CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MATEYU 16-17
Kodi Muli na Maganizo a Ndani?
Ngakhale kuti mwina Petulo anali kukamba ali na zolinga zabwino, Yesu sanazengeleze kumuwongolela pa kaganizidwe kake kolakwika.
Yesu anadziŵa kuti imeneyo siinali nthawi yakuti ‘adzikomele mtima.’ Mosakayikila, Satana ndiye anali kufuna kuti Yesu adzikomele mtima panthawi yovuta ngati imeneyo.
Yesu anachula zinthu zitatu zotithandiza kukwanilitsa cifunilo ca Mulungu. Kodi ciliconse ca zinthuzi citanthauza ciani?
Kudzikana wekha
Kunyamula mtengo wako wozunzikilapo
Kutsatila Yesu mosalekeza