CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YAKOBO 3-5
Muzionetsa Nzelu Yaumulungu
3:17
Nzelu zocokela kwa Yehova n’zothandiza mu umoyo. Mwacitsanzo, zingatithandize kukhazikitsa mtendele na okhulupilila anzathu. Ngati munthu ali na nzelu yaumulungu, makhalidwe ake amaonetsa zimenezi.
DZIFUNSENI KUTI: ‘Pa makhalidwe a nzelu yaumulungu ali pansipa, ni ati amene naonetsako posacedwapa? Nanga ningacite ciani kuti nizionetsanso ena mwa makhalidwe amenewa?’
Yoyela
Yamtendele
Yololela
Yokonzeka kumvela
Yodzadza ndi cifundo na zipatso zabwino
Yopanda tsankho
Yopanda cinyengo