Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 14:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Ndipo Melekizedeki,+ mfumu ya ku Salemu,+ anabweretsa mkate ndi vinyo.+ Iyeyu anali wansembe wa Mulungu Wam’mwambamwamba.+

  • Zekariya 6:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Munthu ameneyu adzamanga kachisi wa Yehova ndipo adzalandira ulemerero.+ Iye azidzalamulira atakhala pampando wake wachifumu ndipo adzakhalanso wansembe ali pampando womwewo.+ Maudindo awiri onsewo adzakhala ogwirizana.+

  • Aheberi 5:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Monga mmene akuneneranso penapake kuti: “Iwe ndiwe wansembe mpaka muyaya monga mwa unsembe wa Melekizedeki.”+

  • Aheberi 6:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 kumene Yesu, yemwe ndi kalambulabwalo anakalowa chifukwa cha ife.+ Iyeyu wakhala mkulu wa ansembe mpaka muyaya monga mwa unsembe wa Melekizedeki.+

  • Aheberi 7:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Popeza kuti analibe bambo, analibe mayi, analibe mzere wa mibadwo ya makolo ndipo tsiku limene anabadwa+ komanso limene anamwalira silikudziwika, koma anamuchititsa kuti afanane ndi Mwana wa Mulungu,+ iye ndi wansembe kwamuyaya.+

  • Aheberi 7:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Ndiyeno, ngati zikanakhala zothekadi kuti munthu akhale wangwiro+ kudzera mu unsembe wa Alevi,+ kodi pakanafunikanso kuti pakhale wansembe wina+ monga mwa unsembe wa Melekizedeki+ osati monga mwa unsembe wa Aroni? (Unsembe wa Alevi unali mbali ya Chilamulo pamene chinaperekedwa kwa anthu.)+

  • Aheberi 7:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Pakuti Malemba amachitira umboni kuti: “Iwe ndiwe wansembe mpaka muyaya monga mwa unsembe wa Melekizedeki.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena