1 Timoteyo
1 Ine Paulo, mtumwi+ wa Khristu Yesu molamulidwa ndi Mulungu+ Mpulumutsi wathu,+ ndi Khristu Yesu yemwe ali chiyembekezo chathu,+ 2 ndikulembera iwe Timoteyo,+ mwana wanga weniweni+ m’chikhulupiriro:
Kukoma mtima kwakukulu, chifundo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate ndi Khristu Yesu Ambuye wathu, zikhale nawe.+
3 Paja nditatsala pang’ono kupita ku Makedoniya, ndinakulimbikitsa kuti ukhalebe ku Efeso.+ Ndikukulimbikitsanso kuti ukhalebe komweko, uletse+ anthu ena ake kuti asaphunzitse chiphunzitso chosiyana ndi chathu,+ 4 ndiponso kuti asamamvere nkhani zonama+ ndi kukumbana mibadwo ya makolo. Zimenezi n’zosapindulitsa,+ koma zimangoyambitsa mafunso ndipo siziphunzitsa anthu chilichonse chochokera kwa Mulungu chokhudza chikhulupiriro. 5 Ndithu, cholinga chokulamulira zimenezi n’chakuti tikhale ndi chikondi+ chochokera mumtima woyera,+ m’chikumbumtima chabwino,+ ndiponso m’chikhulupiriro chopanda chinyengo.+ 6 Anthu ena akana kutsatira zimenezi ndipo asocheretsedwa+ n’kuyamba kutsatira nkhani zopanda pake.+ 7 Amenewa amafuna kukhala aphunzitsi+ a chilamulo+ koma sazindikira zimene akunena kapena mfundo zimene akuzilimbikira.
8 Tikudziwa kuti Chilamulo n’chabwino+ ngati munthu akuchigwiritsa ntchito moyenera.+ 9 Zili choncho podziwa mfundo iyi yakuti, lamulo siliikidwa chifukwa cha munthu wolungama. Limaikidwa chifukwa cha anthu osamvera malamulo,+ osalamulirika,+ osaopa Mulungu, ochimwa, osakoma mtima,*+ onyoza zinthu zopatulika, opha abambo ndi amayi awo, opha anthu, 10 adama,+ amuna ogonana ndi amuna anzawo, oba anthu, onama, olumbira monama,+ ndiponso ochita china chilichonse chosagwirizana+ ndi chiphunzitso cholondola.+ 11 Chiphunzitso chimenechi n’chogwirizana ndi uthenga wabwino waulemerero umene anauika m’manja mwanga,+ wochokera kwa Mulungu wachimwemwe.+
12 Ndikuyamika Khristu Yesu Ambuye wathu amene anandipatsa mphamvu poona kuti ndine wokhulupirika,+ ndipo anandipatsa utumiki.+ 13 Anatero ngakhale kuti kale ndinali wonyoza Mulungu, wozunza anthu ake+ ndiponso wachipongwe.+ Komabe anandichitira chifundo+ chifukwa ndinali wosadziwa+ ndi wopanda chikhulupiriro. 14 Koma ndinalandira kukoma mtima kwakukulu+ kwa Ambuye wathu. Ndinalandiranso chikhulupiriro ndi chikondi chodzera mwa Khristu Yesu.+ 15 Mawu akuti Khristu Yesu anabwera m’dziko kudzapulumutsa ochimwa,+ ndi mawu oona ndi oyenera kuwavomereza ndi mtima wonse.+ Mwa ochimwa amenewa, ine ndiye wochimwa kwambiri.+ 16 Komabe, anandichitira chifundo+ kuti Khristu Yesu asonyeze kuleza mtima kwake konse kudzera mwa ine wochimwa kwambiri, kuti chikhale chitsanzo kwa amene adzamukhulupirire+ n’cholinga chakuti adzapeze moyo wosatha.+
17 Kwa Mfumu yamuyaya,+ imene siifa,+ yosaoneka,+ yekhayo amene ali Mulungu,+ kwa iyeyo kupite ulemu ndi ulemerero mpaka muyaya.+ Ame.
18 Mwana wanga Timoteyo, ndikukulamulira+ kuchita izi malinga ndi maulosi+ amene ananeneratu za iwe, kuti mogwirizana ndi maulosiwo upitirize kumenya nkhondo yabwino.+ 19 Ukhale ndi chikhulupiriro ndi chikumbumtima chabwino+ chimene ena achikankhira kumbali,+ moti chikhulupiriro chawo chasweka ngati ngalawa.+ 20 Ena mwa amenewa ndi Hemenayo+ ndi Alekizanda,+ ndipo ndawapereka kwa Satana+ kuti akalangidwa,* aphunzire kuti sayenera kulankhula zonyoza Mulungu.+