Salimo
Pemphero la Davide.
2 Tetezani moyo wanga chifukwa ndine wokhulupirika.+
Pulumutsani mtumiki wanu amene amakukhulupirirani,
Chifukwa ndinu Mulungu wanga.+
4 Chititsani kuti mtumiki wanu asangalale,*
Chifukwa ndimayangʼana kwa inu, Yehova.
5 Inu Yehova ndinu wabwino+ ndipo ndinu wokonzeka kukhululuka.+
Mumasonyeza chikondi chokhulupirika chochuluka kwa onse amene amaitana inu.+
6 Mvetserani pemphero langa inu Yehova.
Ndipo mvetserani kuchonderera kwanga kopempha thandizo.+
8 Inu Yehova, palibe mulungu wina amene angafanane ndi inu,+
Palibe aliyense amene wachita zinthu zofanana ndi zimene inu mwachita.+
9 Mitundu yonse ya anthu imene munapanga
Idzabwera nʼkudzagwada pamaso panu, inu Yehova,+
Ndipo idzalemekeza dzina lanu.+
11 Ndilangizeni inu Yehova, za njira yanu.+
Kuti ndiyende mʼchoonadi chanu.+
Ndithandizeni kuti ndiziopa dzina lanu ndi mtima wonse.*+
12 Ndimakutamandani ndi mtima wanga wonse, inu Yehova Mulungu wanga,+
Ndipo ndidzalemekeza dzina lanu mpaka kalekale,
13 Chifukwa chikondi chanu chokhulupirika chimene mumandisonyeza ndi chachikulu
14 Inu Mulungu, anthu onyada andiukira.+
Gulu la anthu ankhanza likufuna kuchotsa moyo wanga,
15 Koma inu Yehova, ndinu Mulungu wachifundo komanso wokoma mtima,
Wosakwiya msanga, wachikondi chokhulupirika chochuluka ndiponso wokhulupirika.*+
16 Ndiyangʼaneni ndipo mundikomere mtima.+
Patsani mtumiki wanu mphamvu,+
Ndipo pulumutsani mwana wa kapolo wanu wamkazi.
17 Ndisonyezeni chizindikiro cha* ubwino wanu,
Kuti anthu amene amadana nane aone ndipo achititsidwe manyazi,
Chifukwa inu Yehova ndi amene mumandithandiza komanso kundilimbikitsa.