-
Yesaya 24:3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Anthu onse adzachotsedwa mʼdzikolo.
Katundu yense wamʼdzikolo adzatengedwa,+
Chifukwa Yehova ndi amene wanena mawu amenewa.
-
-
Yeremiya 25:9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 ndikuitana mafuko onse akumpoto,”+ akutero Yehova, “ndikuitananso Mfumu Nebukadinezara* ya ku Babulo, mtumiki wanga.+ Ndibweretsa anthu amenewa kuti aukire dziko lino+ ndi anthu amene akukhala mmenemo komanso mitundu yonse imene yakuzungulirani.+ Ndidzakuwonongani inuyo ndi mitundu yonse yokuzungulirani ndipo ndidzakusandutsani chinthu chochititsa mantha chimene anthu azidzachiimbira mluzu ndipo malo anu adzakhala mabwinja mpaka kalekale.
-