94 Inu Yehova, Mulungu wobwezera anthu oipa,+
Inu Mulungu wobwezera anthu oipa, walani!+
2 Nyamukani inu Woweruza dziko lapansi.+
Perekani chilango kwa anthu odzikweza.+
3 Kodi anthu oipa adzakondwera kufikira liti?+
Kodi adzakondwera kufikira liti, inu Yehova?+
4 Iwo amalankhula zopanda pake, ndipo amalankhula mosasamala.+
Onse ochita zopweteka anzawo amadzitukumula.+
5 Iwo amaphwanya anthu anu, inu Yehova,+
Ndipo amasautsa cholowa chanu.+
6 Amapha mkazi wamasiye ndi mlendo wokhala m’dziko lawo,+
Ndipo amaphanso ana amasiye.+
7 Iwo amanena kuti: “Ya sakuona,+
Ndipo Mulungu wa Yakobo sakudziwa zimene zikuchitika.”+
8 Zindikirani anthu opanda nzeru inu.+
Ndipo opusa inu, mudzakhala liti ozindikira?+
9 Kodi amene anakupatsani makutu, sangamve?+
Kapena amene anapanga maso, sangaone?+
10 Kodi amene amalangiza mitundu ya anthu,+
Amene amaphunzitsa anthu kuti akhale ozindikira, sangathe kudzudzula?+
11 Yehova amadziwa kuti maganizo a anthu ali ngati mpweya wotuluka m’mphuno.+
12 Wodala ndi munthu wamphamvu amene inu Ya mumamudzudzula,+
Komanso amene inu mumamuphunzitsa chilamulo chanu,+
13 Kuti mum’patse mtendere pa nthawi ya masoka,+
Kufikira dzenje la munthu woipa litakumbidwa.+
14 Yehova sadzataya anthu ake,+
Kapena kusiya cholowa chake.+
15 Pakuti zigamulo zidzayambiranso kukhala zachilungamo,+
Ndipo onse owongoka mtima adzazitsatira.
16 Ndani adzanyamuka kuti amenye nkhondo ndi anthu ochita zoipa m’malo mwa ine?+
Ndani adzaima m’malo mwa ine kulimbana ndi anthu ochita zopweteka anzawo?+
17 Yehova akanapanda kundithandiza,+
Ndikanatsikira kuli chete mofulumira.+
18 Pamene ndinanena kuti: “Phazi langa literereka,”+
Kukoma mtima kwanu kosatha, inu Yehova, kunandichirikiza.+
19 Malingaliro osautsa atandichulukira mumtima mwanga,+
Mawu anu otonthoza anayamba kusangalatsa moyo wanga.+
20 Kodi inu mudzagwirizana ndi olamulira ankhanza,+
Pamene akuyambitsa mavuto mwa kupanga malamulo?+
21 Iwo amaukira koopsa munthu wolungama,+
Ndipo munthu wosalakwa amamuweruza kuti ndi woipa. Amachita zimenezi kuti akhetse magazi ake.+
22 Koma Yehova adzakhala malo anga okwezeka ndiponso achitetezo,+
Ndipo Mulungu wanga adzakhala thanthwe langa lothawirako.+
23 Iye adzawabwezera zoipa zawo,+
Ndipo adzawakhalitsa chete mwa kuwadzetsera masoka okonza okha.+
Yehova Mulungu wathu adzawakhalitsa chete.+