Genesis 37:28 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 28 Tsopano amuna amalonda achimidiyani+ aja anali kudutsa mumsewu. Pamenepo abale a Yosefe anamutulutsa m’chitsimemo+ n’kumugulitsa kwa Aisimaeliwo. Anamugulitsa ndalama zasiliva 20,+ ndipo iwo anapita naye ku Iguputo. Genesis 42:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 Kenako iwo anayamba kulankhulana kuti: “Ndithudi, izi zikuchitika chifukwa cha zimene tinachitira m’bale wathu uja.+ Pajatu tinaona kusautsika kwake pamene anatichonderera kuti timumvere chisoni, koma ife sitinalabadire. N’chifukwa chake tsokali latigwera.”+ Miyambo 28:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Munthu wolemedwa ndi mlandu wokhetsa magazi a munthu adzakhala wothawathawa mpaka kumanda.+ Anthu asamugwire n’cholinga choti amuletse. Machitidwe 2:37 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 37 Tsopano iwo atamva mawu amenewa, anavutika kwambiri mumtima,+ ndipo anafunsa Petulo ndi atumwi enawo kuti: “Amuna inu, abale athu, tichite chiyani pamenepa?”+
28 Tsopano amuna amalonda achimidiyani+ aja anali kudutsa mumsewu. Pamenepo abale a Yosefe anamutulutsa m’chitsimemo+ n’kumugulitsa kwa Aisimaeliwo. Anamugulitsa ndalama zasiliva 20,+ ndipo iwo anapita naye ku Iguputo.
21 Kenako iwo anayamba kulankhulana kuti: “Ndithudi, izi zikuchitika chifukwa cha zimene tinachitira m’bale wathu uja.+ Pajatu tinaona kusautsika kwake pamene anatichonderera kuti timumvere chisoni, koma ife sitinalabadire. N’chifukwa chake tsokali latigwera.”+
17 Munthu wolemedwa ndi mlandu wokhetsa magazi a munthu adzakhala wothawathawa mpaka kumanda.+ Anthu asamugwire n’cholinga choti amuletse.
37 Tsopano iwo atamva mawu amenewa, anavutika kwambiri mumtima,+ ndipo anafunsa Petulo ndi atumwi enawo kuti: “Amuna inu, abale athu, tichite chiyani pamenepa?”+