Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
Tulukani
Lowani
Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Takulandirani.
Laibulaleyi imathandiza anthu kufufuza mabuku ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova a m'zinenero zosiyanasiyana.
Kuti mupange dawunilodi mabuku, pitani pa jw.org.
  • Lero

Lolemba, November 3

[Yehova] akanena kanthu, kodi angalephere kuchita?​—Num. 23:19.

Njira imodzi yomwe tingalimbitsire chikhulupiriro chathu ndi kuganizira mozama zokhudza dipo. Dipo ndi lomwe limatitsimikizira kuti malonjezo a Mulungu adzakwaniritsidwa. Tikamaganizira mosamala chifukwa chake dipo linaperekedwa komanso zimene zinalowetsedwapo, timayamba kukhulupirira kwambiri kuti lonjezo la Mulungu loti tidzakhala ndi moyo wosatha m’dziko labwino lidzakwaniritsidwa. N’chifukwa chiyani tikutero? Kodi panafunika chiyani kuti dipo liperekedwe? Yehova anatumiza Mwana wake wokondedwa woyamba kubadwa komanso mnzake wapamtima, kuti adzabadwe monga munthu wangwiro padzikoli. Ali padzikoli, Yesu anapirira mavuto osiyanasiyana. Kenako anazunzidwa komanso kufa imfa yowawa. Apatu Yehova analipira mtengo wokwera kwambiri. Mulungu wathu wachikondi sakanalola kuti Mwana wake avutike n’kufa pongofuna kuti tidzakhale ndi moyo wabwino koma waufupi. (Yoh. 3:16; 1 Pet. 1:18, 19) Chifukwa choti anapereka mtengo wokwera chonchi, Yehova adzaonetsetsa kuti tidzakhale ndi moyo wosatha m’dziko latsopano. w23.04 19:8-9

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025

Lachiwiri, November 4

Iwe Imfa amene umabweretsa ululu woopsa, kodi mphamvu yako ili kuti?​—Hos. 13:14.

Kodi Yehova amafunitsitsa kudzaukitsa akufa? N’zosachita kufunsa. Iye anauzira anthu angapo kuti alembe m’Baibulo lonjezo lake lakuti adzaukitsa akufa. (Yes. 26:19; Chiv. 20:11-13) Yehova akalonjeza, nthawi zonse amakwaniritsa zomwe walonjezazo. (Yos. 23:14) Ndipotu iye ndi wofunitsitsa kudzaukitsa anthu amene anamwalira. Taganizirani zomwe Yobu analankhula. Iye sankakayikira kuti ngakhale atamwalira, Yehova adzalakalaka kumuonanso ali ndi moyo. (Yobu 14:14, 15) Yehova amafunitsitsanso kudzaukitsa atumiki ake onse amene anamwalira, kuti akhale athanzi komanso osangalala. Nanga bwanji za anthu mabiliyoni omwe anamwalira asanapeze mwayi wophunzira za Yehova? Mulungu wathu wachikondi amafunanso kudzawaukitsa. (Mac. 24:15) Iye amafuna kuti iwo akhale ndi mwayi wokhala anzake komanso kuti adzakhale ndi mwayi wokhala padzikoli mpaka kalekale.—Yoh. 3:16. w23.04 16:5-6

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025

Lachitatu, November 5

Mulungu adzatipatsa mphamvu.​—Sal. 108:13.

Kodi mungatani kuti chiyembekezo chanu chikhale champhamvu? Mwachitsanzo, ngati mukuyembekezera moyo wosatha padziko lapansi, muziwerenga ndiponso kuganizira zimene Baibulo limafotokoza zokhudza Paradaiso. (Yes. 25:8; 32:16-18) Muziganizira mmene moyo udzakhalire m’dziko latsopano. Muziyerekezera muli m’dzikolo. Tikamaganizira kwambiri za chiyembekezo chathu cha dziko latsopano, mavuto athu adzaoneka kuti ndi “akanthawi ndiponso aang’ono.” (2 Akor. 4:17) Chiyembekezo chimene Yehova wakupatsani chingakuthandizeni kuti mupirire mayesero. Iye wapereka kale zinthu zomwe zingatithandize kuti tipeze mphamvu. Choncho ngati tikufuna kuti atithandize kuti tichite bwino utumiki wathu, tipirire mayesero kapena tikhalebe osangalala, tiyenera kupemphera kwa Yehova mochokera pansi pamtima ndiponso kufufuza malangizo ake pophunzira Baibulo patokha. Tizilolanso kuti abale ndi alongo atilimbikitse. Nthawi zonse tiziganizira za chiyembekezo chathu. Tikatero tidzalandira ‘mphamvu zazikulu mogwirizana ndi mphamvu zake zochititsa mantha, n’cholinga choti tithe kupirira zinthu zonse moleza mtima ndiponso mwachimwemwe.’—Akol. 1:11. w23.10 43:19-20

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025
Takulandirani.
Laibulaleyi imathandiza anthu kufufuza mabuku ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova a m'zinenero zosiyanasiyana.
Kuti mupange dawunilodi mabuku, pitani pa jw.org.
  • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • tumizirani
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • zachinsinsi
  • JW.ORG
  • Lowani
tumizirani