Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Salimo 40:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  5 Inu Yehova Mulungu wanga, mwatichitira zinthu zambiri zodabwitsa,+

      Ndipo mumatiganizira.+

      Palibe angafanane ndi inu.+

      Ndikafuna kulankhula ndi kunena za zodabwitsazo,

      Zimachuluka kwambiri moti sindingathe kuzifotokoza.+

  • Salimo 66:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  3 Muuzeni Mulungu kuti: “Ntchito zanu ndi zochititsadi mantha!+

      Chifukwa cha kuchuluka kwa mphamvu zanu, adani anu adzabwera kwa inu mogonjera.+

  • Salimo 104:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 Ntchito zanu ndi zochuluka, inu Yehova!+

      Zonsezo munazipanga mwanzeru zanu.+

      Dziko lapansi ladzaza ndi zinthu zimene munapanga.+

  • Salimo 145:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  4 Anthu adzatamanda ntchito zanu ku mibadwomibadwo,+

      Ndipo adzasimba za zochita zanu zamphamvu.+

  • Salimo 150:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  2 Mutamandeni chifukwa cha ntchito zake zamphamvu.+

      Mutamandeni mogwirizana ndi ukulu wake wosaneneka.+

  • Mlaliki 3:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Chilichonse iye anachipanga chokongola ndiponso pa nthawi yake.+ Komanso anapatsa anthu mtima wofuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale+ kuti ntchito imene Mulungu woona wagwira, iwo asaidziwe kuyambira pa chiyambi mpaka pa mapeto.+

  • Chivumbulutso 15:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Iwo akuimba nyimbo ya Mose+ kapolo wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwanawankhosa,+ yakuti:

      “Ntchito zanu n’zazikulu ndi zodabwitsa,+ inu Yehova Mulungu Wamphamvuyonse.+ Njira zanu ndi zolungama ndi zoona,+ inu Mfumu yamuyaya.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena