CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | YOBU 11-15
Yobu Anali ndi Cikhulupililo Cakuti Akufa Adzauka
Yobu anaonetsa kuti anali ndi cikhulupililo cakuti Mulungu adzamuukitsa
14:7-9, 13-15
Yobu anaonetsa cikhulupililo cake cakuti Mulungu adzaukitsa akufa pamene anayelekezela ciyembekezoco ndi mtengo, mwina wa maolivi
Mtengo wa maolivi akaudula umaphukanso cifukwa cakuti mizu yake imapita pansi kwambili ndiponso imayala malo aakulu. Ngati mizu yake ikali bwino, mtengowu sulephela kuphuka
Mvula ikagwa pambuyo pa cilala coopsa, mizu ya citsa couma ca mtengo wa maolivi imaphuka n’kukhala ndi “nthambi ngati mtengo watsopano”