MAFUNSO KWA ANTHU AMENE AKUFUNA KUBATIZIDWA
Chigawo Chachitatu Yehova Ndi Mulungu Wadongosolo
Pophunzira Baibulo, mwadziwa kuti cholinga cha Mulungu n’chofuna kubwezeretsa zinthu mmene zinalili poyamba kuti zonse zizimugonjera. (1 Akor. 15:24-28; Aef. 1:8-10) Pofika pano, mwaona zimene mungachite kuti musonyeze kuti mukugonjera Yehova ndi ulamuliro wake. Mafunso ndi Malemba otsatirawa akuthandizani kumvetsa mmene mungasonyezere kuti mukugonjera Yehova kaya ndi mumpingo, m’banja kapena olamulira a dziko. Mumvetsa bwino mmene Yehova amaphunzitsira anthu ake ndi kuwalimbikitsa mwauzimu. Zimenezi zikuphatikizapo kusonkhana ndiponso kuyankha pa misonkhano.
Komanso chigawo chino chikusonyeza kufunika kogwira nawo ntchito yolalikira nthawi zonse pothandiza ena kuti adziwe Yehova ndi zimene akuchitira anthu. (Mat. 24:14; 28:19, 20) Chigawochi chikuthandizani kudziwa kufunika kodzipereka kwa Yehova ndi kubatizidwa. Dziwani kuti Yehova amayamikira chifukwa munalandira kukoma mtima kwakukulu komwe anakusonyezani.
1. Malinga ndi zimene Mulungu anakonza, kodi mutu wa mkazi wokwatiwa ndi ndani?
“Inu akazi, muzigonjera amuna anu, pakuti zimenezi ndiye zoyenera kwa anthu otsatira Ambuye.”—Akol. 3:18.
“Akazi agonjere amuna awo ngati mmene amagonjerera Ambuye, chifukwa mwamuna ndiye mutu wa mkazi wake monganso mmene Khristu alili mutu wa mpingo, pokhala mpulumutsi wa thupilo.”—Aef. 5:22, 23.
2. Kodi mwamuna ayenera kukhala mutu wotani kwa mkazi wake?
“Amuna akonde akazi awo monga matupi awo. Amene amakonda mkazi wake amadzikonda yekha, pakuti palibe munthu anadapo thupi lake, koma amalidyetsa ndi kulikonda, mmenenso Khristu amachitira ndi mpingo.”—Aef. 5:28, 29.
“Inu amuna, musaleke kukonda akazi anu ndipo musamawapsere mtima kwambiri.”—Akol. 3:19.
3. Kodi mkazi wachikhristu ayenera kuiona bwanji nkhani yogonjera ngati mwamuna wake ali wosakhulupirira?
“Inu akazi, muzigonjera amuna anu kuti ngati ali osamvera mawu akopeke, osati ndi mawu, koma ndi khalidwe lanu, poona okha ndi maso awo khalidwe lanu loyera ndi ulemu wanu waukulu.”—1 Pet. 3:1, 2.
4. Kodi Mulungu wapereka kwa ndani udindo wophunzitsa ndi kulangiza ana?
“Abambo, musamapsetse mtima ana anu, koma muwalere m’malangizo a Yehova ndi kuwaphunzitsa kaganizidwe kake.”—Aef. 6:4.
“Mwana wanga, tamvera malangizo a bambo ako, ndipo usasiye malamulo a mayi ako.”—Miy. 1:8.
5. Kodi ana ali ndi udindo wotani m’banja?
“Ananu, muzimvera makolo anu mwa Ambuye, pakuti kuchita zimenezi n’chilungamo. ‘Uzilemekeza bambo ako ndi mayi ako,’ ndilo lamulo loyamba lokhala ndi lonjezo: ‘Kuti zinthu zikuyendere bwino, ndiponso kuti ukhale ndi moyo wautali padziko lapansi.’”—Aef. 6:1-3.
“Ananu, muzimvera makolo anu pa zinthu zonse, pakuti kuchita zimenezi kumakondweretsa Ambuye.”—Akol. 3:20.
6. Kodi Akhristu ayenera kuwaona bwanji olamulira?
“Munthu aliyense azimvera olamulira akuluakulu, chifukwa palibe ulamuliro umene ungakhalepo kupatulapo ngati Mulungu waulola. Olamulira amene alipowa ali m’malo awo osiyanasiyana mololedwa ndi Mulungu.”—Aroma 13:1.
“Pitiriza kuwakumbutsa kuti azigonjera ndi kumvera maboma ndiponso olamulira. Komanso akhale okonzekera ntchito iliyonse yabwino.”—Tito 3:1.
7. N’chifukwa chiyani Mkhristu ayenera kukhoma misonkho yonse imene boma limafuna?
“Perekani kwa onse zimene amafuna. Amene amafuna msonkho, m’patseni msonkho. Amene amafuna ndalama ya chiphaso, m’patseni ndalama ya chiphaso. Amene amafuna kuopedwa, muopeni. Amene amafuna kupatsidwa ulemu, m’patseni ulemu wake.”—Aroma 13:7.
Lemba lowonjezera: Luka 20:21-25.
8. Kodi pali zochitika zina zimene zingachititse Mkhristu kuti akane kumvera olamulira?
“Atatero anawaitana ndi kuwalamula kuti asalankhulenso kapena kuphunzitsa m’dzina la Yesu kwina kulikonse. Koma poyankha, Petulo ndi Yohane anawauza kuti: ‘Weruzani nokha, ngati n’koyenera pamaso pa Mulungu kumvera inu koposa Mulungu. Koma ife sitingaleke kulankhula zinthu zimene tinaziona ndi kuzimva.’”—Mac. 4:18-20.
“Poyankha Petulo ndi atumwi enawo ananena kuti: ‘Ife tiyenera kumvera Mulungu monga wolamulira, osati anthu.’”—Mac. 5:29.
9. Kodi Mkhristu ayenera kuchita zimene boma limafuna ngati sizikusemphana ndi malamulo a Mulungu, monga kulembetsa ukwati ndi kubadwa kwa ana, kuyankha mafunso a kalembera kapena kukhala ndi ziphaso zofunikira ndi malaisensi?
“M’masiku amenewo, . . . analamula kuti anthu onse m’dzikolo akalembetse m’kaundula. . . . Yosefe nayenso anachoka ku Galileya . . . [ndipo] anapita kukalembetsa limodzi ndi Mariya, amene anamanga naye banja.”—Luka 2:1-5.
“Pitiriza kuwakumbutsa kuti azigonjera ndi kumvera maboma ndiponso olamulira.”—Tito 3:1.
10. Kodi mumpingo wachikhristu amatsatira zotani pa nkhani yogonjera mutu?
“Ndikufuna mudziwe kuti mutu wa mwamuna aliyense ndi Khristu. Mutu wa mkazi ndi mwamuna, ndipo mutu wa Khristu ndiye Mulungu.”—1 Akor. 11:3.
11. Kodi mutu wa mpingo wachikhristu ndi ndani?
“[Khristu] ndiye chifaniziro cha Mulungu wosaonekayo, woyamba kubadwa wa chilengedwe chonse, chifukwa kudzera mwa iye zinthu zina zonse zinalengedwa, zakumwamba ndi zapadziko lapansi. Inde, zinthu zooneka ndi zinthu zosaoneka, kaya ndi mipando yachifumu, kapena ambuye, kapena maboma, kapena maulamuliro. Zinthu zina zonse zinalengedwa kudzera mwa iye, ndiponso chifukwa cha iye. Ndiponso, iye ali patsogolo pa zinthu zina zonse, ndipo zinthu zina zonse zinakhalapo kudzera mwa iye. Iye ndiyenso mutu wa thupilo, lomwe ndi mpingo. Iye ndiye chiyambi, woyamba kubadwa kuchokera kwa akufa, kuti adzakhale woyamba pa zinthu zonse.”—Akol. 1:15-18.
12. Kodi Bungwe Lolamulira n’chiyani, ndipo likugwira ntchito yotani masiku ano?
“Amuna ena ochokera ku Yudeya anapita kumeneko ndi kuyamba kuphunzitsa abale kuti: ‘Mukapanda kudulidwa malinga ndi mwambo wa Mose, simungapulumuke.’ Koma Paulo ndi Baranaba sanamvane nawo ndipo anatsutsana nawo kwambiri. Choncho iwo anasankha Paulo ndi Baranaba, pamodzi ndi ena mwa iwo, kuti apite kwa atumwi ndi akulu ku Yerusalemu, kuti akawauze za kutsutsanako.”—Mac. 15:1, 2.
“Popitiriza ulendo wawo m’mizinda, anali kupatsa okhulupirira a kumeneko malamulo oyenera kuwatsatira, malinga ndi zimene atumwi ndi akulu ku Yerusalemu anagamula. Choncho mipingo inapitiriza kulimba m’chikhulupiriro ndipo chiwerengero chinapitiriza kuwonjezeka tsiku ndi tsiku.”—Mac. 16:4, 5.
“Ndani kwenikweni amene ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru amene mbuye wake anamuika kuti aziyang’anira antchito ake apakhomo, ndi kuwapatsa chakudya pa nthawi yoyenera? Kapolo ameneyu adzakhala wodala ngati mbuye wake pobwera adzam’peza akuchita zimenezo! Ndithu ndikukuuzani, Adzamuika kuti aziyang’anira zinthu zake zonse.”—Mat. 24:45-47.
13. Kodi ndani mumpingo amene amaimira Khristu yemwe ndi mutu wa mpingo?
“Mukhale tcheru ndi kuyang’anira gulu lonse la nkhosa, limene mzimu woyera wakuikani pakati pawo kukhala oyang’anira, kuti muwete mpingo wa Mulungu, umene anaugula ndi magazi a Mwana wake weniweni.”—Mac. 20:28.
“Choncho, ndikulangiza akulu amene ali pakati panu mowadandaulira, pakuti inenso ndine mkulu ngati iwowo. Ndinenso mboni ya masautso a Khristu, ndiponso ndidzalandira nawo ulemerero umene udzaonekere. Kwa iwo ndikuti: Wetani gulu la nkhosa za Mulungu lomwe analisiya m’manja mwanu, osati mokakamizika, koma mofunitsitsa. Osatinso chifukwa chofuna kupindulapo kenakake, koma ndi mtima wonse. Osati mochita ufumu pa anthu amene ali cholowa chochokera kwa Mulungu, koma mukhale zitsanzo kwa gulu la nkhosa.”—1 Pet. 5:1-3.
14. Kodi abale ndi alongo mumpingo amasonyeza bwanji kuti amagonjera Khristu monga mutu wa mpingo?
“Kumbukirani amene akutsogolera pakati panu. Amenewa anakuphunzitsani mawu a Mulungu. Ndipo pamene mukuonetsetsa zotsatira zabwino za khalidwe lawo, tsanzirani chikhulupiriro chawo.”—Aheb. 13:7.
“Muzimvera amene akutsogolera pakati panu ndipo muziwagonjera. Iwo amayang’anira miyoyo yanu monga anthu amene adzayankhe mlandu. Muziwamvera ndi kuwagonjera kuti agwire ntchito yawo mwachimwemwe, osati modandaula, pakuti akatero zingakhale zokuvulazani.”—Aheb. 13:17.
15. Kodi m’Baibulo analembamo maganizo a ndani? N’chifukwa chiyani nthawi zonse muyenera kumaphunzira Mawu a Mulungu komanso kumapeza nthawi yopanga kulambira kwa pabanja mlungu uliwonse?
“Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa pa kuphunzitsa, kudzudzula, kuwongola zinthu ndi kulangiza m’chilungamo, kuti munthu wa Mulungu akhale woyenerera bwino ndi wokonzeka mokwanira kuchita ntchito iliyonse yabwino.”—2 Tim. 3:16, 17.
“Amakondwera ndi chilamulo cha Yehova, ndipo amawerenga ndi kusinkhasinkha chilamulo chake usana ndi usiku. Munthu ameneyo adzakhala ngati mtengo wobzalidwa m’mphepete mwa mitsinje ya madzi, umene umabala zipatso m’nyengo yake, umenenso masamba ake safota, ndipo zochita zake zonse zidzamuyendera bwino.”—Sal. 1:2, 3.
Malemba owonjezera: Deut. 17:18-20; Miy. 2:1-6; 1 Ates. 2:13.
16. N’chifukwa chiyani kupezeka pa misonkhano n’kothandiza? Nanga inuyo mumachita zotani kuti muzipezekapo nthawi zonse?
“Phazi langa lidzaimadi pamalo athyathyathya. Pamsonkhano, ndidzatamanda Yehova.”—Sal. 26:12.
“Ndipo tiyeni tiganizirane kuti tilimbikitsane pa chikondi ndi ntchito zabwino. Tisaleke kusonkhana pamodzi, monga mmene ena achizolowezi chosafika pamisonkhano akuchitira. Koma tiyeni tilimbikitsane, ndipo tiwonjezere kuchita zimenezi, makamaka pamene mukuona kuti tsikulo likuyandikira.”—Aheb. 10:24, 25.
Malemba owonjezera: Sal. 35:18; 149:1.
17. N’chifukwa chiyani muyenera kumayankha pa misonkhano ya mpingo ngati mungakwanitse?
“Ndidzalengeza dzina lanu kwa abale anga. Ndidzakutamandani pakati pa mpingo.”—Sal. 22:22.
“Chitsulo chimanola chitsulo chinzake. Momwemonso munthu amanola munthu mnzake.”—Miy. 27:17.
“Tiyeni nthawi zonse tizitamanda Mulungu. Tizichita zimenezi monga nsembe imene tikupereka kwa Mulungu, yomwe ndi chipatso cha milomo yathu. Timagwiritsa ntchito milomo imeneyi polengeza dzina lake kwa anthu ena.”—Aheb. 13:15.
18. N’chifukwa chiyani tiyenera kumasonyeza chikhulupiriro mwa ntchito zathu?
“Chikhulupiriro pachokha, ngati chilibe ntchito zake, ndi chakufa. Koma wina anganene kuti: ‘Iweyo uli ndi chikhulupiriro, koma ine ndili ndi ntchito zake. Undionetse chikhulupiriro chako popanda ntchito zake, ndipo ine ndikuonetsa chikhulupiriro changa mwa ntchito.’ Ndithudi, monga mmene thupi lopanda mzimu limakhalira lakufa, nachonso chikhulupiriro chopanda ntchito zake ndi chakufa.”—Yak. 2:17, 18, 26.
19. Kodi ndi ntchito iti yotchulidwa m’Baibulo imene Akhristu onse ayenera kuigwira mwamsanga?
“Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.”—Mat. 24:14.
“Choncho pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga. Muziwabatiza m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyera, ndi kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulirani.”—Mat. 28:19, 20.
20. Kodi ndi ndani amene tiyenera kuwauza uthenga wabwino wa Ufumu?
“Sindinakubisireni chilichonse chopindulitsa, ndipo sindinaleke kukuphunzitsani poyera komanso kunyumba ndi nyumba. Koma ndachitira umboni mokwanira kwa Ayuda ndi kwa Agiriki omwe, kuti alape ndi kutembenukira kwa Mulungu, komanso kuti akhale ndi chikhulupiriro mwa Ambuye wathu Yesu.”—Mac. 20:20, 21.
“Anayamba kukambirana . . . tsiku ndi tsiku analinso kukambirana ndi anthu amene anali kuwapeza pamsika.”—Mac. 17:17.
21. N’chifukwa chiyani muyenera kuona udindo wanu wolalikira uthenga wabwino kukhala wofunika kwambiri?
“Choncho mukhale mboni lero, kuti ine ndine woyera pa mlandu wa magazi a anthu onse. Pakuti sindinakubisireni kanthu, koma ndinakuuzani chifuniro chonse cha Mulungu.”—Mac. 20:26, 27.
“Tsopano ngati ndikulengeza uthenga wabwino, chimenechi si chifukwa chodzitamira, pakuti ndinalamulidwa kutero. Ndithudi, tsoka kwa ine ngati sindilengeza uthenga wabwino!”—1 Akor. 9:16.
22. Kodi tingachite chiyani pothandiza pa ntchito ya Ufumu?
“Uzilemekeza Yehova ndi zinthu zako zamtengo wapatali ndiponso ndi zipatso zako zonse zoyambirira. Ukatero nkhokwe zako zidzakhala zodzaza ndipo zoponderamo mphesa zako zidzasefukira ndi vinyo watsopano.”—Miy. 3:9, 10.
“Wobzala moumira adzakololanso zochepa, ndipo wobzala mowolowa manja adzakololanso zochuluka. Aliyense achite mogwirizana ndi mmene watsimikizira mumtima mwake, osati monyinyirika kapena mokakamizika, chifukwa Mulungu amakonda munthu wopereka mokondwera.”—2 Akor. 9:6, 7.
23. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakonda abale ndi alongo athu amene akufunikira thandizo?
“Ngati m’bale kapena mlongo ali waumphawi ndipo alibe chakudya chokwanira pa tsikulo, koma wina mwa inu n’kunena kuti: ‘Yendani bwino, mupeze zovala ndi zakudya za tsiku lililonse,’ koma osamupatsa zimene thupi lake likusowazo, kodi pali phindu lanji?”—Yak. 2:15, 16.
Malemba owonjezera: Miy. 3:27; Yak. 1:27.
24. Kodi maganizo athu ayenera kukhala otani pa nkhani ya kudzipereka komanso kugwiritsa ntchito chuma chathu potumikira Yehova?
“Ndine ndani ine, ndipo anthu anga ndani kuti tithe kupereka nsembe zaufulu ngati zimenezi? Pakuti chilichonse n’chochokera kwa inu, ndipo tapereka kwa inu zochokera m’dzanja lanu.”—1 Mbiri 29:14.
“Aliyense achite mogwirizana ndi mmene watsimikizira mumtima mwake, osati monyinyirika kapena mokakamizika, chifukwa Mulungu amakonda munthu wopereka mokondwera.”—2 Akor. 9:7.
25. Kodi tiyenera kukhala ndi maganizo otani tikamazunzidwa kapena tikakumana ndi mayesero?
“Odala ndi anthu amene akuzunzidwa chifukwa cha chilungamo, pakuti ufumu wakumwamba ndi wawo. Ndinu odala pamene anthu akukunyozani ndi kukuzunzani, komanso kukunamizirani zoipa zilizonse chifukwa cha ine. Kondwerani, dumphani ndi chimwemwe, chifukwa mphoto yanu ndi yaikulu kumwamba, pakuti umu ndi mmenenso anazunzira aneneri amene analipo inu musanakhaleko.”—Mat. 5:10-12.
“Abale anga, sangalalani pamene mukukumana ndi mayesero osiyanasiyana, monga mukudziwira kuti chikhulupiriro chanu chikayesedwa, chimabala kupirira.”—Yak. 1:2, 3.
“Atumwiwo anachoka pamaso pa Khoti Lalikulu la Ayuda, ali osangalala chifukwa chakuti Mulungu anawaona kuti ndi oyenera kuchitiridwa chipongwe chifukwa cha dzina la Yesu.”—Mac. 5:41.
26. Kodi tiyenera kupemphera kwa ndani, ndiponso m’dzina la ndani?
“Inu Wakumva pemphero, anthu a mitundu yonse adzabwera kwa inu.”—Sal. 65:2.
“Pa tsiku limenelo simudzandifunsanso mafunso. Ndithudi ndikukuuzani, Ngati mupempha chilichonse kwa Atate m’dzina langa adzakupatsani.”—Yoh. 16:23.
Lemba lowonjezera: Yoh. 14:6.
27. Kodi tiyenera kumapemphera bwanji?
“Pamene mukupemphera, musamachite ngati anthu onyenga. Pakuti iwo amakonda kuimirira m’masunagoge ndi m’mphambano za misewu ikuluikulu kuti anthu aziwaona. Ndithu ndikukuuzani, Amenewo akulandiriratu mphoto yawo yonse. Koma iwe popemphera, lowa m’chipinda chako pawekha ndi kutseka chitseko, ndipo pemphera kwa Atate wako amene ali kosaoneka. Ukatero Atate wako amene amaona kuchokera kosaonekako adzakubwezera. Iwe popemphera, usanene zinthu mobwerezabwereza ngati mmene amachitira anthu a mitundu ina, chifukwa iwo amaganiza kuti Mulungu awamvera akanena mawu ambirimbiri. Chotero inu musafanane nawo, chifukwa Mulungu Atate wanu amadziwa zimene mukufuna musanapemphe n’komwe.”—Mat. 6:5-8.
28. Kodi ndi zinthu zina ziti zimene mungatchule m’mapemphero anu?
“Koma inu muzipemphera motere: ‘Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano. Mutipatse ife lero chakudya chathu chalero. Mutikhululukire zolakwa zathu monga mmene ifenso takhululukira amene atilakwira. Musatilowetse m’mayesero, koma mutilanditse kwa woipayo.’”—Mat. 6:9-13.
“Ifetu timamudalira kuti chilichonse chimene tingamupemphe mogwirizana ndi chifuniro chake, amatimvera.”—1 Yoh. 5:14.
29. Kodi khalidwe lathu lingakhudze bwanji mapemphero athu?
“Inunso amuna, pitirizani kukhala ndi akazi anu mowadziwa bwino, ndi kuwapatsa ulemu monga chiwiya chosalimba, kuti mapemphero anu asatsekerezedwe, pakuti mudzalandira nawo limodzi moyo umene Mulungu adzakupatseni chifukwa cha kukoma mtima kwake kwakukulu. Pakuti maso a Yehova ali pa olungama, ndipo makutu ake amamva pembedzero lawo, koma nkhope ya Yehova imakwiyira anthu ochita zoipa.”—1 Pet. 3:7, 12.
Lemba lowonjezera: Yes. 1:15-17.
30. N’chifukwa chiyani a Mboni za Yehova amabatiza m’madzi anthu amene asonyeza chikhulupiriro?
“Choncho pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga. Muziwabatiza m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyera.”—Mat. 28:19.
“M’masiku amenewo, Yesu anabwera kuchokera ku Nazareti wa ku Galileya ndipo anabatizidwa ndi Yohane mu Yorodano.”—Maliko 1:9.
31. N’chifukwa chiyani kuli koyenera kuti Akhristu amene adzipereka kwa Yehova ndi kubatizidwa azitchedwa Mboni za Yehova?
“‘Inu ndinu mboni zanga,’ akutero Yehova. ‘Ndinu mtumiki wanga amene ndakusankhani kuti mundidziwe ndi kundikhulupirira, komanso kuti mumvetse kuti ine sindinasinthe. Ine ndisanakhaleko kunalibe Mulungu amene anapangidwa, ndipo pambuyo panga palibenso wina. Ine ndine Yehova. Popanda ine palibenso mpulumutsi wina.’ ‘Ine ndanena ndipo ndapulumutsa. Pa nthawi imene pakati panu panalibe mulungu wachilendo, ine ndinachititsa kuti chipulumutsocho chimveke. Choncho inuyo ndinu mboni zanga, ndipo ine ndine Mulungu,’ akutero Yehova.”—Yes. 43:10-12.
MFUNDO ZOMALIZIRA ZOKAMBIRANA NDI OFUNA KUBATIZIDWA
Ubatizo umachitika pa misonkhano yadera ndi yachigawo ya Mboni za Yehova. Pa mapeto pa nkhani ya ubatizo, wokamba nkhaniyo amapempha ofuna kubatizidwa kuti aimirire ndi kuyankha mokweza mafunso awiri otsatirawa:
1. Pa maziko a nsembe ya Yesu Khristu, kodi munalapa machimo anu ndi kudzipereka kwa Yehova kuti muchite chifuniro chake?
2. Kodi mukuzindikira kuti kudzipereka kumene munachita, ndi kubatizidwa kwanu lero, zikupangitsani kukhala wa Mboni za Yehova, wogwirizana ndi gulu la Mulungu limene amalitsogolera ndi mzimu wake?
Ofuna kubatizidwa akayankha mafunso amenewa, “amalengeza poyera” kuti amakhulupirira dipo ndiponso adzipereka kwa Yehova. (Aroma 10:9, 10) Nthawi ya ubatizo isanafike, ofuna kubatizidwa ayenera kumapemphera ndi kusinkhasinkha mafunso amenewa kuti akathe kuyankha mochokera pansi pa mtima.
Kodi okabatizidwa ayenera kuvala zovala zotani? (Yoh. 15:19; Afil. 1:10; 1 Tim. 2:9)
Okabatizidwa ayenera kuvala zovala zoyenera polemekeza mwambowo. Sayenera kuvala ngati kuti akupita kukasambira ndiponso sayenera kuvala motayirira. Komanso sayenera kuvala zovala zolembedwa mawu kapena zojambulajambula. Ngati obatizidwa atavala moyenerera adzasonyeza kuti akulemekeza mwambowo ndiponso kungapangitse kuti tizioneka kukhala osiyana ndi dzikoli.
Kodi munthu ayenera kusonyeza khalidwe lotani pamene akubatizidwa? (Luka 3:21, 22)
Ubatizo wa Yesu ndi chitsanzo kwa Akhristu masiku ano. Iye ankadziwa kuti ubatizo ndi mwambo wolemekezeka kwambiri ndipo anasonyeza zimenezi mwa maganizo ndi zochita zake. Choncho malo a ubatizo si malo ochitirako zamasewera, kusambira kapena zina zilizonse zomwe zingapeputse mwambowo. Komanso Mkhristu amene wangobatizidwa kumeneyo sayenera kuchita zinthu ngati kuti wapambana mpikisano winawake. Ngakhale kuti ubatizo ndi chinthu chosangalatsa, chisangalalocho chiyenera kusonyezedwa moyenerera.
Ngakhale pamene mwabatizidwa, n’chifukwa chiyani muyenera kupitirizabe kukhala ndi pulogalamu yabwino yophunzira Baibulo panokha komanso yolowa nawo mu utumiki nthawi zonse?
Kodi kugwirizana kwambiri ndi mpingo kudzakuthandizani bwanji kukhala ndi moyo wogwirizana ndi kudzipereka kwanu kwa Yehova?
Kodi tsopano mwakonzeka kuti mubatizidwe pa msonkhano ukubwerawu?
MALANGIZO KWA AKULU
Wofalitsa wosabatizidwa akadziwitsa akulu kuti akufuna kubatizidwa, muyenera kumulimbikitsa kuti awerenge mosamala “Mafunso Kwa Anthu Amene Akufuna Kubatizidwa,” omwe akupezeka pa tsamba 170-208. Afunikanso aone bwinobwino mutu wakuti “Mawu kwa Wofalitsa Wosabatizidwa,” kuyambira pa tsamba 167, womwe ukufotokoza mmene angakonzekerere zimene akulu adzakambirane naye. Monga tafotokozera kale, wofuna kubatizidwa angagwiritse ntchito notsi zake zimene analemba ndiponso akhoza kutsegula bukuli pa nthawi imene akukambirana ndi akulu. Choncho si kofunika kuti wina akambirane naye mafunsowo asanakakumane ndi akulu.
Munthu akafuna kubatizidwa, ayenera kudziwitsa wogwirizanitsa ntchito za akulu. Munthu wofuna kubatizidwayo akamaliza kuwerenga nkhani ndi mafunsowa, wogwirizanitsa ntchito za akulu adzakonza zoti akulu akumane naye kuti akambirane naye mafunsowo. Simuyenera kudikira chilengezo cha msonkhano kuti muyambe kukambirana mafunsowa ndi anthu ofuna kubatizidwa. Zigawo zitatuzo zingachitidwe maulendo atatu ndipo chilichonse chingatenge pafupifupi ola limodzi, komabe palibe choletsa kupitirira nthawiyi ngati kutakhala kofunika kutero. Mkulu kapena wofuna kubatizidwayo sayenera kukhala pa changu pamene akukambirana mafunsowa. Choncho akulu amene apatsidwa mbaliyi ayenera kupatula nthawi yokwanira ya pulogalamuyi. Ngati n’kotheka chigawo chilichonse chichitidwe ndi mkulu wina. Zingakhale bwino kuyamba ndi kumaliza chigawo chilichonse ndi pemphero.
Nthawi zambiri zimakhala bwino kukambirana mafunsowo ndi munthu aliyense payekha m’malo mokambirana nawo monga gulu. Wofuna kubatizidwa akamayankha funso lililonse, akulu amatha kuona kuti munthuyo akudziwa zinthu zambiri bwanji ndiponso ngati ndi woyenera kubatizidwa kapena ayi. Munthu wofuna kubatizidwayo amakhala womasuka kwambiri akamafunsidwa mafunsowa payekha. Koma ngati ofuna kubatizidwawo ndi banja, mwamuna ndi mkazi wake, angafunsidwe mafunsowa ali limodzi.
Ngati wofuna kubatizidwayo ndi mlongo, mkulu amene akukambirana naye mafunsowa aonetsetse kuti asakhale pamalo a okhaokha. Akhale pamalo oti anthu ena aziwaona koma sangamve nawo zomwe akukambiranazo. Ngati mkuluyo akufuna kukhala ndi munthu wina angachite bwino kutenga mkulu kapena mtumiki wothandiza malinga ndi chigawo chimene akukambirana ndi munthuyo.
M’mipingo imene muli akulu ochepa, atumiki othandiza oyenerera, akhoza kukambirana ndi ofuna kubatizidwa mbali za mafunso zomwe zikukhudza ziphunzitso. Mbali zimenezi ndi “Chigawo Choyamba−Ziphunzitso Zoyambirira za M’Baibulo” ndi “Chigawo Chachitatu−Yehova Ndi Mulungu Wadongosolo.” Akulu okha ndi amene ayenera kukambirana ndi ofuna kubatizidwa “Chigawo Chachiwiri−Malamulo Olungama A Yehova.” Ngati mumpingo mulibe akulu okwanira, akulu angadziwitse woyang’anira dera kuti aone ngati angafunike kupempha akulu a mpingo wapafupi.
Akulu ayenera kutsimikiza kuti munthu amene akufuna kubatizidwayo akumvetsa bwino ziphunzitso zoyambirira za m’Baibulo. Komanso ayenera kuona ngati munthuyo amayamikiradi choonadi ndipo amalemekeza gulu la Yehova. Ngati akuoneka kuti sanamvetsebe ziphunzitso zoyambirira za m’Baibulo, akuluwo angakonze zoti munthuyo apitirize kuthandizidwa kuti nthawi ina adzayenerere kubatizidwa. Ena angafunike kupatsidwa nthawi yaitali yoti asonyeze kuti amakonda kulalikira kapenanso kuti amagonjera malangizo a gulu la Mulungu. Zili ndi akuluwo kuona mmene angachitire kuti nthawi ya ola limodzilo kapena kuposerapo pa chigawo chilichonse, aigwiritse ntchito bwino kuti iwathandize kudziwa ngati munthuyo ali woyenerera kubatizidwa. Mungasankhe kugwiritsa ntchito nthawi yambiri pa mafunso ena kusiyana ndi mafunso ena, koma muyenera kuonetsetsa kuti mwakambirana mafunso onse.
Akulu amene anapatsidwa mbali yokambirana ndi ofuna kubatizidwawo ayenera kukumana pambuyo pa chigawo chachitatu kuti akambirane ndi kuona ngati munthuyo akuyenera kubatizidwa kapena ayi. Akuluwo ayenera kuganizira mbiri ya munthuyo, luso lake, ndi zinthu zina zokhudza munthuyo. Kwenikweni timafuna kudziwa anthu amene atembenukira kwa Yehova ndi mtima wonse ndipo akumvetsa bwino ziphunzitso zoyambirira za m’Baibulo. Akathandizidwa mwachikondi, anthu amene akubatizidwawo adzakhala atumiki okonzeka kugwira ntchito yolalikira uthenga wabwino, yomwe ndi yofunika kwambiri.
Pambuyo pake, mkulu mmodzi kapena awiri angakumane ndi munthu wofuna kubatizidwa uja n’kumufotokozera ngati ali woyenera kubatizidwa kapena ayi. Ngati munthuyo ali woyenerera kubatizidwa, akuluwo ayenera kukambirana naye “Mfundo Zomalizira Zokambirana ndi Ofuna Kubatizidwa,” zomwe zili pa tsamba 209-210. Ngati wofuna kubatizidwayo sanamalize kuphunzira buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani ndi la ‘Mulungu Apitirize Kukukondani,’ akulu ayenera kumulimbikitsa kuti akabatizidwa adzamalize kuphunzira mabukuwa. Kukambirana mfundozi kuyenera kutenga mphindi 10 zokha kapena kucheperapo.
Pakadutsa chaka chimodzi kuchokera pamene munthu wabatizidwa, akulu awiri ayenera kumuyendera kuti akamulimbikitse ndi kumupatsa malangizo ena ndi ena. Mkulu mmodzi pa akulu awiriwo ayenera kukhala woyang’anira kagulu ka utumiki ka munthuyo. Zikakhala kuti wobatizidwa kumeneyo ndi wachinyamata, makolo ake ayenera kukhalapo pa nthawiyi ngati ali a Mboni. Zokambirana zimenezi ziyenera kukhala zosangalatsa ndi zolimbikitsa. Akulu adzafotokoza mmene munthuyo akupitira patsogolo mwauzimu ndi kumuthandiza mmene angachitire kuti apitirize kukhala ndi pulogalamu yabwino yophunzira Baibulo payekha, kuwerenga Baibulo tsiku ndi tsiku, kulambira kwa pabanja mlungu uliwonse, kupezeka pa misonkhano nthawi zonse komanso kuyankha pa misonkhano ndi kulowa mu utumiki wakumunda mlungu uliwonse. (Afil. 3:16) Ngati sanamalizebe kuphunzira buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani ndi la ‘Mulungu Apitirize Kukukondani,’ akuluwo ayenera kukonza zoti munthu wina apitirize kuphunzira naye mabukuwa. Akuluwo angapereke uphungu ndi malangizo mwa apo ndi apo pa nkhani zina koma mbali yaikulu ayenera kumuyamikira kwambiri munthuyo.