Masalimo
Salimo la Davide.
110 Yehova wauza Ambuye wanga kuti:+
“Khala kudzanja langa lamanja+
Kufikira nditaika adani ako monga chopondapo mapazi ako.”+
2 Yehova adzatambasula ndodo+ yako yachifumu yamphamvu kuchokera m’Ziyoni+ ndi kunena kuti:
“Pita ukagonjetse anthu pakati pa adani ako.”+
3 Anthu ako+ adzadzipereka mofunitsitsa+ pa tsiku limene udzatsogolera asilikali ako kunkhondo.+
Wadzikongoletsa ndi ulemerero,+
Ndipo gulu la achinyamata amene ali ngati mame a m’bandakucha lili pamodzi ndi iwe.+
4 Yehova walumbira+ (ndipo sadzasintha maganizo). Iye wati:+
“Iwe ndiwe wansembe mpaka kalekale,+
Monga mwa unsembe wa Melekizedeki!”+