3 Mngelo wina anafika ndi kuimirira kuguwa+ lansembe. Iye anali ndi chiwiya chofukiziramo chagolide, ndipo anamupatsa zofukiza zambiri+ kuti azipereke nsembe limodzi ndi mapemphero a oyera onse paguwa lansembe lagolide, limene linali pamaso pa mpando wachifumu.