Masalimo
Masalimo*
BUKU LOYAMBA
(Masalimo 1 – 41)
1 Wodala+ ndi munthu amene sayenda motsatira malangizo a anthu oipa,+
Saima m’njira ya anthu ochimwa,+
Ndipo sakhala pansi pamodzi ndi anthu onyoza.+
2 Koma amakondwera ndi chilamulo cha Yehova,+
Ndipo amawerenga ndi kusinkhasinkha chilamulo chake usana ndi usiku.+