza ano, ndi makhalidwe ati a Yehu amene atumiki onse a Yehova ayenela kutengela? (2 Maf. 10:16) [Aug. 31, w11 11/15 tsa. 5 ndime 4]