Chivumbulutso
12 Kenako chizindikiro chachikulu+ chinaoneka kumwamba. Ndicho mkazi+ atavala dzuwa, ndipo mwezi unali kunsi kwa mapazi ake. Kumutu kwake kunali chisoti chachifumu chokhala ndi nyenyezi 12, 2 ndipo mkaziyo anali ndi pakati. Iye analira pomva ululu+ chifukwa cha zowawa za pobereka.
3 Chizindikiro chinanso chinaoneka kumwamba, ndipo ndinaona chinjoka chachikulu+ chofiira, chokhala ndi mitu 7 ndi nyanga 10, ndipo pamitupo panali zisoti zachifumu 7. 4 Mchira+ wake unakokolola gawo limodzi mwa magawo atatu a nyenyezi+ zakumwamba n’kuzigwetsera kudziko lapansi.+ Ndipo chinjokacho chinangoimabe pamaso pa mkazi uja,+ amene anali pafupi kubereka,+ kuti akabereka chidye+ mwana wakeyo.
5 Mkaziyo anabereka mwana wamwamuna,+ mnyamata amene adzakusa mitundu yonse ndi ndodo yachitsulo.+ Ndipo mwana wakeyo anatengedwa msangamsanga n’kupititsidwa kwa Mulungu ndi kumpando wake wachifumu.+ 6 Koma mkaziyo anathawira kuchipululu,+ kumene Mulungu anamukonzera malo, kuti akadyetsedwe+ masiku 1,260.+
7 Ndipo kumwamba kunabuka nkhondo: Mikayeli+ ndi angelo ake anamenyana ndi chinjoka. Chinjokacho ndi angelo ake chinamenya nkhondo, 8 koma sichinapambane, ndipo malo awo sanapezekenso kumwamba. 9 Choncho chinjokacho+ chinaponyedwa pansi, njoka yakale ija,+ iye wotchedwa Mdyerekezi+ ndi Satana,+ amene akusocheretsa dziko lonse lapansi+ kumene kuli anthu. Iye anaponyedwa kudziko lapansi,+ ndipo angelo akenso anaponyedwa naye limodzi. 10 Ndipo ndinamva mawu ofuula kumwamba, akuti:
“Tsopano chipulumutso,+ mphamvu,+ ufumu wa Mulungu wathu,+ ndi ulamuliro wa Khristu+ wake zafika, chifukwa woneneza abale athu waponyedwa pansi. Iyeyo anali kuwaneneza usana ndi usiku pamaso pa Mulungu wathu.+ 11 Iwo anamugonjetsa+ chifukwa cha magazi a Mwanawankhosa,+ ndiponso chifukwa cha mawu a umboni wawo.+ Ndipo iwo sanaone kuti miyoyo yawo ndi yofunika,+ ngakhale pamene anali pa ngozi yoti akhoza kufa. 12 Pa chifukwa chimenechi, kondwerani kumwamba inu ndi inu okhala kumeneko!+ Tsoka+ dziko lapansi ndi nyanja,+ chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu, ndipo ali ndi mkwiyo waukulu podziwa kuti wangotsala ndi kanthawi kochepa.”+
13 Tsopano chinjoka chitaona kuti achigwetsera kudziko lapansi,+ chinazunza mkazi+ amene anabereka mwana wamwamuna uja. 14 Koma mkaziyo anapatsidwa mapiko awiri+ a chiwombankhanga chachikulu kuti aulukire kuchipululu,+ kumalo ake aja. Kumeneko n’kumene akudyetsedwa+ kwa nthawi imodzi, nthawi ziwiri, ndi hafu ya nthawi,+ kutali ndi njoka ija.+
15 Kenako njokayo inalavula madzi+ ngati mtsinje kuchokera m’kamwa mwake, kulavulira mkazi uja, kuti amizidwe ndi mtsinjewo.+ 16 Koma dziko lapansi linathandiza mkaziyo.+ Dzikolo linatsegula pakamwa pake ndi kumeza mtsinje umene chinjoka chija chinalavula kuchokera m’kamwa mwake. 17 Ndipo chinjokacho chinakwiya ndi mkazi uja,+ moti chinapita kukachita nkhondo ndi otsala a mbewu yake, amene amasunga malamulo a Mulungu, amenenso ali ndi ntchito yochitira umboni+ za Yesu.