Lachiwiri, September 9
Mkazi wopusa amakhala wolongolola. Iye ndi woperewera nzeru.—Miy. 9:13.
Amene amamva kuitana kwa “mkazi wopusa” amafunika kusankha, kaya kuvomera kupita kapena kukana. Pali zifukwa zomveka zotichititsa kupewa zachiwerewere. “Mkazi wopusa” akufotokozedwa ngati akunena kuti: “Madzi akuba amatsekemera.” (Miy. 9:17) Kodi “madzi akuba” akutchulidwawa ndi chiyani? Baibulo limayerekezera kugonana pakati pa anthu okwatirana ndi madzi otsitsimula. (Miy. 5:15-18) Mwamuna ndi mkazi okwatirana mwalamulo ndi amene amaloledwa kuti azigonana. Ndiye kodi zimenezi zikusiyana bwanji ndi “madzi akuba.” Madziwa ndi zachiwerewere zomwe n’zosaloleka. Nthawi zambiri zoterezi zimachitika mwachinsinsi, ngati mmene zimakhalira ndi wakuba. “Madzi akuba” angamaoneke ngati otsekemera makamaka ngati anthu ochita zachiwerewerewo akuona kuti sakukumana ndi vuto lililonse chifukwa cha zoipa zomwe akuchitazo. Kumenekutu n’kudzinamiza chifukwa Yehova amaona zonse. Palibe chinthu chowawa kwambiri kuposa kusiya kukondedwa ndi Yehova, ndipo sipakhala chilichonse “chotsekemera” kapena kuti chosangalatsa munthu akataya mwayi wamtengo wapataliwu.—1 Akor. 6:9, 10. w23.06 28:7-9
Lachitatu, September 10
Ngakhale nditachita mokakamizika, ndinebe woyangʼanira mogwirizana ndi udindo umene ndinapatsidwa.—1 Akor. 9:17.
Kodi mungatani ngati mwayamba kuona kuti mapemphero anu si ochokeranso mumtima kapenanso simukusangalala ndi ntchito yolalikira ngati kale? Musamaganize kuti Yehova wasiya kukuthandizani ndi mzimu wake. Monga munthu yemwe si wangwiro, nthawi ndi nthawi mungamasinthe mmene mumamvera. Ngati mwayamba kuona kuti simukuchitanso khama muziganizira chitsanzo cha mtumwi Paulo. Ngakhale kuti ankayesetsa kutsanzira Yesu, ankadziwa kuti si nthawi zonse pomwe angachite zimene akulakalaka. Paulo anali wotsimikiza kukwaniritsa utumiki wake posatengera mmene akumvera. Mofanana ndi zimenezi, inunso musamalole kuti muzisankha zochita potengera mmene mukumvera. Muzitsimikiza kuchita zoyenera ngakhale kuti si zimene mungakonde kuchita. Mukamachita zoyenera nthawi zonse mungayambe kusintha mmene mumamvera.—1 Akor. 9:16. w24.03 10:12-13
Lachinayi, September 11
Asonyezeni kuti mumawakonda.—2 Akor. 8:24.
Tingasonyeze kuti timakonda abale ndi alongo athu powalola kuti akhale anzathu. (2 Akor. 6:11-13) Ambirife tili m’mipingo imene muli abale ndi alongo omwe ndi osiyana pa zinthu zambiri komanso makhalidwe. Kuganizira makhalidwe awo abwino kungatithandize kuti tiziwakonda kwambiri. Tikamaphunzira kuona anthu mmene Yehova amawaonera, timasonyeza kuti timawakonda. Chikondi chidzakhala chofunika kwambiri pa chisautso chachikulu. Kodi n’kuti komwe tidzapeze chitetezo chisautsochi chikadzayamba? Taganizirani malangizo amene Yehova anapereka kwa anthu ake pamene Ababulo ankawaukira. Iye anati: “Inu anthu anga, pitani mukalowe m’zipinda zanu zamkati, ndipo mukatseke zitseko. Mukabisale kwa kanthawi mpaka mkwiyo utadutsa.” (Yes. 26:20) Zikuoneka kuti malangizo amenewa akugwiranso ntchito kwa ife amene tikuyembekezera chisautso chachikulu. w23.07 29:14-16