NYIMBO 73
Tilimbitseni Mtima
Yopulinta
1. Pamene tilalikila,
Uthenga wa Ufumu,
Ambili amatitsutsa
Ena amatiseka.
Koma sitiŵayopa
Timvelela imwe mwekha
Conde tipempha mzimu wanu,
Mvelani pemphelo lathu.
(KOLASI)
Tithandizeni Yehova,
Mu utumiki wathu,
Tikhale olimba mtima
Tisayope adani,
Pamene tiyembekeza
Tsiku lanu lalikulu,
Tithandizeni Yehova
Tipemphela.
2. Pamene tivutitsiwa,
Ise mutithandiza,
Ngakhale ticite mantha
Imwe mutimvetsetsa.
Conde tilanditseni
Kwa adani athu onse.
Tilankhule molimba mtima
Pamene tilalikila.
(KOLASI)
Tithandizeni Yehova,
Mu utumiki wathu,
Tikhale olimba mtima
Tisayope adani,
Pamene tiyembekeza
Tsiku lanu Lalikulu,
Tithandizeni Yehova
Tipemphela.
(Onaninso 1 Ates. 2:2; Aheb. 10:35.)