August
Lachisanu, August 1
Mavuto a munthu wolungama ndi ambiri, koma Yehova amamupulumutsa ku mavuto onsewo.—Sal. 34:19.
Taonani mfundo ziwiri zofunika zomwe tikupeza mu salimoli: (1) Anthu olungama amakumana ndi mavuto. (2) Yehova amatipulumutsa tikamakumana ndi mayesero. Ndiye kodi iye amatipulumutsa bwanji? Njira imodzi ndi kutithandiza kuti tiziona zinthu moyenera m’dzikoli. Ngakhale kuti Yehova amatilonjeza kuti tizisangalala tikamamutumikira, sanena kuti sitizikumana ndi mavuto panopa. (Yes. 66:14) Iye amatilimbikitsa kuti tiziganizira za nthawi imene tidzakhale ndi moyo umene amafuna kuti tidzasangalale nawo mpaka kalekale. (2 Akor. 4:16-18) Koma panopa iye amatithandiza kuti tipitirize kumutumikira tsiku lililonse. (Maliro 3:22-24) Kodi tingaphunzire chiyani pa zitsanzo za atumiki okhulupirika a Yehova otchulidwa m’Baibulo komanso a masiku ano? Tingakumane ndi mavuto omwe sitimayembekezera. Koma ngati timadalira Yehova, iye sadzalephera kutithandiza.—Sal. 55:22. w23.04 17:3-4
Loweruka, August 2
Munthu aliyense azimvera olamulira akuluakulu.—Aroma 13:1.
Tingaphunzirepo kanthu pa chitsanzo cha Yosefe ndi Mariya, omwe anali okonzeka kumvera olamulira akuluakulu ngakhale pamene zinali zovuta kutero. (Luka 2:1-6) Pamene Mariya anali woyembekezera kwa miyezi 9, iye ndi Yosefe anauzidwa kuti achite zinthu zovuta. Augusto yemwe anali wolamulira wa ufumu wa Roma, anali atalamula kuti anthu akalembetse m’kaundula. Yosefe ndi Mariya ankafunika kuyenda ulendo wovuta wodutsa m’mapiri kupita ku Betelehemu, umene unali wamakilomita pafupifupi 150. Ulendo umenewu unali wovuta kwambiri, makamaka kwa Mariya. Iwo akanamadera nkhawa kwambiri zokhudza thanzi la Mariya komanso mwana amene ankayembekezerayo. Kodi zikanakhala bwanji ngati matenda akanamuyambira pamsewu? Iye amayembekezera kudzabereka mwana yemwe adzakhale Mesiya. Koma kodi zimenezi zinachititsa kuti iwo asamvere lamulo la boma? Yosefe ndi Mariya sanalole kuti zinthu zimenezi ziwalepheretse kumvera lamulo. Yehova anawadalitsa chifukwa cha kumvera kwawo. Mariya anafika bwinobwino ku Betelehemu, anabereka mwana wathanzi ndipo anathandiza kuti ulosi wa m’Baibulo ukwaniritsidwe.—Mika 5:2. w23.10 42:9, 11-12
Lamlungu, August 3
Tilimbikitsane.—Aheb. 10:25.
Bwanji ngati mumachita mantha kupereka ndemanga pamisonkhano? Muzikonzekera bwino. (Miy. 21:5) Mukamaidziwa bwino nkhaniyo, sizingakhale zovuta kuti muyankhepo. Komanso ndemanga zanu zizikhala zachidule. (Miy. 15:23; 17:27) Simungamachite mantha kwambiri kupereka ndemanga yachidule. Ndemanga yachidule, mwinanso yokhala ndi chiganizo chimodzi kapena ziwiri, ingakhale yosavuta kumvetsa kwa abale ndi alongo anu kusiyana ndi ndemanga yaitali yokhala ndi mfundo zambiri. Mukamayankha mwachidule komanso m’mawu anuanu, mumasonyeza kuti mwakonzekera bwino komanso mwamvetsa zimene mukuphunzirazo. Bwanji ngati mwayesa kutsatira ena mwa malangizowa koma mukuona kuti mukuchitabe mantha kupereka ndemanga kawiri kapena kuposerapo? Musamakayikire kuti Yehova amayamikira kuti mukuyesetsa kuchita zomwe mungathe. (Luka 21:1-4) Komatu kuchita zomwe mungathe sikutanthauza kudzipanikiza. (Afil. 4:5) Muziona zimene mungakwanitse kuchita, muzidziikira cholinga choti muchite zimenezo ndipo muzipemphera kuti musachite mantha. Mungayambe ndi cholinga choti muzipereka ndemanga imodzi yachidule. w23.04 18:6-8
Lolemba, August 4
Tivale chodzitetezera pachifuwa . . . tivalenso . . . chipewa.—1 Ates. 5:8.
Mtumwi Paulo amatiyerekezera ndi asilikali omwe ali tcheru ndipo avala zovala za kunkhondo. Msilikali yemwe ali pantchito yake, nthawi zonse amayembekezeredwa kukhala wokonzeka kumenya nkhondo. N’chimodzimodzinso ndi ifeyo. Timapitiriza kukonzekera tsiku la Yehova povala chodzitetezera pachifuwa chachikhulupiriro ndi chikondi komanso chisoti chachipulumutso. Chodzitetezera pachifuwa chinkateteza mtima wa msilikali. Chikhulupiriro komanso chikondi, zimateteza mtima wathu wophiphiritsa. Makhalidwewa amatithandiza kuti tipitirizebe kutumikira Mulungu komanso kutsatira Yesu. Chikhulupiriro chimatithandiza kukhala otsimikiza kuti Yehova adzatipatsa mphoto chifukwa chomufunafuna ndi mtima wonse. (Aheb. 11:6) Chimatithandizanso kukhalabe okhulupirika kwa Mtsogoleri wathu, Yesu, ngakhale pamene tikukumana ndi mavuto. Tingalimbitse chikhulupiriro chathu kuti tizipirira mavuto, poganizira zitsanzo za masiku ano za anthu omwe anakhalabe okhulupirika ngakhale kuti ankazunzidwa kapenanso ankakumana ndi mavuto a zachuma. Tingapewe msampha wokonda chuma potsanzira anthu amene anasankha kukhala ndi moyo wosalira zambiri n’cholinga choti aziika zinthu za Ufumu pamalo oyamba. w23.06 26:8-9
Lachiwiri, August 5
Munthu amene amayang’ana mphepo sadzadzala mbewu ndipo amene amayang’ana mitambo sadzakolola.—Mlal. 11:4
Kudziletsa kumaphatikizapo mmene tikumvera komanso zochita zathu. Kudziletsa kumafunikanso kuti tichite zabwino makamaka ngati zimene tikufuna kuchitazo zili zovuta kapena tilibe mtima wofunitsitsa kuzichita. Kumbukirani kuti kudziletsa ndi limodzi mwa makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa choncho muzipempha mzimu woyera kwa Yehova kuti ukuthandizeni kukhala ndi khalidwe lofunikali. (Luka 11:13; Agal. 5:22, 23) Musamadikire kuti zinthu zikhale bwino. M’dzikoli palibe nthawi imene zinthu zonse zingatiyendere bwino. Ngati tingadikire kuti zinthu zikhale bwino, sitingakwaniritse cholinga chathu. Nthawi zina sitingakhale ndi mtima wofunitsitsa kukwaniritsa cholinga chathu chifukwa chakuti cholingacho chikuoneka chovuta. Ngati umu ndi mmene zilili ndi inuyo, kodi mungayambe ndi zinthu zing’onozing’ono pokwaniritsa cholingacho? Ngati cholinga chanu ndi chakuti mukhale ndi khalidwe linalake, bwanji osayamba ndi kusonyeza khalidwelo m’njira zing’onozing’ono? Ngati cholinga chanu ndi choti muwerenge Baibulo lonse, bwanji osayamba ndi kumawerenga kwa nthawi yochepa? w23.05 24:11-13
Lachitatu, August 6
Njira ya olungama ili ngati kuwala kwamphamvu kwa m’mawa kumene kumawonjezereka mpaka kunja kutawala kwambiri.—Miy. 4:18.
M’masiku otsiriza ano, Yehova wakhala akugwiritsa ntchito gulu lake potipatsa chakudya chauzimu n’cholinga choti tonsefe tipitirizebe kuyenda pa “Msewu Wopatulika.” (Yes. 35:8; 48:17; 60:17) Tinganene kuti munthu akavomera kuphunzira Baibulo, amakhala ndi mwayi woyamba kuyenda pa “Msewu Wopatulika.” Ena amangoyenda pamsewuwu kwa kanthawi kochepa kenako n’kuchokapo. Pomwe ena atsimikiza kupitirizabe kuyenda pamsewuwu mpaka atafika komwe akupita. Kodi akupita kuti? Kwa amene ali ndi chiyembekezo chodzapita kumwamba, “Msewu Wopatulika” umakawafikitsa “m’paradaiso wa Mulungu” kumwamba. (Chiv. 2:7) Kwa amene ali ndi chiyembekezo chodzakhala padzikoli, msewuwu umawathandiza kuti adzafike pokhala angwiro kumapeto kwa zaka 1,000. Ngati mukuyenda pamsewu umenewu musamayang’ane kumbuyo, ndipo musachokepo mpaka mutafika m’dziko latsopano. w23.05 22:15-18
Lachinayi, August 7
Ife timasonyeza chikondi, chifukwa Mulungu ndi amene anayamba kutikonda.—1 Yoh. 4:19.
Zingakhale zosavuta kuti mudzipereke kwa Yehova ngati mumaganizira zinthu zonse zimene wakuchitirani. (Sal. 116:12-14) Baibulo limanena kuti Yehova ndi amene amapereka “mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro.” (Yak. 1:17) Mphatso yaikulu kwambiri imene anatipatsa ndi nsembe ya Mwana wake, Yesu. Tangoganizani, dipo lachititsa kuti zikhale zotheka kuti mukhale pa ubwenzi ndi Yehova. Komanso lathandiza kuti mukhale ndi mwayi wodzakhala ndi moyo mpaka kalekale. (1 Yoh. 4:9, 10) Kudzipereka ndi njira yabwino yosonyezera kuti mukuyamikira chikondi chachikulu chimene Yehova wakusonyezani komanso madalitso onse omwe wakupatsani.—Deut. 16:17; 2 Akor. 5:15. w24.03 9:8
Lachisanu, August 8
Munthu amene amachita zabwino amaopa Yehova.—Miy. 14:2.
Makhalidwe oipa omwe dzikoli limalimbikitsa angatichititse kumva ngati mmene anamvera Loti, yemwe anali wolungama. Iye “ankavutika kwambiri mumtima chifukwa cha khalidwe lopanda manyazi limene anthu ophwanya malamulo ankachita,” podziwa kuti Atate wathu wakumwamba amadana ndi makhalidwe oipawa. (2 Pet. 2:7, 8) Kuopa komanso kukonda Mulungu kunachititsa Loti kuti azipewa makhalidwe oipa omwe anthu omuzungulira ankachita. Ifenso tazunguliridwa ndi anthu amene salemekeza mfundo za Yehova za makhalidwe abwino. Ngakhale zili choncho, tingakhalebe ndi makhalidwe abwino ngati titapitiriza kukonda Mulungu komanso kumulemekeza kwambiri. Pofuna kutithandiza kuchita zimenezi, Yehova amatilimbikitsa mwachikondi pogwiritsa ntchito buku la Miyambo. Akhristu onse, amuna, akazi, ana komanso achikulire angapindule kwambiri potsatira malangizo anzeru opezeka m’bukuli. Kuopa Yehova kumatithandiza kuti tisamapereke zifukwa zodzikhululukira ngati khalidwe lathu si labwino. w23.06 28:1-2, 5
Loweruka, August 9
Ngati munthu akufuna kunditsatira, adzikane yekha ndipo anyamule mtengo wake wozunzikirapo nʼkupitiriza kunditsatira tsiku ndi tsiku.—Luka 9:23.
N’kutheka kuti inuyo mwakumana ndi mavuto monga kutsutsidwa ndi achibale, kapenanso mwalolera kuti musakhale ndi zinthu zambiri n’cholinga choti muziika zinthu zokhudza Ufumu pamalo oyamba. (Mat. 6:33) Ngati ndi choncho, dziwani kuti Yehova amaona zimene mukuchita pomutumikira mokhulupirika. (Aheb. 6:10) Mwina inunso mwaona kukwaniritsidwa kwa mawu a Yesu akuti: “Palibe amene wasiya nyumba, azichimwene, azichemwali, amayi, abambo, ana kapena minda chifukwa cha ine komanso chifukwa cha uthenga wabwino, amene panopa sadzapeza zochuluka kuwirikiza maulendo 100 mʼnthawi ino. Iye adzapeza nyumba, azichimwene, azichemwali, amayi, ana ndi minda, komanso adzazunzidwa, ndipo mʼnthawi imene ikubwerayo, adzapeza moyo wosatha.” (Maliko 10:29, 30) Madalitso amene mungapeze ndi aakulu kuposa zimene munadzimana.—Sal. 37:4. w24.03 10:5
Lamlungu, August 10
Mnzako weniweni amakusonyeza chikondi nthawi zonse, ndipo ndi m’bale amene anabadwa kuti akuthandize pakagwa mavuto.—Miy. 17:17.
Pa nthawi imene Akhristu a ku Yudeya ankavutika ndi njala yaikulu, Akhristu a mumpingo wa ku Antiokeya wa ku Siriya “anatsimikiza mtima kutumiza thandizo kwa abale a ku Yudeya, aliyense mogwirizana ndi zimene akanakwanitsa.” (Mac. 11:27-30) Ngakhale kuti Akhristu omwe anakhudzidwa ndi njalayi ankakhala kutali, Akhristu a ku Antiokeya anali atatsimikiza mtima kuti awathandize. (1 Yoh. 3:17, 18.) Ifenso masiku ano tingasonyeze chifundo ngati Akhristu anzathu akhudzidwa ndi ngozi zam’chilengedwe kapena mavuto ena aakulu. Tingachitepo kanthu mofulumira, mwina pofunsa akulu ngati tingagwire nawo ntchito yopereka thandizo, popereka ndalama zothandiza pa ntchito yapadziko lonse kapenanso popempherera amene akhudzidwa. Tingafunikenso kuthandiza abale ndi alongo athu kupeza zofunikira pa moyo. Choncho tiyeni tiyesetse kuti pamene Mfumu yathu, Khristu Yesu, adzabwere kudzapereka chiweruzo, adzatipeze tikusonyeza chifundo ndipo adzatiuze kuti ‘tilowe mu Ufumu.’—Mat. 25:34-40. w23.07 29:9-10, 12
Lolemba, August 11
Anthu onse adziwe kuti ndinu ololera.—Afil. 4:5.
Yesu ankatsanzira Yehova pa nkhani yololera. Iye anatumizidwa padziko lapansili kuti akalalikire kwa “nkhosa zotayika za nyumba ya Isiraeli.” Komabe iye anasonyeza kuti ndi wololera pamene ankachita utumiki wake. Pa nthawi ina, mayi wina yemwe sanali wa Chiisiraeli anamupempha kuti achiritse mwana wake wamkazi, yemwe anali atagwidwa ndi ‘chiwanda chimene chinkamuzunza mwankhanza.’ Mwachifundo Yesu anachita zomwe mayiyo anamupempha ndipo anamuchiritsira mwana wakeyo. (Mat. 15:21-28) Taganiziraninso chitsanzo china. Chakumayambiriro kwa utumiki wake, Yesu ananena kuti:“Aliyense amene adzandikane . . . , inenso ndidzamukana.” (Mat. 10:33) Komatu Yesu sanamusiye Petulo ngakhale kuti Petuloyo anali atamukana maulendo angapo. Ankadziwa kuti Petulo anali atalapa komanso anali wokhulupirika. Ataukitsidwa, iye anaonekera kwa Petulo ndipo mwachidziwikire anamutsimikizira kuti anamukhululukira komanso kuti amamukonda. (Luka 24:33, 34) Onse awiri, Yehova Mulungu komanso Yesu Khristu ndi ololera. Nanga bwanji ifeyo? Yehova amayembekezera kuti ifenso tizikhala ololera. w23.07 32:6-7
Lachiwiri, August 12
Imfa sidzakhalaponso.—Chiv. 21:4.
Kodi tingathandize bwanji anthu amene amakayikira lonjezo la Mulungu lokhudza paradaiso? Choyamba, amene wapereka lonjezoli ndi Yehova. Buku la Chivumbulutso limati: “Ndipo Mulungu amene wakhala pampando wachifumu anati: ‘Taonani! Zinthu zonse zimene ndikupanga ndi zatsopano.’” Iye ali ndi nzeru komanso mphamvu ndipo amafunitsitsa atakwaniritsa malonjezo ake. Chachiwiri, n’zosakayikitsa kuti lonjezoli lidzakwaniritsidwa ndipo kwa Yehova zili ngati lakwaniritsidwa kale. Mpake kuti iye anati: “Mawu amenewa ndi odalirika komanso oona. . . . Zakwaniritsidwa!” Chachitatu, mawu akuti, “Ine ndi Alefa ndi Omega,” akutsimikizira kuti Yehova akayamba kuchita chinthu sasiya mpaka chitatheka. (Chiv. 21:6) Zimene Yehova adzachite zidzasonyeza kuti Satana ndi wabodza komanso wolephera. Ndiye munthu wina akadzanena kuti lonjezo la pa Chivumbulutso 21:4, “likumveka labwino koma n’lovuta kulikhulupirira,” mungadzamuwerengere vesi 5 ndi 6 n’kumufotokozera zimene Yehova ananena potsimikizira lonjezolo, zomwe zinali ngati akusainira mawu ake.—Yes. 65:16. w23.11 46:18-19
Lachitatu, August 13
Ndidzakupangitsa kuti ukhale mtundu waukulu.—Gen. 12:2.
Yehova anamulonjeza Abulahamu pa nthawi yomwe anali ndi zaka 75, ndipo analibe mwana. Kodi Abulahamu anaona zinthu zonse zokhudza lonjezoli zikukwaniritsidwa? Ayi. N’zoona kuti atawoloka mtsinje wa Firate n’kuyembekezera kwa zaka 25, Abulahamu anaona mwana wake Isaki atabadwa m’njira yodabwitsa. Ndipo pambuyo pa zaka zina 60, anaonanso zidzukulu zake, Esau ndi Yakobo zitabadwa. (Aheb. 6:15) Koma Abulahamu sanaone mbadwa zake zikukhala mtundu waukulu komanso kulandira Dziko Lolonjezedwa. Ngakhale zinali choncho, mwamuna wokhulupirikayu anali pa ubwenzi wolimba ndi Mlengi wake. (Yak. 2:23) Ndipo akadzaukitsidwa, adzasangalala kudziwa kuti mitundu yonse ya anthu inadalitsidwa chifukwa cha chikhulupiriro komanso kuleza mtima kwake. (Gen. 22:18) Kodi tikuphunzirapo chiyani? N’kutheka kuti ifenso sitingaone panopa zimene Yehova analonjeza zikukwaniritsidwa. Komabe ngati tili oleza mtima ngati Abulahamu, tingakhale otsimikiza kuti Yehova atidalitsa panopa komanso adzatidalitsa kwambiri m’dziko latsopano lomwe walonjeza.—Maliko 10:29, 30. w23.08 35:14
Lachinayi, August 14
Pa nthawi imene iye ankafunafuna Yehova, Mulungu woonayo anachititsa kuti zinthu zizimuyendera bwino.—2 Mbiri 26:5.
Mfumu Uziya ali wachinyamata anali wodzichepetsa. Iye anaphunzira ‘kuopa Mulungu woona.’ Iye anakhala ndi moyo kwa zaka 68 ndipo Yehova anamudalitsa pa zaka zambiri za moyo wake. (2 Mbiri 26:1-4) Uziya anagonjetsa adani ambiri a Aisiraeli ndipo ankaonetsetsa kuti mzinda wa Yerusalemu ndi wotetezeka. (2 Mbiri 26:6-15) N’zosachita kufunsa kuti Uziya ankasangalala ndi zonse zimene Mulungu anamuthandiza kuchita. (Mlal. 3:12, 13) Mfumu Uziya anali atazolowera kuuza ena zochita. Kodi mwina zimenezi ndi zimene zinamuchititsa kuti aziganiza kuti angathe kuchita chilichonse chomwe ankafuna? Tsiku lina Uziya anachita zinthu modzikuza. Iye analowa m’kachisi wa Yehova n’kuyamba kupereka nsembe zofukiza paguwa, zimene mafumu sankaloledwa kuchita. (2 Mbiri 26:16-18) Mkulu wa Ansembe Azariya anayesa kumuletsa koma iye anakwiya kwambiri. N’zomvetsa chisoni kuti Uziya anawononga mbiri yake yokhala wokhulupirika ndipo Yehova anamulanga pomuchititsa khate. (2 Mbiri 26:19-21) Zinthutu zikanamuyendera bwino akanakhalabe wodzichepetsa. w23.09 38:9-10
Lachisanu, August 15
Anadzipatula, chifukwa ankaopa anthu odulidwawo.—Agal. 2:12.
Ngakhale pambuyo podzozedwa, mtumwi Petulo ankalakwitsabe zinthu zina. Mu 36 C.E., iye analipo pamene Koneliyo anadzozedwa ndi mzimu woyera. Umenewu unali umboni woonekeratu woti “Mulungu alibe tsankho” komanso kuti anthu a mitundu ina anali ndi mwayi wolowa mumpingo wa Chikhristu. (Mac. 10:34, 44, 45) Pambuyo pa zimenezi, Petulo ankamasuka kudya ndi anthu a mitundu ina, zinthu zomwe poyamba sakanachita. Komabe, Akhristu ena a Chiyuda sankaona kuti n’koyenera kuti Ayuda azidya ndi anthu a mitundu ina. Ayuda ena omwe anali ndi maganizo amenewa atabwera ku Antiokeya, Petulo anasiya kudya ndi abale ake a mitundu ina, mwina poopa kuti akhumudwitsa Ayudawo. Mtumwi Paulo ataona zachinyengo zomwe Petulo anachitazi, anamudzudzula pamaso pa anthu onse. (Agal. 2:13, 14) Ngakhale kuti iye analakwitsa zinthu, zimenezi sizinamufooketse. w23.09 40:8
Loweruka, August 16
Adzakulimbitsani.—1 Pet. 5:10.
Kudzifufuza moona mtima kungakuthandizeni kuti mudziwe mbali zina zomwe mukufunika kukonza, komabe simuyenera kutaya mtima. “Ambuye ndi wokoma mtima” ndipo adzakuthandizani. (1 Pet. 2:3) Petulo anatitsimikizira kuti: “Mulungu . . . adzamalizitsa kukuphunzitsani. Iye adzakupatsani mphamvu.” Pa nthawi ina, Petulo ankadziona kuti sanali woyenera kukhala pafupi ndi Mwana wa Mulungu. (Luka 5:8) Koma mothandizidwa ndi Yehova komanso Yesu, iye anapitirizabe kutsatira Khristu mokhulupirika. Choncho Yehova analola kuti Petulo ‘alowe mwaulemerero mu Ufumu wosatha wa Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu.’ (2 Pet. 1:11) Umenewutu unali mwayi wamtengo wapatali. Ngati inunso mutapitirizabe kukhala okhulupirika ngati Petulo, n’kumalola kuphunzitsidwa ndi Yehova, mudzalandira moyo wosatha. “Chikhulupiriro chanu chidzachititsa kuti mupulumuke.”—1 Pet. 1:9. w23.09 41:16-17
Lamlungu, August 17
Lambirani iye amene anapanga kumwamba, [ndi] dziko lapansi.—Chiv. 14:7.
Chihema chinali ndi bwalo lomwe linali malo otchingidwa ndi mpanda kumene ansembe ankagwira ntchito zawo. M’bwaloli munali guwa la nsembe lalikulu lamkuwa ndiponso beseni lamkuwa la madzi limene ansembe ankaligwiritsa ntchito podziyeretsa asanayambe utumiki wawo wopatulika. (Eks. 30:17-20; 40:6-8) Masiku ano, abale a Yesu odzozedwa asanapite kukatumikira ndi Yesu kumwamba monga ansembe amatumikira mokhulupirika padziko lapansi m’bwalo lamkati la kachisi wauzimu. Beseni lalikulu la madzi limakumbutsa odzozedwawo komanso Akhristu ena onse kuti ayenera kukhala ndi makhalidwe abwino komanso oyera mwauzimu. Koma kodi a “khamu lalikulu” amatumikira Yehova ali kuti? Mtumwi Yohane anawaona “ataimirira pamaso pa mpando wachifumu,” zimene zikusonyeza kuti ali m’bwalo lakunja lomwe ndi padziko lapansi kumene ‘akuchitira [Mulungu] utumiki wopatulika usana ndi usiku m’kachisi wake.” (Chiv. 7:9, 13-15) Timayamikira kwambiri kuti Yehova watipatsa mwayi wamtengo wapatali womulambira m’kachisi wake wamkulu wauzimu. w23.10 45:15-16
Lolemba, August 18
Chifukwa cha lonjezo la Mulungu, chikhulupiriro chake . . . chinamupatsa mphamvu.—Aroma 4:20.
Yehova amatipatsa mphamvu pogwiritsa ntchito akulu. (Yes. 32:1, 2) Choncho mukakhala ndi nkhawa, muzifotokozera akulu mavuto anu. Muzivomera akamafuna kukuthandizani ndipo muziyamikira. Yehova akhoza kuwagwiritsa ntchito kuti akupatseni mphamvu. Chiyembekezo chathu chimatipatsa mphamvu. (Aroma 4:3, 18, 19) Chimatithandiza kuti tithe kupirira mayesero, tizilalikira uthenga wabwino komanso tizichita bwino utumiki uliwonse mumpingo. (1 Ates. 1:3) Chiyembekezo chimenechi ndi chomwenso chinapatsa mphamvu mtumwi Paulo. Iye ‘ankapanikizidwa,’ ‘kuthedwa nzeru,’ ‘kuzunzidwa’ ndiponso ‘kugwetsedwa pansi.’ Nthawi zina, ngakhale moyo wake weniweniwo unkakhala pangozi. (2 Akor. 4:8-10) Kuganizira za chiyembekezo chake kunkamuthandiza Paulo kuti apeze mphamvu zoti apirire. (2 Akor. 4:16-18) Iye ankaganizira chiyembekezo chake chokakhala ndi moyo wosatha kumwamba. Zimenezi zinamuthandiza kuti azikhala “watsopano tsiku ndi tsiku.” w23.10 43:14-17
Lachiwiri, August 19
Yehova adzapatsa anthu ake mphamvu. Yehova adzadalitsa anthu ake powapatsa mtendere.—Sal. 29:11.
Tikamapemphera tiziganizira ngati ili nthawi yoyenera yoti Yehova atipatse zimene tikupemphazo. Mwina tingamafune kuti iye aziyankha mapemphero athu nthawi yomweyo. Koma zoona n’zakuti Yehova amadziwa nthawi yabwino yoti atithandize. (Aheb. 4:16) Ngati sitinapatsidwe nthawi yomweyo zimene tapempha, mwina tingamaone kuti Yehova wakana zomwe tapemphazo. Koma mwina zingakhale kuti iye wayankha kuti, ‘Dikira kaye.’ Mwachitsanzo, m’bale wina wachinyamata anapempha kuti achiritsidwe, koma matenda akewo sanathe. Ngati Yehova atamuchiritsa modabwitsa, Satana anganene kuti m’baleyo akupitiriza kutumikira Yehova chifukwa chakuti wamuchiritsa. (Yobu 1:9-11; 2:4) Kuwonjezera pamenepo, Yehova anakonza kale nthawi yoti adzathetse matenda onse. (Yes. 33:24; Chiv. 21:3, 4) Choncho sitimayembekezera kuti Yehova azichiritsa anthu modabwitsa masiku ano. Ndiye m’baleyo angapemphe Yehova kuti amupatse mphamvu komanso mtendere wamumtima kuti apirire matendawo komanso apitirize kumutumikira mokhulupirika.—w23.11 49:13
Lachitatu, August 20
Sanatichitire mogwirizana ndi machimo athu, kapena kutipatsa chilango chogwirizana ndi zolakwa zathu.—Sal. 103:10.
Samisoni anali atalakwitsa zinthu kwambiri komabe sanasiye kutumikira Yehova. Iye anafunafuna mpata woti akwaniritse utumiki umene Mulungu anamupatsa, wogonjetsa Afilisiti. (Ower. 16:28-30) Samisoni anapempha Yehova kuti: “Ndiloleni ndiwabwezere Afilisitiwa.” Mulungu woona anamuyankha ndipo anamupatsanso mphamvu zodabwitsa. Choncho pa nthawiyi, Samisoni anapha Afilisiti ambiri kuposa maulendo ena m’mbuyomo. Ngakhale kuti Samisoni anakumana ndi mavuto aakulu chifukwa cholakwitsa zinthu, iye sanasiye kuchita chifuniro cha Yehova. Choncho kaya talakwitsa zinthu ndipo tikufunika kudzudzulidwa, kusiyitsidwa udindo kapena utumiki winawake, sitiyenera kufooka. Tizikumbukira kuti Yehova amakhala wokonzeka kutikhululukira. (Sal. 103:8, 9) Ngakhale kuti timalakwitsa zinthu, Yehova angatigwiritsebe ntchito ngati mmene anachitira ndi Samisoni. w23.09 37:15-16
Lachinayi, August 21
Kupirira kumachititsa kuti tikhale ovomerezeka kwa Mulungu ndipo kukhala ovomerezeka kwa Mulungu kumachititsa kuti tikhale ndi chiyembekezo.—Aroma 5:4.
Tikapirira mayesero timakhala ovomerezeka kwa Yehova. Zimenezi sizikutanthauza kuti Yehova amasangalala tikamakumana ndi mayesero kapena mavuto. M’malomwake, Mulungu amasangalala ndi ifeyo. Kupirira kwathu kumachititsa kuti tikhale ovomerezeka kwa Mulungu. Amenewatu ndi madalitso aakulu kwambiri. (Sal. 5:12) Kumbukirani kuti Abulahamu anapirira mayesero ndipo Mulungu anasangalala naye. Yehova ankamuona kuti ndi mnzake, ndipo anamutchula kuti ndi wolungama. (Gen. 15:6; Aroma 4:13, 22) Zimenezi zingatichitikirenso ifeyo. Sikuti Mulungu amasangalala ndi kuchuluka kwa zimene timachita pomutumikira kapena maudindo omwe tili nawo. Iye amasangalala nafe chifukwa chakupirira kwathu mokhulupirika. Ndipotu tonsefe tingathe kupirira posatengera msinkhu wathu, mmene zinthu zilili kapenanso luso lathu. Kodi pali mayesero omwe mukupirira mokhulupirika panopa? Ngati ndi choncho, zikulimbikitsani kudziwa kuti Mulungu akusangalala nanu. Kudziwa kuti Mulungu akusangalala nafe kungatithandize kuti chiyembekezo chathu chikhale champhamvu. w23.12 51:13-14
Lachisanu, August 22
Ukhale wolimba mtima.—1 Maf. 2:2.
Mwamuna wa Chikhristu ayenera kuphunzira kulankhula bwino ndi anthu. Munthu amene amalankhula bwino ndi anthu, amamvetsera kuti azindikire zimene zili m’maganizo mwa anthu komanso kuti adziwe mmene akumvera. (Miy. 20:5) Iye amatha kuzindikira zinthu zina chifukwa cha mmene mawu akumvekera, mmene nkhope ikuonekera komanso mmene munthu akuchitira zinthu. Komatu simungadziwe zinthu ngati zimenezi ngati simucheza ndi anthu. Ngati nthawi zonse mumalankhula ndi anthu pogwiritsa ntchito zipangizo zamakono, monga polemba ma imelo kapena mameseji, simungakhale ndi luso lolankhula ndi anthu pamasom’pamaso. Choncho, muziyesetsa kumapeza nthawi yocheza ndi anthu pamasom’pamaso. (2 Yoh. 12) Mwamuna wolimba mwauzimu amafunikanso azipeza zofunika pa moyo wake komanso wa anthu a m’banja lake. (1 Tim. 5:8) Muyenera kuphunzira luso limene lingakuthandizeni kudzapeza ntchito. (Mac. 18:2, 3; 20:34; Aef. 4:28) Muzidziwika kuti ndinu munthu wakhama, amene sasiya ntchito mpaka ataimaliza. Mukatero, mukhoza kupeza ntchito ndipo sangakuchotseni. w23.12 53:12-13
Loweruka, August 23
Tsiku la Yehova lidzabwera ndendende ngati wakuba usiku.—1 Ates. 5:2.
Baibulo likamanena za “tsiku la Yehova,” limatanthauza nthawi imene iye adzawononge adani ake ndi kupulumutsa anthu ake. M’mbuyomu, nthawi zina Yehova ankawononga adani ake. (Yes. 13:1, 6; Ezek. 13:5; Zef. 1:8) M’masiku athu ano, “tsiku la Yehova” lidzayamba ndi kuwonongedwa kwa Babulo Wamkulu ndipo lidzafika pachimake pa nkhondo ya Aramagedo. Kuti tidzapulumuke pa “tsiku” limeneli, tiyenera kukonzekera panopa. Yesu anaphunzitsa kuti, sikuti tiyenera kungokonzekera “chisautso chachikulu” koma tiyeneranso kupitirizabe ‘kukhala okonzeka.’ (Mat. 24:21; Luka 12:40) M’kalata yake youziridwa yoyamba yomwe analembera Akhristu a ku Tesalonika, mtumwi Paulo anagwiritsa ntchito mafanizo angapo pofuna kuwathandiza kuti apitirize kukonzekera tsiku lalikulu la Yehova. Iye ankadziwa kuti tsikuli silinali pafupi pa nthawiyo. (2 Ates. 2:1-3) Komabe, analimbikitsa abale akewo kuti azikonzekera tsikuli ngati kuti libwera mawa ndipo ifenso tiyenera kugwiritsa ntchito malangizo akewa. w23.06 26:1-2
Lamlungu, August 24
Abale anga okondedwa, khalani olimba ndiponso osasunthika.—1 Akor. 15:58.
Cha m’ma 1970, ku Tokyo m’dziko la Japan kunamangidwa nyumba ya nsanjika 60. Anthu amene ankaona nyumbayi ikumangidwa ankada nkhawa chifukwa mumzindawu munkakonda kuchitika zivomerezi. Kodi chinsinsi cha nyumbayi chinagona pati? Akatswiri amene anamanga nyumbayi anaimanga m’njira yakuti ikhale yolimba komanso kuti izitha kugwedezeka koma osawonongeka. Kodi Akhristu amafanana bwanji ndi nyumba imeneyi? Mkhristu ayenera kukhala wosasunthika koma pa nthawi yofananayo ayeneranso kukhala wololera. Iye ayenera kukhala wolimba ndi wosasunthika pa nkhani yotsatira malamulo a Yehova ndiponso mfundo zake. Amakhalanso ‘wokonzeka kumvera’ ndipo amapitiriza kukhala wokhulupirika. Komabe amayenera kukhala ‘wololera’ ngati ndi zotheka kapenanso ngati pakufunika kutero. (Yak. 3:17) Mkhristu amene amaona zinthu moyenera pa nkhani zimenezi amapewa kukhwimitsa kwambiri kapena kulekerera zinthu. w23.07 31:1-2
Lolemba, August 25
Ngakhale kuti Khristuyo simunamuonepo, mumamukonda.—1 Pet. 1:8.
Yesu ankafunika kukana mayesero a Satana Mdyerekezi kuphatikizaponso zimene ankamuuza kuti asakhale wokhulupirika kwa Mulungu. (Mat. 4:1-11) Satana ankayesetsa kuti Yesu achimwe n’cholinga choti alephere kupereka dipo. Pa utumiki wake wapadzikoli, Yesu anapiriranso mayesero ena ambiri. Ankazunzidwa ndipo adani ake ambiri ankamuopseza kuti amupha. (Luka 4:28, 29; 13:31) Ankafunikanso kupirira zimene ophunzira ake ankalakwitsa. (Maliko 9:33, 34) Pamene ankaimbidwa mlandu anachitiridwa nkhanza komanso kunyozedwa. Kenako anaphedwa imfa yowawa komanso yochititsa manyazi. (Aheb. 12:1-3) Ankafunika kupirira mbali yomaliza ya mayesero ake payekha, popanda kuthandizidwa ndi Yehova. (Mat. 27:46) Kunena zoona, Yesu anakumana ndi mavuto aakulu kuti apereke dipo. Kodi kuganizira mavuto amene Yesu anakumana nawo chifukwa chofunitsitsa kupereka moyo wake, sikukukuchititsani kuti muzimukonda kwambiri? w24.01 2:7-9
Lachiwiri, August 26
Onse amene amachita zinthu mopupuluma amasauka.—Miy. 21:5.
Kuleza mtima kumatithandiza tikamachita zinthu ndi ena. Timatha kumvetsera mwatcheru ena akamalankhula. (Yak. 1:19) Kuleza mtima kumalimbikitsanso mtendere. Pamene takhumudwa, kuleza mtima kumatiteteza kuti tisachite zinthu mofulumira kwambiri kapena kulankhula zinthu zimene zingakhumudwitse ena. Ndipo ngati ndife oleza mtima, sitikwiya msanga munthu wina akatikhumudwitsa. M’malo mobwezera, timapitiriza “kulolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse.” (Akol. 3:12, 13) Kuleza mtima kungatithandizenso kuti tizisankha zochita mwanzeru. M’malo mochita zinthu mwaphuma kapena mosaganiza bwino, tidzafufuza komanso kuganizira zimene tikufuna kusankhazo kenako n’kusankha zimene zili zabwino kwambiri. Mwachitsanzo, ngati tikufunafuna ntchito, tikhoza kutengeka kuti tivomere ntchito imene yapezeka mwamsanga. Komabe ngati tili oleza mtima, tidzaganizira mmene ingakhudzire banja lathu ndiponso ubwenzi wathu ndi Yehova. Kuleza mtima kumatithandiza kuti tisasankhe zinthu molakwika. w23.08 35:8-9
Lachitatu, August 27
Ndimaona lamulo lina mʼthupi langa likumenyana ndi malamulo amʼmaganizo mwanga nʼkundichititsa kukhala kapolo wa lamulo la uchimo limene lili mʼthupi langa.—Aroma 7:23.
Mungamafooke chifukwa cha zinthu zoipa zimene mumalakalaka. Kuganizira zimene munalonjeza kwa Yehova pamene munkadzipereka kungakupatseni mphamvu kuti mupitirize kulimbana ndi mayesero. Motani? Mukadzipereka kwa Yehova mumadzikana nokha. Zimenezi zikutanthauza kuti mumakana zolakalaka komanso zofuna zanu zomwe mukuona kuti sizingasangalatse Yehova. (Mat. 16:24) Choncho ngati mutakumana ndi mayesero, simudzachedwa ndi kuganizira zomwe mungachite. Mudzakhala mukudziwa kale chochita, chomwe ndi kukhalabe wokhulupirika kwa Yehova. Mudzafunitsitsa kupitiriza kusangalatsa Yehova. Pochita zimenezo, mudzafanana ndi Yobu. Ngakhale kuti anakumana ndi mayesero aakulu, iye ananena motsimikiza kuti: “Sindidzasiya kukhala wokhulupirika.”—Yobu 27:5. w24.03 10:6-7
Lachinayi, August 28
Yehova ali pafupi ndi onse amene amamuitana, onse amene amamuitana mʼchoonadi.—Sal. 145:18.
Yehova “Mulungu amene ndi wachikondi,” ali nafe. (2 Akor. 13:11) Iye amakonda munthu aliyense payekha. Sitimakayikira kuti nthawi zonse amatisonyeza “chikondi chake chokhulupirika.” (Sal. 32:10) Tikamaganizira kwambiri mmene amasonyezera chikondi chake kwa ife, m’pamenenso timakhala naye pa ubwenzi wolimba kwambiri. Tingathe kupemphera kwa iye momasuka ndi kumufotokozera mmene timayamikirira chikondi chake. Tingamamufotokozerenso zonse zimene zikutidetsa nkhawa n’kumakhulupirira kuti amatimvetsa ndiponso ndi wofunitsitsa kutithandiza. (Sal. 145:19) Tonsefe timakopeka ndi chikondi cha Yehova ngati mmene timachitira ndi moto pa tsiku limene kukuzizira. Chikondi cha Yehova ndi champhamvu koma amachisonyezanso mokoma mtima. Choncho muzisangalala chifukwa Yehova amakukondani. Zimenezi zizitichititsa tonsefe kunena mosangalala kuti: “Ndimakonda Yehova.”—Sal. 116:1. w24.01 4:19-20
Lachisanu, August 29
Ine ndachititsa kuti iwo adziwe dzina lanu.—Yoh. 17:26.
Yesu anachita zambiri kuposa kungodziwitsa anthu kuti dzina la Mulungu ndi Yehova. Ayuda omwe ankawaphunzitsa, ankadziwa kale dzina la Mulungu. Koma Yesu anapereka chitsanzo chabwino chifukwa “ndi amene anafotokoza za Mulungu.” (Yoh. 1:17, 18) Mwachitsanzo, Malemba a Chiheberi amasonyeza kuti Yehova ndi Mulungu wachifundo komanso wokoma mtima. (Eks. 34:5-7) Yesu anamveketsa bwino mfundo ya choonadi imeneyi pamene anafotokoza fanizo la mwana wolowerera ndi bambo ake. Tikamawerenga zimene bamboyu anachita ataona mwana wake wolapayo “ali chapatali ndithu,” n’kumuthamangira, kumukumbatira komanso kumukhululukira ndi mtima wonse, timamvetsa bwino chifundo komanso kukoma mtima kwa Yehova. (Luka 15:11-32) Apa Yesu anathandiza anthu kumvetsa zoona zenizeni zokhudza mmene Atate wake alili. w24.02 6:8-9
Loweruka, August 30
Tizitonthoza [ena] . . . chifukwa nafenso tatonthozedwa ndi Mulungu.—2 Akor. 1:4.
Yehova amatsitsimula komanso kutonthoza anthu omwe akumana ndi mavuto. Kodi tingatsanzire bwanji Yehova potonthoza ena komanso kusonyeza chifundo? Tingachite zimenezi poyesetsa kukhala ndi makhalidwe amene angatithandize kuti titonthoze anthu ena. Kodi ena mwa makhalidwe amenewa ndi ati? Nanga n’chiyani chingatithandize kukhala ndi chikondi chimene chimafunika kuti tizitonthozana kapena kuti “kulimbikitsana” tsiku ndi tsiku? (1 Ates. 4:18) Tiyenera kukhala ndi makhalidwe monga kumvera ena chisoni, kukonda abale komanso kukoma mtima. (Akol. 3:12; 1 Pet. 3:8) Kodi makhalidwe amenewa angatithandize bwanji? Tikamakhala ndi chifundo komanso makhalidwe amene tatchulawa, sitingachitire mwina koma kutonthoza ena. Paja Yesu anati: “Pakamwa pamalankhula zosefukira mumtima. Munthu wabwino amatulutsa zabwino m’chuma chabwino chamumtima mwake, koma munthu woipa amatulutsa zoipa m’chuma choipa chamumtima mwake.” (Mat. 12:34, 35) Kutonthoza abale ndi alongo athu omwe akumana ndi mavuto ndi njira yofunika kwambiri yomwe tingasonyezere kuti timawakonda. w23.11 47:10-11
Lamlungu, August 31
Anthu ozindikira adzawamvetsetsa.—Dan. 12:10.
Tiyenera kupempha Mulungu kuti atithandize kumvetsa ulosi wa m’Baibulo. Taganizirani chitsanzo ichi: Tayerekezerani kuti mukuyenda m’dera lachilendo koma mnzanu amene mwayenda naye akudziwa bwino deralo. Akudziwa bwino pamene muli komanso kumene msewu uliwonse ukulowera. Mosakayikira mungasangalale kuti mnzanuyo anavomera kuti muyende naye. Mofanana ndi zimenezi, Yehova akudziwa bwino nthawi yomwe tikukhalamoyi komanso zimene zichitike kutsogoloku. Choncho kuti tizimvetsa maulosi a m’Baibulo, modzichepetsa tiyenera kupempha Yehova kuti atithandize. (Dan. 2:28; 2 Pet. 1:19, 20) Mofanana ndi kholo lililonse lachikondi, Yehova amafuna kuti ana ake akhale ndi tsogolo labwino. (Yer. 29:11) Koma mosiyana ndi makolo athu, Yehova akhoza kuneneratu zinthu zimene zidzachitike m’tsogolo molondola kwambiri. Iye analola kuti maulosi alembedwe m’Mawu ake ndi cholinga choti tizidziwa zinthu zofunika zisanachitike.—Yes. 46:10. w23.08 34:3-4