Salimo
Nyimbo ndi Salimo la ana a Kora.+
48 Yehova ndi wamkulu komanso woyenera kutamandidwa kwambiri,
Mumzinda wa Mulungu wathu, mʼphiri lake loyera.
2 Phiri la Ziyoni limene lili mʼdera lakutali lakumpoto,
Ndi lokongola chifukwa lili pamalo okwezeka komanso anthu padziko lonse lapansi akusangalala nalo,+
Ndipo ndi mzinda wa Mfumu Yaikulu.+
3 Munsanja zake zokhala ndi mpanda wolimba,
4 Taonani! Mafumu asonkhana,*
Onse pamodzi abwera.
5 Iwo ataona mzindawo, anadabwa.
Anapanikizika nʼkuthawa mwamantha.
6 Kumeneko iwo anayamba kunjenjemera,
Anavutika ngati mkazi amene akubereka.
7 Pogwiritsa ntchito mphepo yamphamvu yakumʼmawa, munaswa sitima za ku Tarisi.
8 Zimene tinangomva, tsopano taziona tokha,
Mumzinda wa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, mumzinda wa Mulungu wathu.
Mulungu adzakhazikitsa mzindawo mpaka kalekale.+ (Selah)
9 Inu Mulungu, ife timaganizira mozama za chikondi chanu chokhulupirika,+
Tili mʼkachisi wanu.
10 Inu Mulungu, mofanana ndi dzina lanu, mawu okutamandani
Afika kumalire a dziko lapansi.+
Dzanja lanu lamanja ladzaza ndi chilungamo.+
12 Gubani mozungulira Ziyoni. Zungulirani mzinda wonsewo,
Werengani nsanja zake.+
13 Ganizirani mofatsa za mpanda wake wolimba.+
Yenderani nsanja zake zokhala ndi mpanda wolimba,
Kuti mudzafotokozere mibadwo yamʼtsogolo.
14 Chifukwa Mulungu uyu ndi Mulungu wathu+ mpaka muyaya.