Masalimo
Nyimbo ndi Salimo la pa tsiku la sabata.
92 Ndi bwino kuyamika inu Yehova,+
Ndi kuimba nyimbo zotamanda dzina lanu, inu Wam’mwambamwamba.+
2 Ndi bwino kunena za kukoma mtima kwanu kosatha m’mawa,+
Ndi za kukhulupirika kwanu usiku,+
3 Ndipo ndidzatero pogwiritsa ntchito choimbira cha zingwe 10 ndi choimbira cha zingwe zitatu.+
Ndidzaimba nyimbo yomveka bwino ndi zeze.+
4 Pakuti mwandichititsa kusangalala, inu Yehova, chifukwa cha zochita zanu.
Ndimafuula mosangalala chifukwa cha ntchito ya manja anu.+
7 Anthu oipa akamaphuka ngati msipu,+
Ndipo anthu onse ochita zopweteka anzawo akamaphuka ngati maluwa,
Amatero kuti awonongeke kwamuyaya.+
8 Koma inu Yehova, ndinu wokwezeka mpaka kalekale.+
9 Pakuti taonani adani anu, inu Yehova!+
Adani anu onse adzatha!+
Anthu onse ochita zopweteka anzawo adzamwazikana.+
10 Koma inu mudzakweza nyanga* yanga ngati nyanga ya ng’ombe yam’tchire yamphongo.*+
Ndidzadzola mafuta abwino.+
11 Diso langa lidzayang’ana adani anga atagonja,+
Makutu anga adzamva za anthu ondiukira, anthu ochita zoipa.