Lachinayi, September 11
Asonyezeni kuti mumawakonda.—2 Akor. 8:24.
Tingasonyeze kuti timakonda abale ndi alongo athu powalola kuti akhale anzathu. (2 Akor. 6:11-13) Ambirife tili m’mipingo imene muli abale ndi alongo omwe ndi osiyana pa zinthu zambiri komanso makhalidwe. Kuganizira makhalidwe awo abwino kungatithandize kuti tiziwakonda kwambiri. Tikamaphunzira kuona anthu mmene Yehova amawaonera, timasonyeza kuti timawakonda. Chikondi chidzakhala chofunika kwambiri pa chisautso chachikulu. Kodi n’kuti komwe tidzapeze chitetezo chisautsochi chikadzayamba? Taganizirani malangizo amene Yehova anapereka kwa anthu ake pamene Ababulo ankawaukira. Iye anati: “Inu anthu anga, pitani mukalowe m’zipinda zanu zamkati, ndipo mukatseke zitseko. Mukabisale kwa kanthawi mpaka mkwiyo utadutsa.” (Yes. 26:20) Zikuoneka kuti malangizo amenewa akugwiranso ntchito kwa ife amene tikuyembekezera chisautso chachikulu. w23.07 29:14-16
Lachisanu, September 12
Zochitika zapadzikoli zikusintha.—1 Akor. 7:31.
Muzidziwika ndi mbiri yoti ndinu ololera. Muzidzifunsa kuti: ‘Kodi anthu amaona kuti ndine wololera kapena amandiona kuti ndine wokhwimitsa zinthu, wovuta kapena womva zake zokha? Kodi ndimamvetsera maganizo a ena komanso kuchita zimene akufuna ngati zili zoyenera kutero?’ Zimene timachita pa nkhani ya kulolera zingasonyeze ngati timatsanzira kwambiri Yehova ndi Yesu kapena ayi. Kulolera kumaphatikizapo kukhala okonzeka kusintha zinthu zikasintha pa moyo wathu. Nthawi zina kusintha kungachititse kuti tikumane ndi mavuto osayembekezereka. Mwadzidzidzi, tingakumane ndi mavuto okhudza thanzi lathu. Mwinanso kusintha pa nkhani zachuma kapena zandale kungasokoneze kwambiri moyo wathu. (Mlal. 9:11) Chikhulupiriro chathu chingayesedwenso pamene utumiki wathu wasintha. Komabe tikhoza kuzolowera kusintha komwe kwachitika ngati titachita zinthu 4 zotsatirazi: (1) kuvomereza mmene zinthu zilili, (2) kuganizira zam’tsogolo, (3) kuganizira zabwino zimene zikuchitika komanso (4) kuthandiza ena. w23.07 32:7-8
Loweruka, September 13
Ndiwe munthu wokondedwa kwambiri.—Dan. 9:23.
Mneneri Danieli anali wachinyamata pamene Ababulo anamugwira monga kapolo n’kupita naye kudziko lakutali ndi kwawo. Anthuwo ayenera kuti anachita naye chidwi. Iwo anaona “zooneka ndi maso,” monga zakuti Danieli “analibe chilema chilichonse” ndiponso ankachokera m’banja lolemekezeka. (1 Sam. 16:7) Pa zifukwa zimenezi, Ababulo anamuphunzitsa kuti azikatumikira kunyumba yachifumu. (Dan. 1:3, 4, 6) Yehova ankakonda Danieli chifukwa cha zimene mnyamatayu anasankha kuti azichita pa moyo wake. Ndipotu n’kutheka kuti iye anali ndi zaka pafupifupi 20 zokha, pamene Yehova anamutchula pamodzi ndi Nowa komanso Yobu, amuna amene anatumikira Mulungu mokhulupirika kwa zaka zambiri. (Gen. 5:32; 6:9, 10; Yobu 42:16, 17; Ezek. 14:14) Danieli anakhala ndi moyo kwa nthawi yaitali ndipo Yehova anapitiriza kumukonda kwa moyo wake wonse munthu wokhulupirikayu.—Dan. 10:11, 19. w23.08 33:1-2