Masalimo
2 N’chifukwa chiyani anthu a mitundu ina akuchita chipolowe,+
Ndiponso n’chifukwa chiyani mitundu ya anthu ikung’ung’udza za chinthu chopanda pake?+
2 Mafumu a dziko lapansi aima pamalo awo,+
Ndipo nduna zapamwamba zasonkhana pamodzi mogwirizana.+
Atero kuti alimbane ndi Yehova+ komanso wodzozedwa wake.+
3 Iwo akunena kuti: “Tiyeni tidule zomangira zawo,+
Ndipo titaye zingwe zawo kutali ndi ife!”+
5 Pa nthawiyo, adzawalankhula mu mkwiyo wake,+
Adzawasokoneza ataipidwa kwambiri.+
7 Ndinene za lamulo la Yehova.
Iye wandiuza kuti: “Iwe ndiwe mwana wanga,+
Lero, ine ndakhala bambo ako.+
8 Tandipempha,+ ndipo ndikupatsa mitundu ya anthu kukhala cholowa chako,+
Ndikupatsa dziko lonse lapansi kukhala lako.+
9 Mitunduyo udzaiswa ndi ndodo yachifumu yachitsulo,+
Udzaiphwanya ngati mbiya yadothi, n’kukhala zidutswazidutswa.”+