2 Mbiri
27 Yotamu+ anakhala mfumu ali ndi zaka 25 ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 16. Mayi ake dzina lawo linali Yerusa mwana wa Zadoki.+ 2 Yotamu ankachita zoyenera pamaso pa Yehova ngati mmene anachitira Uziya bambo ake,+ kungoti sanachite makani nʼkukalowa mʼkachisi wa Yehova.+ Koma anthu ankachitabe zoipa. 3 Iye anamanga geti lakumtunda la nyumba ya Yehova+ ndipo pakhoma la mpanda wa Ofeli anamangapo zinthu zambiri.+ 4 Komanso anamanga mizinda+ mʼdera lamapiri la Yuda+ ndipo mʼdera lankhalango anamangamo nsanja+ ndiponso malo okhala ndi mipanda yolimba kwambiri.+ 5 Yotamu anamenyana ndi mfumu ya Aamoni+ ndipo patapita nthawi anawagonjetsa. Choncho chaka chimenecho Aamoni anamʼpatsa matalente* a siliva 100, tirigu wokwana miyezo 10,000 ya kori* komanso balere wokwana miyezo 10,000 ya kori. Aamoni anamupatsanso zinthu zimenezi mʼchaka chachiwiri ndi chachitatu.+ 6 Choncho Yotamu anapitiriza kukhala wamphamvu popeza anatsimikiza kuyenda mʼnjira za Yehova Mulungu wake.
7 Nkhani zina zokhudza Yotamu, zimene anachita komanso nkhondo zonse zomwe anamenya, zinalembedwa mʼBuku la Mafumu a Isiraeli ndi Yuda.+ 8 Iye anakhala mfumu ali ndi zaka 25 ndipo analamulira zaka 16 ku Yerusalemu.+ 9 Kenako Yotamu mofanana ndi makolo ake, anamwalira ndipo anaikidwa mʼmanda mu Mzinda wa Davide.+ Ndiyeno mwana wake Ahazi anakhala mfumu mʼmalo mwake.+