Salimo
Nyimbo Yokwerera Kumzinda.
125 Anthu amene amakhulupirira Yehova+
Ali ngati phiri la Ziyoni, limene silingagwedezeke
Koma lidzakhalapo mpaka kalekale.+
2 Mofanana ndi mapiri amene azungulira Yerusalemu,+
Yehova wazungulira anthu ake,+
Kuyambira panopa mpaka kalekale.
5 Koma anthu amene apatuka panjira yabwino nʼkuyamba kuyenda mʼnjira zokhotakhota,
Yehova adzawachotsa limodzi ndi anthu ochita zoipa.+
Mu Isiraeli mukhale mtendere.