-
Yeremiya 39:13, 14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Choncho Nebuzaradani mkulu wa asilikali olondera mfumu ndi Nebusazibani amene anali Rabisarisi,* Nerigali-sarezera amene anali Rabimagi* ndi akuluakulu onse a mfumu ya Babulo anatuma anthu. 14 Iwo anatuma anthuwo kuti akatenge Yeremiya mʼBwalo la Alonda+ nʼkumupereka kwa Gedaliya+ mwana wa Ahikamu,+ mwana wa Safani,+ kuti apite naye kunyumba kwake. Choncho Yeremiya anayamba kukhala ndi anthu.
-
-
Yeremiya 40:5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Yeremiya akuganizira koti apite, Nebuzaradani anamuuza kuti: “Bwerera kwa Gedaliya,+ mwana wa Ahikamu,+ mwana wa Safani,+ amene mfumu ya Babulo yamuika kuti azilamulira mizinda ya Yuda. Ukakhale naye pakati pa anthuwo, kapena ukhoza kupita kulikonse kumene ungakonde.”
Kenako mkulu wa asilikali olondera mfumu anamupatsa chakudya chapaulendo ndi mphatso ndipo anamulola kuti apite.
-