LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb23 May tsa. 16
  • Dziteteni kwa Anthu Ampatuko

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Dziteteni kwa Anthu Ampatuko
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
  • Nkhani Zofanana
  • Zisankho Zimene Zimaonetsa Kuti Timadalila Yehova
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
  • Pezani Mayankho pa Mafunso Aya
    2025-2026 Pulogilamu ya Msonkhano wa Dela—Wa Woyang’anila Dela
  • Mmene Tingathetsele Zikaiko Zathu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Pezani Mayankho pa Mafunso Aya
    2025-2026 Pulogilamu ya Msonkhano wa Dela—Wa Woimila Nthambi
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
mwb23 May tsa. 16

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Dziteteni kwa Anthu Ampatuko

Satana komanso anthu amene ali kumbali yake, nthawi zambili amafalitsa mabodza pofuna kufooketsa cikhulupililo cathu. (2 Mbiri 11:3) Mwacitsanzo, Asuri anagwilitsa nchito mfundo zosoceletsa, komanso mabodza amkunkhuniza pofuna kufooketsa anthu a Yehova (2 Mbiri 32:10-15) Izi n’zimenenso ampatuko amacita masiku ano. Kodi tiyenela kuziona bwanji ziphunzitso za ampatuko? Tiyenela kuziona kuti ni zovulaza mofanana na poizoni! Sitiyenela kuziŵelenga ziphunzitso zimenezo kapena kunenapo ciliconse. Komanso sitiyenela kuzitumiza kwa ena kapena kuwafotokozelako. Cinanso, muziyesetsa kuzindikila mwamsanga mfundo zabodza zimene zingakupangitseni kukayikila Yehova na gulu lake, ndipo zikaneni!—Yuda 3, 4.

Cithunzi cocokela m’vidiyo yakuti “‘Menyani Mwamphamvu Nkhondo ya Cikhulupililo”!—Mbali Yake.” M’bale David Splane wa m’Bungwe Lolamulila.

ONELELANI VIDIYO YAKUTI “MENYANI MWAMPHAMVU NKHONDO YA CIKHULUPILILO”!—MBALI YAKE, KENAKO YANKHANI MAFUNSO AWA:

  • N’cifukwa ciyani tiyenela kukhala osamala pogwilitsa nchito mawebusaiti a makambilano?

  • Kodi tingatsatile bwanji ulangizi wa pa Aroma 16:17?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani