Genesis
46 Choncho Isiraeli ndi onse a m’nyumba yake ananyamuka kupita ku Beere-seba.+ Kumeneko iye anapereka nsembe kwa Mulungu wa bambo ake Isaki.+ 2 Ndiyeno Mulungu analankhula ndi Isiraeli m’masomphenya usiku,+ kuti: “Yakobo, Yakobo!” Ndipo Yakobo anayankha kuti: “Ine pano!”+ 3 Mulungu anapitiriza kuti: “Ine ndine Mulungu woona,+ Mulungu wa bambo ako.+ Usaope kupita ku Iguputo, chifukwa kumeneko ndidzakukuza kukhala mtundu waukulu.+ 4 Ineyo ndipita nawe ku Iguputo, ndiponso ine ndi amene ndidzabwere nawe kuchokera kumeneko.+ Ndipo Yosefe ndi amene adzakutseke maso pa imfa yako.”+
5 Kenako, Yakobo ananyamuka ku Beere-sebako. Ana a Isiraeliwo anatenga bambo awo, Yakobo, limodzi ndi ana awo aang’ono, ndi akazi awo. Anawatengera m’ngolo zimene Farao anatumiza.+ 6 Anatenganso ziweto zawo zonse ndi katundu wawo yense amene anapeza m’dziko la Kanani.+ Potsirizira pake, Yakobo ndi ana ake onse anafika ku Iguputo. 7 Anafika limodzi ndi ana ake aamuna ndi aakazi, limodzinso ndi adzukulu ake aamuna ndi aakazi obadwa kwa ana ake aamuna, mbadwa zake zonse.+
8 Tsopano nawa mayina a ana a Isiraeli, kapena kuti ana a Yakobo, omwe anabwera nawo ku Iguputo:+ Mwana woyamba wa Yakobo anali Rubeni.+
9 Ndipo ana a Rubeni anali Hanoki, Palu, Hezironi ndi Karami.+
10 Ana a Simiyoni+ anali Yemueli, Yamini, Ohadi, Yakini,+ Zohari ndi Shauli+ mwana wa mkazi wachikanani.
11 Ana a Levi+ anali Gerisoni,+ Kohati+ ndi Merari.+
12 Ana a Yuda+ anali Ere,+ Onani,+ Shela,+ Perezi,+ ndi Zera.+ Komabe, Ere ndi Onani anafera kudziko la Kanani.+
Ana a Perezi anali Hezironi+ ndi Hamuli.+
13 Ana a Isakara+ anali Tola,+ Puva,+ Yabi ndi Simironi.+
14 Ana a Zebuloni+ anali Seredi, Eloni ndi Yahaleeli.+
15 Amenewa ndiwo anali ana a Leya,+ amene anaberekera Yakobo ku Padana-ramu, kuphatikizapo Dina+ mwana wamkazi wa Yakobo. Ana ake onse aamuna ndi aakazi ndi adzukulu ake analipo 33.
16 Ana a Gadi+ anali Zifioni, Hagi, Suni, Eziboni, Eri, Arodi ndi Areli.+
17 Ana a Aseri+ anali Imuna, Isiva, Isivi ndi Beriya.+ Panalinso mlongo wawo Sera.
Ana a Beriya anali Hiberi ndi Malikieli.+
18 Amenewa ndiwo anali ana a Zilipa,+ yemwe Labani anam’pereka kwa mwana wake wamkazi Leya. Ndiwo ana amene Zilipa anaberekera Yakobo m’kupita kwa nthawi. Onse pamodzi analipo 16.
19 Ana a Rakele,+ mkazi wa Yakobo, anali Yosefe+ ndi Benjamini.+
20 Yosefe anabereka Manase+ ndi Efuraimu*+ ku Iguputo. Anabereka anawa kwa mkazi wake Asenati+ mwana wa Potifera, yemwe anali wansembe wa mzinda wa Oni.
21 Ana a Benjamini anali Bela,+ Bekeri,+ Asibeli, Gera,+ Namani,+ Ehi, Rosi, Mupimu,+ Hupimu+ ndi Aridi.
22 Amenewa ndiwo ana amene Rakele anaberekera Yakobo. Onse pamodzi analipo 14.
23 Ana a Dani+ anali Husimu.*+
24 Ana a Nafitali+ anali Yahazeeli, Guni,+ Yezera ndi Silemu.+
25 Amenewa ndiwo anali ana a Biliha,+ yemwe Labani anam’pereka kwa mwana wake wamkazi Rakele. Awa ndiwo ana amene Biliha anaberekera Yakobo m’kupita kwa nthawi. Onse pamodzi analipo 7.
26 Ana onse a Yakobo otuluka m’chiuno mwake,+ amene anali nawo ku Iguputo, analipo 66 onse pamodzi, osawerengera akazi a ana ake. 27 Ana amene Yosefe anabereka ku Iguputo analipo awiri. Onse a m’nyumba ya Yakobo amene anali nawo ku Iguputo analipo 70.+
28 Yakobo anatumiza Yuda+ kuti atsogole kupita kwa Yosefe kukam’dziwitsa za kubwera kwa bambo ake ku Goseni. Pambuyo pake iwo anafika ku Goseni.+ 29 Pamenepo Yosefe anakonza galeta lake n’kunyamuka kupita kukakumana ndi Isiraeli bambo ake ku Goseni.+ Atangofika kwa bambo akewo, nthawi yomweyo anawakumbatira n’kulira ndi kugwetsa misozi. Anachita zimenezi mobwerezabwereza.+ 30 Pamapeto pake Isiraeli anauza Yosefe kuti: “Ndingathe kufa+ tsopano chifukwa ndaona nkhope yako, popeza ukadali ndi moyo.”
31 Ndiyeno Yosefe anauza abale ake ndi a m’nyumba ya bambo ake kuti: “Ndipite kwa Farao ndikam’dziwitse.+ Ndikanene kuti, ‘Abale anga ndi a m’nyumba ya bambo anga, amene anali m’dziko la Kanani, abwera kuno kwa ine.+ 32 Anthuwa ndi abusa,+ pakuti amaweta ziweto.+ Abwera ndi nkhosa zawo, ng’ombe, ndi zinthu zawo zonse.’+ 33 Farao akakuitanani n’kukufunsani kuti, ‘Kodi mumagwira ntchito yanji?’ 34 Inu mukayankhe kuti: ‘Akapolo anufe takhala tikuweta ziweto kuyambira tili ana kufikira lero, ifeyo ndi makolo athu omwe.’+ Mukayankhe choncho kuti mukhale ku Goseni,+ chifukwa aliyense woweta nkhosa Aiguputo amanyansidwa naye.”+