NYIMBO 38
Mulungu Adzakulimbitsa
zosindikizidwa
	- 1. Panali chifukwa chimene Mulungu - Anakupatsira choonadi. - Anaona mtima wofuna kuchita - Zabwino zomusangalatsadi. - Unalonjeza kum’tumikira; - Ndipo iye anakuthandiza. - (KOLASI) - Ndi magazi a Yesu - Anakuwombola. - Ndiwe wa Mulungu, - adzakulimbitsa. - Adzakutsogolera - ndi mzimu woyera. - Adzakulimbitsa - adzakuteteza. 
- 2. Mulungu anapereka Mwana wake; - Amafunatu zikuyendere. - Ngati Mwana wakeyo sanatimane - Kukulimbitsa sangalephere. - Chikondi chako sangaiwale; - Sangasiye ndithu anthu ake. - (KOLASI) - Ndi magazi a Yesu - Anakuwombola. - Ndiwe wa Mulungu, - adzakulimbitsa. - Adzakutsogolera - ndi mzimu woyera. - Adzakulimbitsa - adzakuteteza. 
(Onaninso Aroma 8:32; 14:8, 9; Aheb. 6:10; 1 Pet. 2:9.)