CUMA COCOKELA M’MAU A MULUNGU | YESAYA 24-28
Yehova Amasamalila Anthu Ake
Mofanana ndi munthu wolandila alendo mooloŵa manja, Yehova amatigaŵila cakudya cauzimu ca mwana alilenji.
“Yehova wa makamu adzakonzela anthu a mitundu yonse . . . phwando la zakudya zabwino zabwino”
25:6
M’nthawi za m’Baibo, kudyela pamodzi cakudya kunali kuonetsa kuti anthuwo anali pamtendele ndi paubwenzi
“Zokhala ndi mafuta a m’mafupa, ndiponso la vinyo wokoma kwambili, wosefedwa bwino”
Zakudya zabwino-zabwino ndi vinyo wokoma kwambili ziimila zakudya za kuuzimu zabwino ngako zimene Yehova amatipatsa