Lachitatu, September 10
Ngakhale nditachita mokakamizika, ndinebe woyangʼanira mogwirizana ndi udindo umene ndinapatsidwa.—1 Akor. 9:17.
Kodi mungatani ngati mwayamba kuona kuti mapemphero anu si ochokeranso mumtima kapenanso simukusangalala ndi ntchito yolalikira ngati kale? Musamaganize kuti Yehova wasiya kukuthandizani ndi mzimu wake. Monga munthu yemwe si wangwiro, nthawi ndi nthawi mungamasinthe mmene mumamvera. Ngati mwayamba kuona kuti simukuchitanso khama muziganizira chitsanzo cha mtumwi Paulo. Ngakhale kuti ankayesetsa kutsanzira Yesu, ankadziwa kuti si nthawi zonse pomwe angachite zimene akulakalaka. Paulo anali wotsimikiza kukwaniritsa utumiki wake posatengera mmene akumvera. Mofanana ndi zimenezi, inunso musamalole kuti muzisankha zochita potengera mmene mukumvera. Muzitsimikiza kuchita zoyenera ngakhale kuti si zimene mungakonde kuchita. Mukamachita zoyenera nthawi zonse mungayambe kusintha mmene mumamvera.—1 Akor. 9:16. w24.03 10:12-13
Lachinayi, September 11
Asonyezeni kuti mumawakonda.—2 Akor. 8:24.
Tingasonyeze kuti timakonda abale ndi alongo athu powalola kuti akhale anzathu. (2 Akor. 6:11-13) Ambirife tili m’mipingo imene muli abale ndi alongo omwe ndi osiyana pa zinthu zambiri komanso makhalidwe. Kuganizira makhalidwe awo abwino kungatithandize kuti tiziwakonda kwambiri. Tikamaphunzira kuona anthu mmene Yehova amawaonera, timasonyeza kuti timawakonda. Chikondi chidzakhala chofunika kwambiri pa chisautso chachikulu. Kodi n’kuti komwe tidzapeze chitetezo chisautsochi chikadzayamba? Taganizirani malangizo amene Yehova anapereka kwa anthu ake pamene Ababulo ankawaukira. Iye anati: “Inu anthu anga, pitani mukalowe m’zipinda zanu zamkati, ndipo mukatseke zitseko. Mukabisale kwa kanthawi mpaka mkwiyo utadutsa.” (Yes. 26:20) Zikuoneka kuti malangizo amenewa akugwiranso ntchito kwa ife amene tikuyembekezera chisautso chachikulu. w23.07 29:14-16
Lachisanu, September 12
Zochitika zapadzikoli zikusintha.—1 Akor. 7:31.
Muzidziwika ndi mbiri yoti ndinu ololera. Muzidzifunsa kuti: ‘Kodi anthu amaona kuti ndine wololera kapena amandiona kuti ndine wokhwimitsa zinthu, wovuta kapena womva zake zokha? Kodi ndimamvetsera maganizo a ena komanso kuchita zimene akufuna ngati zili zoyenera kutero?’ Zimene timachita pa nkhani ya kulolera zingasonyeze ngati timatsanzira kwambiri Yehova ndi Yesu kapena ayi. Kulolera kumaphatikizapo kukhala okonzeka kusintha zinthu zikasintha pa moyo wathu. Nthawi zina kusintha kungachititse kuti tikumane ndi mavuto osayembekezereka. Mwadzidzidzi, tingakumane ndi mavuto okhudza thanzi lathu. Mwinanso kusintha pa nkhani zachuma kapena zandale kungasokoneze kwambiri moyo wathu. (Mlal. 9:11) Chikhulupiriro chathu chingayesedwenso pamene utumiki wathu wasintha. Komabe tikhoza kuzolowera kusintha komwe kwachitika ngati titachita zinthu 4 zotsatirazi: (1) kuvomereza mmene zinthu zilili, (2) kuganizira zam’tsogolo, (3) kuganizira zabwino zimene zikuchitika komanso (4) kuthandiza ena. w23.07 32:7-8