Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 16:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Kenako mame aja anauma ndipo panthaka ya m’chipululumo panapezeka tinthu topyapyala ndi tolimba+ koma tosalala ngati mame+ amene aundana panthaka.

  • Ekisodo 16:35
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 35 Ndipo ana a Isiraeli anadya mana kwa zaka 40+ mpaka pamene analowa m’dziko lokhalidwa ndi anthu.+ Mana ndiwo anali chakudya chawo mpaka pamene anafika m’malire a dziko la Kanani.+

  • Numeri 11:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Manawo+ anali ngati mapira,*+ ndipo maonekedwe ake anali ngati utomoni woonekera mkati ngati galasi.+

  • Deuteronomo 8:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Anakuphunzitsani kudzichepetsa pokukhalitsani ndi njala+ ndi kukudyetsani mana,+ amene inu kapena makolo anu sanawadziwe. Anachita zimenezi kuti mudziwe kuti munthu sakhala ndi moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mawu onse ochokera m’kamwa mwa Yehova.+

  • Nehemiya 9:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Munawapatsanso mkate wochokera kumwamba kuti athetse njala yawo.+ Munatulutsa madzi pathanthwe ndi kuwapatsa kuti athetse ludzu lawo,+ ndiyeno munawauza kuti alowe+ ndi kutenga dziko limene munalumbira mutakweza dzanja lanu kuti mudzawapatsa.+

  • Yohane 6:31
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 31 Makolo athu anadya mana+ m’chipululu, monga mmene Malemba amanenera kuti, ‘Anawapatsa chakudya chochokera kumwamba kuti adye.’”+

  • 1 Akorinto 10:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Ndiponso, onse anadya chakudya chimodzimodzi chauzimu,+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena